Liwu loti “Bridal” (bride to be) likuimira mkazi yemwe ali ndi ukwati wake posachedwa. “Shower” ndi kupereka mwambo ndi mphatso komanso madalitso ndi malangizo ndi kumukondwelera pamene azikakhala m’banja ndi mwamuna wake.
 
Malingana ndi matanthauzo awa a “bridal shower”,  zikusemphana kwambiri ndi chiphunzitso cha Chisilamu, chifukwa kupereka mphatso kapena kusangalalira mtsikana ndi kumufunira mafuno abwino pa kukwatiwa kwake ziyenera kuti zidzikhala mu gulu la chikondwelero cha nikaah (walimah).  Izi zikutanthauza kuti ziyenera zizikhala kumapeto kwa nikaah osati nikaah isanachitike.
Kuchita mwambo oterewu ndi kulakwa kwakukulu mu Chipembedzo cha Chisilamu, chifukwa ndi zopeka zomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanachite pa mwambo wa nikaah. Tisaiwale kuti nikaah ndi mapemphero (ibaadah), ndipo palibe ibaada yomwe imachitika mChislamu kupatula yochokera mu Qur’an kapena mu Sunnah. Bridal Shower sikupezeka mu Qur’an kapena mu Sunnah, mundondomeko ya ukwati.
Poonjezera apo, nthawi zina nikaah imatha kulephereka osachitika bridal shower itachitika kale, malingana ndi kusemphana maganizo kwa anthu okwatirana komwe kumatha kuchitika nikaah isanachitike, ndikusakwatirana zonse nkukanika. Zikakanika chonchi, ndiye kuti zonse zomwe apanga pa bridal shower zimakhala zaonongeka –  kuyambira nthawi komanso chuma – ndiponso mtsikanayo amakhala kuti wasokonezedwa nzeru zake.  (Allah samakonda anthu oononga). Choncho ndibwino kupewa zinthu zomwe mu Chipembezo mulibe komanso zomwe zimachitika nthawi yosayenera.
Ndikofunikira kumusangalalira mtsikana ndi mnyamata amene wakwatira kapena wakwatiwa ndi kumufunira zabwino ponena mawu oti Baarakallah fiikumaa wa baaraka ‘alykuma wa jama’ bainakumaa bil-khair.
Apa mungapereke malangizo osiyanasiyana komanso mutha kupereka mphatso pagulu la azimayi okhaokha, atapanga nikaah, uku mukumusangalalira ngati gawo la walimah ndipo zidzalowa mu walimah osati bridal shower ya bid’ahyo.
 
Tikumbutsane kuti Nikaah simalonda opezerapo ndalama ayi, koma ndigawo la mapemphero potsatira chiphunzitso cha Chisilamu.
Tinene momveka bwino kuti ndi zolakwika kuyenda azimayi kupita kulikonse ulendo oyenda usiku ndi usana ngakhale ulendowo uli ofunika bwanji, kupatula kuthawa nkhondo poteteza moyo wake (mkaziyo). Choncho kupita ku walima kaya ku hajj ku maulendo a mwambo wa Chisilamu kapena ku mapemphero aliwonse, ndi zosavomerezedwa mkazi kuyenda popanda mahram wake, ngati kupita ndi kubwera ku ulendowo kukupitilira gawo lamasana. Ndipo ngati ndi zoletsedwa kutero pa mwambo wa Chisilamu kapena ku mapemphero aliwonse, ndiye kuti mzimayi atalikire kwatunthu kuyenda popanda mahram pa myambo ya chikunja ndi yosakhala mapemphero a Chisilamu yomwe ngati bridal party kapena bridal shower.
 
Pomaliza tikumbutsane kuti mzimayi sangakhale mahram kwa mzimayi mzake ngakhale ali chigulu, azimayiwo sakuloledwa kuyenda okha chifukwa chosowa mahram wawo. Mahram ndi m’bale wachimuna wamkazi (mlongo wake, bambo wake etc) kapena mwamuna wake.