KUBWEZA (QADHAA) MASIKU OSIYIDWA PAKUSALA MWEZI WA RAMADHAN

Qadhaa ya Swawm ndi chani?

Qadhaa ya swawm ndiko kusala kwa munthu yemwe sanasale masiku ena a mwezi wa Ramadhan, kapena kumusalira m’bale wake pambuyo poti munthu wamwalira atasiya swawm yomwe analonjeza kwa Allah kuti asala (Nadhr) modzikakamiza yekha, kapenanso kumupelekera dipo yemwe anamwalira.

Kodi Oyenera Kupanga Qadhaa Ndindani?

Yemwe anamasula chifukwa cha Haidh (monthly period), Nifaas (postpartum period kapena kuti pambuyo pa kubereka), odwala matenda ochizika, komanso yemwe anali paulendo ndipo anamasula chifukwa cha mavuto a paulendowo.

AMAI OMWE SAMABWEZA MASIKU OMWE ANAMASULA MWEZI WA RAMADHAN CHIFUKWA CHA PERIOD

Funso: Ineyo kuyambira chaka chomwe ndinayamba kusala mwezi wa Ramadhan, sindimabweza masiku omwe ndamasula kamba ka period, ndipo izi zapangitsa kuti ndisamathe kukumbukira masiku onse omwe ndinasiya osasala. Ndilangizeni ndipange bwanji, poti panopa ndazindikira kuti sindimapanga chilungamo kwa Allah.

Yankho: Ndizodandaulitsa kwambiri kumva kuti zimenezi zikuchitika pakati pa amai athu komanso alongo athu okhulupilira.

Kusabweza masiku okakamizidwa kusala omwe mwasiya moiwala ngakhale mwadala, zikuthanthauza kuti simunakwaniritse cholinga cha kusala kwanu, komwe ndi kumuopa Allah (Taqwa). Kumbukirani Allah akunena kuti

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آَمَنُوا كُتِبَ عَلَيْكُمُ الصِّيَامُ كَمَا كُتِبَ عَلَى الَّذِينَ مِنْ قَبْلِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ

“Ee inu amene mwakhulupilira, kwalamulidwa kwainu kusala monga mmene kunalamulidwira kwa anthu akale pambuyo panu, kuti mukhale owopa Allah (Taqwa)” Surah Al Baqarah 183

Ngati Taqwa yako sikukuthandiza kupewa kulekelera komanso kukhala tcheru pantchito yomwe ukuchita, ndiye kuti kusala kwako kulibe phindu.

Choncho inuyo mukuyenera kupanga tawbah (mubwelere ndi kulapa kwa Allah) pazomwe mwakhala mukuchita, ndikupempha chikhululuko.

Kenako mufufuze chiwelengero cha masiku omwe munasiyawo mmene mungathere ndikuwabweza. Mukatero basi inuyo mwapulumuka. Koma mukasankhabe kulekelera kuti simubweza, basi ndiye kuti mwalolera chilango cha Allah pa inu.

Timpemphe Allah kuti akufewetsereni mukwanitse.

KUSALA KWA MAI YEMWE ALI MU HAIDH (PERIOD) KAPENA NIFAAS (WANGOBEREKA KUMENE)

Yemwe ali mu period kapena wangobwereka kumene, sakuyenera kusala, komanso sakuyenera kuswali panthawi ziwiri zimenezi. Ndipo ngakhale atasala kapena kuswali, sizilandiridwa kwa iye komanso kukhala kuchimwa. Koma amasule ndipo akadzayera adzabweze masiku omwe wamasulawo, kupatula swalaat yokha, sanalamulidwe kubweza. Izi zikuchokera mu kuyankhula kwa Aaisha radhia Allahu anha:

كنا نؤمر بقضاء الصوم ولا نؤمر بقضاء الصلاة

“Tinali kulamulidwa kubweza swawm koma sitinali kulamulidwa kubweza swalaat”

Ndipo ma Ulamaa anagwirizana, kuchokera muzomwe Aaisha anayankhula, kuti akuyenera kubweza swawm yokha osati swalaat, kwayemwe wasiya chifukwa cha Haidh ndi Nifaas.

