Tisaiwale kukumbukira kuti Kusangalala tsiku la Nikkah, sikuti Ndi chikakamizo ayi, koma kuti ndi Sunnah, chifukwa Anthu amazikakamiza ndikupanikizika Poona kuti afune asafune akuyenera kuchititsa Chisangalalo cha Nikkah yawo,dziwani kuti Kumangitsa Nikkah ndi chinthu China kusangalalaso Ndi chinthu China,Sikuti kupanda kusangalala ndiye kuti Nikkah yo Siyidatheke ayi,chifukwa Mu malamulo a Nikkah mulibemo Kusangalala komwe Tikukukamba apaku.
Ndipo kusangalalako ndi utendere waukulu wa Allah, kuwasangalalira awiri okwatirana ndi khomo limodzi kuchokera mu makomo achisangalalo ndi chimwemwe,chifukwa kukwatirako ndi njira kuchokera mu njira yakuzibisa Ndi kuzisunga ku zinthu zonyasa {chiwerewere}, kuyambira kale anthu amaonetsera ndipo adzakhalabe akuonetsera chisangalalo Chawo cha utendere wabanjawu mpaka kale ,ndipo adazipangira Njira zosiyanasiyana zosangalalira motengera ndi kugwirizana ndi Maiko awo kapena madera awo ndi Zikhalidwe zawo.
Ndipo Njira yoyamba yosangalalira Tsiku la Nikkah ndiko kukonza Chakudya, Ndipo Mtumiki wathu adatilimbikitsa zakutero
عن أنسٍ قال: ((ما أولَمَ النبيُّ صلَّى اللهُ عليه وسلَّم على شيءٍ مِن نسائِه ما أولَمَ على زينبَ، أولمَ بشاةٍ )) .
Hadith ikuchokera kwa Anas Ibn Malik Allah asangalale naye adati: Mtumiki sadachititseko phwando pa chilichonse kuchokera mwa azikazi ake kuposera momwe adachititsira phwando pa ukwati wake ndi mkazi wake Zainab Allah asangalale naye, adachititsa phwando ndi mbuzi imodzi.
Kuli maumboni ambiri olimbikitsa kuphika chakudya ndikuyitana Anthu monga achibale,ndi oyandikana nawo,ndi Anthu ochita nawo chinzake {Friends},kutero ndi Njira inaso yolengezetsera ukwatii chifukwa Sharia idalimbikitsa zakulengezetsa ukwati ndikutiso usamachitike mobisa,akuyankhula Mtumiki
عن عائشة رضي الله عنها قالت قال النبى صلى الله عليه وسلم: أعلنوا هذا النِّكاحَ واجعلوهُ في المساجِدِ واضربوا عليهِ بالدُّفوفِ
أخرجه الترمذي، والبيهقي.
Hadith ikuchokera kwa Mayi Aisha Allah asangalale nawo adati:adayankhula Mtumiki Muhammad madalitso ndi mtendere zikhale paiye kuti:lengezetsani zaukwatiyu {ukamachitika} ndipo mukapangire ku mzikiti ndipo mukaumenyere ma Duffu.
Mu Hadith imeneyi tikupeza zinthu ziwiri:
Zolakwika za Chisangalalo cha Nikkah:
________________________
عن عائشةَ رضي الله عنها ((أنَّ أبا بكرٍ رَضِيَ الله عنه دخل عليها وعِندَها جاريتانِ في أيَّامِ مِنًى تُدَفِّفانِ وتَضرِبانِ، والنبيُّ صلَّى اللهُ عليه وسلَّم متغَشٍّ بثوبِه، فانتَهَرهما أبو بكرٍ، فكشف النبيُّ صلَّى اللهُ عليه وسلَّم عن وَجهِه، فقال: دَعْهما يا أبا بكرٍ؛ فإنَّها أيامُ عيدٍ، وتلك الأيَّامُ أيَّامُ مِنًى)). رواه البخاريُّ.
Hadith ikuchokera kwa Mayi Aisha Allah asangalale nawo,ndithu Abubakr Allah asangalale naye adalowa mnyumba mwa Aisha Allah asangalale naye,ndipo panthawiyo ndikuti Mayi Aisha adali ndi Atsikana awiri akuyimba ndikumamenya ma Duffu masiku a mina, ndipo Mtumiki adali atazibisa ndi chovala chake {kuti asamaone Atsikanawo} Abubakr adawakalipira atsikana awiri aja, kenako Mtumiki adazivundukula Nkhope Yake nayankhula kwa Abubakr kuti: Asiye Atsikanawo eeeh! iwe Abubakr chifukwa ndithu amenewa ndi Masiku achisangalalo, ndipo masiku amenewa ndi Masiku a mina (masiku a Mina ndi masiku atatu pambuyo pa tsiku la Eidul-Adhuha mu Dhul Hijja, ndipo amatchedwaso ndi dzina lakuti Ayyamu Tashriq,choncho palibe vuto kusangalala mu masiku amenewo).
Mu Hadith imeneyi Muli kuloleza kuimba kwa Azimayi ndi kuvina, masiku azisangalalo Monga Eid ndi Tsiku laukwati, komatu Tikuyenera Kumvetsa apa kuti Zida zomwe amaimbira ndi Ma Duff,ambiri tikuwadziwa ma Duffu, Kwa amene sakuwadziwa afufuze ena mwa ma Nasheed aku Tanzania oyimbidwa ndi Anyamata amagwiritsira ntchito ma Duff, Koma Timvetse bwino kuti kuvina komwe kudaloledwa apa ndi kuvina kwa akazi okhaokha, komaso kuvinako kuzichitika mosakweza mawu mwakuti sangathe kumva azimuna achikunja, komaso Mawu oyankhulidwa mu nyimbo wo akhale opanda uthenga oipa kapena olimbikitsa zoipa.
Tsopano Tiyeni tione Masiku ano ndi kufalikira kwa Zikhalidwe zonyasa zochokera kwa Azungu ndi kutengeka kwa azikazi achisilamu ndi Asilamu ena mwaunyinji, Tipeza kuti Kuvina kwa Akazi komwe Kumachitika Masiku ano Sikungafanane ndi momwe Akazi akale amachitira, mu nthawi imene kudali umunthu mwa azimayi ndi Mavalidwe abwino.
Ndiye ndi zachidziwikire kuti masiku ano Kuvina komwe kumachitika mu ma Nikkah, kumakhala kosakanikana Amuna ndi Akazi, chachiwiri Akazi amavala Zoonetsa matupi ndi Zothina komaso zo Dinda, mwakuti akamavina aliyense amakhala wayika thupi lake pa Scale, chachitatu mupeza mkazi mkazi wachisilamu pa Nikkah akuvina mopeleka mayesero,kugwedeza Thupi lake paliponse, izi zimachitika chifukwa chakutengera kwawo mavinidwe achikunja ama Kafir, Choncho Chifukwa cha Zotsatira za Mchitidwe umenewu potengera ndi zoipa zomwe Zimatsatizirapo,ndi Haram Akazi kuvina mu Zisangalalo za Nikkah pa zifukwa zomwe Tafotokozazo, Ndipo tanena kale kuti Sharia imatseka Njira iliyonse yofikitsa ku Zinthu za Haram (سد الذريعة) ngakhale zitakhala kuti Chinthucho pachiyambi chake ndi chololedwa.
Your Comments