Salaf ndi liwu lomwe limatanthauza zinthu zomwe zidapita, za mbuyomu.
Ndipo liwuli likamagwiritsidwa ntchito mchipembedzo cha Chisilamu limatanthauza  mibadwo ya anthu akale omwe anayambilira kugwiritsa ntchito Shariah. Tsopano mibadwo imeneyi kuyambira pa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ma Swahaba ake ndi mibadwo iwiri yomwe inadza pambuyo pa ma swahaba, imatchedwa Salaf Swaalih (anthu olungama omwe adapita).
سلف صالح
Amenewa ndi omwe anali kuchita zinthu mu deen molingana ndi Sharia, ndipo Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawatchula kuti:
خير أمتي قرني ثم الذين يلونهم ثم الذين يلونهم…
“anthu abwino mu Ummah wanga ndi a mum’badwo uno, kenako omwe adzabwere pambuyo, komanso omwe adzabwere pambuyopo”
Mwachidule, imeneyi ndi njira imene Msilamu wina aliyense amayenera kuyendera komanso kuifalitsa chifukwa palibe yemwe ali Msilamu koma samatsatira Mtumiki ndi ma Sahabiy ake.
Munthu aliyense amene amatsatira zomwe anali kuchita anthu a mmibadwo imeneyo, amatsatira anthu akale omwe anapita (ma Salaf), choncho amatchedwa Salafiyyu – osati Salaf – chifukwa ma Salaf ndamene anapitawo, salaf sangapezeke panthawi yatsopano ndipo sitingamuone. Koma timaona Salafiyyu (Otsatira Salaf).
Anthu ambiri a magulu ena owonongeka mChislamu, amabisana ku gulu limeneli la Salafi pochita za uchigawenga ndi kuphwanya malamulo a Chisilamu komanso aqeeda yeniyeni anaikwilira. Nchifukwa chake pakali pano kuti muonesetse mupeza kuti anthu amadana kwambiri ndi Salafiy, gulu la anthu omwe amatsatira Qur’an,  Mtumiki ndi ma Sahabiy ake, ndipo amalitcha kuti ndi zigawenga  pofuna kuthana ndi Chisilamu. Amalipekera iti ndi ito cholinga choti anthu asiye kutsatira chifukwa amadziwa kuti ndi mmene Chisilamu chikuyendera, Ndiye anthu akasiya kutsatira Salafi Basi pamenepo Chisilamu achitha.
Kodi Salafiyyu ndi limodzi mwa magulu a mChisilamu?
Ayi ndithu. Ma Salafiyyu sangakhale mu gulp lina lake chifukwa iwo paokha ndi gulu limodzi lokha loima palokha, anthu ake amatsatira gulu limodzi lomwe liribe kugawanika, gulu lomwe ndi la Mtumiki ndi ma Swahaba ake komanso ma Taabieen. Gulu lochita zimodzi, losasemphana chikhulupiliro (aqeeda) ndipo mkati mwawo mulibe maina osiyanasiyana. Salaf Swaalih ndi description ya gulu la Mtumiki ndi ma Swahaba ake (Salaf Swaalih = anthu abwino omwe adatsogola).
Izi zikuchokeranso mmau a Mtumiki pamene anali kulongosola za kugawanika kwa Ummah wake kumene kudzachitike kutsogolo, ndipo anati magulu onsewo ngakumoto kupatula limodzi, ma Swahaba atafunsa kuti gulu lake liti, anayankha kuti:
الجماعة
Gulu (limodzi lomwe silidzagawanika mtimagulu)
Ndipo mu report lina, anati
ما أنا عليه وأصحابي
Lomwe ndili ine ndi ma Swahaba anga
Ndikhulupilira kuti tadziwano tanthauzo la Salafi (Salafiyyu).
CHENJEZO
Simugamudziwe mSalafiyyu weniweni pongolankhula kuti ndine Salafiyyu. Sali mSalafiyyu aliyense yemwe akudzitchula kuti ndine Salafi.
Msalafiyyu weniweni mungamudziwe kuzera mu zochitika zake. Chifukwa Salafiyy si dzina la munthu koma mbiri ya munthu.  Chimodzimodzi yemwe sali Salafiyyu mungamudziwe kuzera muzochitika zake.
Komanso mukuyankhula kwina, anthu amene amatsatira Qur’an ndi Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam amatchedwa Ahlu Sunnah wal Jamaah
 
Allah ndiye Mwini kudziwa konse
Madh’ab