Ichi n’chifundo cha Allah Subhanah wa Ta’ala kwa amai komanso kuwafewetsera mu Deen; chifukwa choti swalaat imabwerezedwa tsiku ndi tsiku kasanu, choncho kubweza kwake kumakhala kovuta chifukwa cha kuchuluka. Pomwe swawm yokakamiziwa imachitika kamodzi pachaka, mwezi wa Ramadhan masiku ochepa, kubweza kwake kumakhala kosavuta.

Mai yemwe wachedwetsa kubweza masiku mpaka kufika mwezi wa Ramadhan chaka china

Yemwe wachedwetsa kubweza masiku mpaka Ramadhan wina popanda vuto lovomerezeka ndi Shari’ah, akuyenera kupanga tawbah kwa Allah ndi kubweza komanso kudyetsa osauka patsiku lirilonse lomwe akubwezalo. Koma ngati odwala matenda apitilira mpaka Mwezi wina, akuyenera kungobweza pambuyo pakuchira, popanda kudyetsa osauka. Majmu’ Fatawa Ibn Baaz 15/181

Yemwe magazi akutuluka mopitilira, koma si magazi a Haidh (period) kapena Nifaas (pambuyo pa kubereka)

Magazi omwe sali a Haidh komanso sali a Nifaas, amatchedwa Istihaadhwa. Ndipo kwa amene ali mu Istihaadhwa akuyenera kupitiriza kuswali kapena kusala, komanso kukhala malo amodzi ndi mwamuna wake, ndipo azipanga wudhu pa swalaat zonse.

Mwachidule, zochitika za yemwe ali mu Istihaadhwa ndichimodzimodzi yemwe watuluka mkodzo kapena mpweya ndi zina zonse zomwe zimaononga wudhu. Koma akuyenera kutchinga ndi thonje kapena kansalu kuti magaziwo asafalikire pathupi ndi zovala zake, malinga ndimmene zikulongosoledwa mma Hadith a Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Majmu’ Fatawa Ibn Baaz 15/181

Mai yemwe akusala pamene ali mu Haidh chifukwa cha manyazi ndi abale ake

Palibe kuchitira mwina, kumeneko ndikulakwitsa. Sakuyenera kuchita manyazi chifukwa Haidh ndi chilengedwe chomwe Allah anamulengera mwana wa Adam.

Mai wa Haidh waletsedwa kusala ndi kuswali, choncho ngati wasala mmasiku amenewo, sikuwerengedwa kwaiye kuti wasala komanso akuyenera kudzabweza tsiku limenelo ndipo asadzabwereze mchitidwe woterowo. Majmu’ Fatawa Ibn Baaz 15/181

Mai yemwe akudziwonetsera ngati wasala pamene ali mu Haidh kapena Nifaas

Pali amai ena amatha kudziwonetsera ngati akusala pamene sakuyenera kusala, chifukwa chosafuna kuwonekera kuti sakusala. Kutero sizolakwika ngati zili zosadziwika kuti ali mu Haidh, koma asakhale ndi chitsimikizo cha kusala. Ngati sanadziwike kuti ali mu Haidh ndipo sanawauze anthu zamomwe aliri, palibe vuto. Koma sakuloledwa kuikira chitsimikizo cha kusala poti chitsimikizocho komanso kusalako zikhala zosalandiridwa. Palibenso vuto kukhala ndi anthu omwe asala koma osadya, mmalo mwake kukadyera kumbali nthawi ina.

