1. Chiphunzitso cha chi Shia chimanena kuti “Aah” ndilimodzi mwa maina a Allah.

Umboni: Ma’anil Akhbaar, chitabu cholembedwa ndi Al Qummi, page 304:

Onani chithunzi

2. Ma Shia amakhulupilira kuti Abu Talib (Malume a Mtumiki), Abdullah ndi Aaminah (Makolo a Mtumiki) anali Asilamu ndipo anamwalira ndi Imaan.

Maumboni: Al I’tiqaadaat, chitabu cholembedwa ndi Al Qummi (Asswadooq), page 110. Al Mukhtasar fi ‘Aqaaid Shi’ah, cholembedwa ndi Haidar Al Wakeel, page 23. Awaailul Maqaalaat, cholembedwa ndi Sheikhul Mufeed, page 45-46:

3. Mu Adhana ya ma Shia amaikamo mawu oti “Ash’hadu anna Aliyya Waliyyu’Allah”. Koma zitabu zawo zikutsutsa kuti Adhaan yeniyeni ilibe mawu amenewa.

Umboni: Man laa Yahdhuruhul Faqeeh, chitabu cholembedwa ndi Al Qummi, page 202 kapena 188:

4. Akuti Ali radhia Allahu anhu amakwiya ngati wina walemekezedwa kuposa iye.

Umboni: Al Anwaaru Nnu’maaniyya, chitabu cholembedwa ndi Sayyed Ni’matullahi Al Jazaairi, vol. 2 page 168:

5. Akuti Jibril anabwera pa dunia kudzamutenga Ali radhia Allahu anhu kupita kumwamba kuti akayanjanitse pakati pa Angelo omwe anali kukangana:

Umboni: Ma’ajiz Aali Bayt, chitabu cholembedwa ndi Sayyed Haashim Al Jarraani, vol. 1 page 44:

6. Ali radhia Allahu anhu anamusintha munthu kukhala galu:

Umboni: Ma’ajiz Aali Bayt, chitabu cholembedwa ndi Sayyed Haashim Al Jarraani, vol. 1 page 273:

7. Akuti Allah analenga Angelo kuchokera mu Noor ya Ali radhia Allahu anhu, ndipo Angelo 70,000 amawapemphera chikhululuko ma Shia.

Umboni: Bihaarul Anwaar, chitabu cholembedwa ndi Baaqir Al Majilisi, vol. 7:

8. Ma Shia akuti yemwe anayang’ana nyenyezi nkunena kuti “ine ndikudwala”, malinga ndi nkhani ya Ibrahim (as) mu Surah Swaaffaat Aayah 88, si Ibrahim koma Mtumiki Muhammad salla Allahu alaih wasallam, ndipo akuti nyenyeziyo siinali nyenyezi yeniyeni koma anali Al Husain radhia Allahu anhu:

Umboni: Usool Al Kaafi, chitabu cholembedwa ndi Al Kulayni, vol. 1 page 295:

9. Ma Shia amaphunzitsana kuti anthu onse ndiana a mahule, kupatula iwo ma Shia:

Umboni: Furoo’l Kaafi, chitabu cholembedwa ndi Al Kulayni, page 239:

10. Ma Shi’a alibe Qur’an, ndipo Qur’an yomwe ilipoyi mulibemo malamulo awo omwe amayendera. Izi anayankhula student wachi Shia waku Malawi yemwe anali akuphunzira ku Iran. Ndipo ine sindinafune kudelera mawu ake koma ndinafufuza mpaka ndinapezadi maumboni ochuluka pazomwe anayankhulazi. Anati:

“Ife padakali pano tilibe Qur’an. Maverse omwe mukuwerangawonso tilibe. Ili kaye kuphanga.”

Ndipo kenako ndinawerenga izi:

Umboni: Kuchokeram u Mashaariq Shumoos Dduriyyah, fi Ahaqqiyyati Madh’habil Akhbaariyya, chitabu cholembedwa ndi Abdul Jabbaar Al Musawi Al Bahraani, page 127

 Gawo Lachiwiri >>