Mtumiki salla Allah alaih wasallam anayankhula zokhunza Black Seed (Njere Zakuda حبة سوداء) kuti ndi mankhwala a nthenda iliyonse kupatula imfa.

Posachedwapa ma dokotala atulukira kuti ndizoonazdi Black Seed amachiza matenda osiyanasiyana, monga mtima ndi ena ambiri omwe iwowo anali asanawatulukire machiritso ake.

Zimenezitu zimatheka malinga ndi chifuniro cha Allah Ta’la yemwe amaika machiritso munjira yomwe wafuna, ndipo ife timawapeza machiritsowo tikagwiritsa ntchito zinthu moyenera.

Tiyeni tione matenda angapo awa:

Kupanikizika kwa Mtima
ضيق صمام القلب

Black Seed okwana spoon yaing’ono ndi uchi okwana ma spoon awiri.

Musakanize zimenezi mu kapu ya tea kapena mmadzi otentha ndikumamwa kummawa musanadye kalikonse, komanso usiku pogona. Pitirizani zimenezo mpaka 2 weeks kapena kuposerapo.

Ndizabwino pakumwa kumanena kuti:

بسم الله الرحمن الرحيم – بسم الله الذى لا يضر مع اسمة شىء فى الأرض ولا فى السماء وهو السميع العليم

Bismillahi Lladhi laa yadhurru ma’ismihi shay’un fil ardhwi walaa fi ssamaai wa Huwa Ssamee’ul ‘Aleem

Kapena

بسم الله – اللهم رب الناس، أذهب البأس، وأشف أنت الشافى لا شفاء إلا شفاؤك شفاء لا يغادر سقما

Bismillah, Allahummah Rabba Nnaas, adh’hibil ba’sa, anta Al Shaafi laa shifaa illa shifaauka shifaan laa yughaadiru saqman.

Kapena ma dua ena ofanana ndi amenewa, koma modzipereka ndi imaan yonse.

Likango – Hemorrhoids
بواسير

Black Seed osapera (ndibwino mupere nokha); musakanize bwinobwino ndi uchi wa original mpaka zisanduke ngati cream.

Mutenga cream ameneyo mu spoon yaikulu ndikupaka (like greasing) pokhalirapo (anus) then mudikire 30 minutes… kenako muona kuti zikusintha ndithu (kumbali ya ululu) mwachifuniro changed Allah. Pangani zimenezi mopitiriza mpaka two weeks kapena kiposera pamenepo mpaka muone kuti zikusintha.

Mauka – Candida
المبي

1. Black Seed wopera nkusakaniza ndi Uchi mmadzi.

Mudzimwa spoon imodzi kummawa kulikonse musanadye kalikonse.

2. Fresh Orange juice + Black Seed wopera.

Mudzimwa 30 minutes musanadye chakudya (mamawa mmimba mulibe kanthu), komanso musanagone.

3. Mukhonza kusakaniza Black Seed wopera mu salad kapena mu chakudya chilichonse chomwe zingatheke kusakaniza.

Ulcers
قرحة

Madontho 10 a Black Seed Oil (at least ma Spoon awiri), uchi, spoon imodzi ya khungu la pomegranate (ena amati chimanga chachizungu kaya) wouma, ndikusakaniza bwinobwino.

Mudzimwa tsiku lirilonse mmimba mopanda kanthu (kummawa), kenako mumwe kapu ya mkaka wotentha wopanda sugar ngAkHale pang’ono.
Mupange zimenezi kwa myezi iwiri …. kuchira kungachitike mkati mwa nyengo imeneyo mwachifiniro cha Allah

Allah ndiye Mwini Kuchiza