MAI YEMWE AKUYEMBEKEZERA, KAPENA AKUYAMWITSA

Amai omwe akuyembekezera kapena akuyamwitsa, ali mgulu lomwe Allah anawaloleza kumasula ndikudzabweza masiku omwe amasulawo vutolo likadzachoka. Chimenechi ndi chilolezo, kutanthauza kuti kusala ndi chikakamizo koma ngati waona kuti mmene aliri sakwanitsa kusala, ndiololedwa kumasula. Koma ngati akuona kuti kusalako sikupereka vuto lirilonse, akhonza kusala. Ndipo powonetsa kulikonda lamulo la kusalali, mai woyembekezera ndiwololedwa kuyamba tsiku ndi kusala, ndipo adziyang’anire masanawu mpaka pamene dzuwa likulowa; ngati angaone kuti sakwanitsa akhonza kumasula, koma ngati angaone kuti zikutheka, apitiriza. Zonzezi ndi zitsanzo za momwe angasankhire zochita mopanda kupepusa lamulo la Kusala komanso mopanda kudzipatsa mavuto chifukwa cha kudzikakamiza.

Mai yemwe Swawm Yamupeza ali Woyembekezera ndipo Zoletsa Kusala Zikupitilira Mwaiye Mpaka ma Ramadhan Angapo Asakusala

Funso: Mai wina wangobereka kumene ndipo sanasale mwezi wa Ramadhan. Pambuyo pa kuchoka vuto lija sanabweze Ramadhan uja mpaka kudutsa nyengo yaitali kwambiri yomwe sakukwanitsa kusala, kodi pamenepo angatani?

Yankho: Choyambilira, mai ameneyu akuyenera kupanga tawbah pazomwe anachitazo, chifukwa sizololedwa kuti munthu asiye kusala popanda chifukwa chovomerezeka, choncho akuyenera kupanga tawbah. Kenako, ngati angakwanitse kusala ngakhale modumphitsa, ayenera kusala.

“Ndibwino kwambiri pobweza masiku a Ramadhan osadumphitsa mpaka utamaliza masiku onse chifukwa ukubweza momwe unali kuchitira mwezi wa Ramadhan”

Kupepusa Chilolezo Choti Akhonza Kumasula

Ambiri mwa amai athu oyembekezera komanso oyamwitsa amakhala akuipepusa swaumu pochita zinthu moyerekedwa komanso mowagwetsa ulesi ena omwe akusala, moti zimafika poti ena amatha kumalakalaka akanakhala ndi pakati kapena kuyamwitsa.
Izi zimachitika munjira zingapo, zina mwaizo monga:

Kudya moonekera kwa ana

Ndizosaloledwa kuti mai yemwe akuloledwa kudya masana azidya ana akuona. Ena amachita kuwatuma ana omwe akusala kuti awaphikire chakudya, ndipo amakhala poyereyera nkumadya ana akuona. Izi zimapereka kufooka mmitima mwa anawo ndipo kuwayandikitsa chakudya pafupi kumamvetsa kuwawa swawm yawo. Choncho amai ngati muli mu condition imeneyi yetsetsani kumadyera chakudyacho malo obisika, ana asamachite kudziwa kuti mai wachikulire sakusala.

Kudya mowonekera pagulu la anthu ena

Pamene mai woyembekezera kapena woyamwitsa yemwe sakusala ali pagulu la anthu ena, monga munsika, paulendo kapena pamsonkhano winawake, ndipo nthawi yoti adye yakwana, sibwino kutenga chakudya nkumadyera pagulu la anthu omwe asala. Izi eniake amaona ngati zilibe vuto, koma zimapereka chithunzithunzi choipa kwa anthu, choti mzimaiyu sakudzilemekeza, sakulemekeza mwezi wa Ramadhan, akuchitenga chilolezo chomwe Allah wamuloleza mwachibwana, komanso alibe taqwa yomwe Asilamu anzake ali nayo mmwezi umenewu.
Zindikirani kuti Taqwa yomwe Allah waitchula kuti ndichifukwa chomwe anatilamulira kusala, imayenera kupezeka mwa wina aliyense ngakhale yemwe sakusala pachifukwa chovomerezeka.

Choncho amai musamaganize kuti pamene mukudya masana ndiye kuti malamulo ena komanso myambo ina ya mwezi wa Ramadhan simukuyenera kuitsatira.

Kuganiza molakwika ponena kuti poti matendawa ndi ochokera kwa Allah, swawmuyinso njochokera kwa Allah.

Munthu ngati wamasula ndi chifukwa chovomerezeka pamaso pa Allah, ndiye kuti wakhonzekeranso kuti udzabweza masiku omwe wamasulawo.

Choncho izi sizikukuloleza kuyankhula motumbwa anthu ena akamakulangiza za zibwana zomwe ukuchita pamene ukudya masana. Amai ambiri adab imawatalikira panthawi imene akudya masana, makamaka akamalangizidwa ndi anthu ena pazochitika zawo zosalongosoka.

Mai wina, Allah amuwongole ndikumukhululukira, anandiyankha chonchi pambuyo pomuwunikira kuti asamaganize kuti masiku omwe wamasulawo apita basi, koma aziwerengetsa nkusunga chiwelengerocho kuti adzabweze. Anayankha kuti: “Sindidzakwanitsa kubweza masiku amenewa chifukwa choti Allah ndamene analamula kusala, Yemweyonso ndamene wabweretsa period mwaife kukhala system yokhanzikika, choncho ngati Iye anadziwa kuti ine ndidzadutsa munyengo ya Ramadhan, bwanji sanaimike kaye periodiyo kuti ndisale kaye ngati kusalako kuli kofunikira kwambiri kwayemwe ali mu period?”

Kuyankhula uku kumawononga zabwino zomwe Allah amawapatsa amai omwe asiya kusala chifukwa cha period, ndipo munthuyo amapeza machimo chifukwa akumupatsa malamulo Allah kusiya kutsatira malamulo omwe anamupatsa. Komanso kuyankhula kotereku kumaonetsa kuti maiyu samatsatira malamulo a Deen yake, choncho ndikupempha amai kuti muzikhala mukutsatira malamulo a Chipembedzo chanu paumoyo wanu watsiku ndi tsiku, kuwopera kuti mungadzimane zabwino zomwe Allah wakuikira munyengo zanu komanso kuti mangakane madalitso a Allah chifukwa cha kunyozera kwanu.

Maganizo onena kuti ngati mai wasiya masiku ndiye kuti adzagawana ndi mwamuna wake, adzamuthandiza kubweza

Maganizo awa anakhanzikika mwa amai ambiri ngakhalenso abambo ena. Iwo amaganiza kuti swawm ili ngati ndime, ndipo ngati mkazi wawo wasiya masiku 10, ndiye kuti adzagawana pakati, wina 5 winanso 5.

Mai dziwani kuti ngati mungatero ndiye kuti mwasala masiku 5 okha ndipo mwatsala ndi ndongole ya masiku 5 omwe wasala mwamuna wanuyo. Komanso bambowo adziwe kuti asala masiku 35, komwe kuli kulakwitsa kwakukulu.

Ngati munasala ndi masiku 10 mmwezi wa Ramadhan, sungani ndipo mudzabweze nokha vuto lomwe muli nalolo likadzatha.

Kuchokera mwezi wa Shawwaal muli ndi myezi 11, yomwe ndi masiku 300 kapena kuposera pamenepo kuti mudzafikenso mwezi wa Ramadhan, zoona inu simungathe kusala masiku 11 mmasiku 300? Umenewonso ndiulesi, kupatula ngati zingakuvuteni kubweza kamba ka mavuto ena opitilira, komabe sakuyenera kukuthandizani winawake.

Mu Hadith Al Qudsiy, Allah Ta’la ananena kuti swawm ndiyake Allah amadziwa malipiro ake kwa aliyense, choncho aliyense akuyenera kusala payekha chifukwa simukudziwa kuti kodi yemwe akukundithandizayu akusala zenizeni, kapena akukuonongerani? Ibaada ya kusala sitimathandizana.