Kutamandidwa konse ndi kwa Allaah, Wapamwambamwamba, Yemwe alibe wothandizana naye mu Ufumu Wake, Yemwe ali m’Modzi, Yemwe ali Wakutha kuchita chili chonse ndipo kwa Iye ndi komwe kuli Chiongoko. Mtendere ndi madalitso zipite kwa Mtumiki Muhammad (ﷺ), aku banja ake ndi omutsatira ake ndipo Allaah awateteze onsewa ku zoipa zonse zomwe ena amakhala ali nkuwachitira. Pambuyo pake, Allaah awapatsenso madalitso asilamu amene adabwera pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki (ﷺ) omwe ali ma Taabi’iin. Ndipo madalitso apitenso kwa asilamu omwe adachiteteza chipembedzo cha Allaah pambuyo pa kumwalira kwa ma Taabi’iin.
Uthengawu ukupezeka mu Buku ili (Al-Bayyinah – Umboni woonekera poyera) lidalembedwa pa zifukwa zingapo ndipo zina mwa izo ndi izi:
- Kuyesetsa kwawo kwa ma Shī’ah pofalitsa chikhulupiriro chawo ku Malawi,
- Kuopsa kwa gulu logalukirali pa chisilamu ku mbali ya maganizidwe awo,
- Kusazindikira kwa asilamu ambiri pa Aqiidah kapena kuti chikhulupiriro chawo cha ma Shī’ah,
- Kusalondora kwa Aqiidah ya ma Shī’ah, yomwe ikudzadza ndi bodza, Shirk, kunyoza kwa Qur’aan, komanso kunyoza kwa omutsatira a Mtumiki (ﷺ),
- Chikhulupiriro chawo pa ma Imaam awo,
- Zoyenera kudziwa kuti tipewe chiwembu chawo.
Ndaika uthenga umenewu mwatsatanetsatane ndi cholinga choti aliyense yemwe sawadziwa ma Shī’ah, awadziwe ndipo atsutse chikhulupiriro chawo. Uthenga onse mu buku limeneli watengedwa mu ma buku osiyanasiyana omwe akulongosola za chikhulupiriro chawo (ma Shī’ah) ndipo tawaika (mabukuwo) mkati mwa mfundo zomwe zayankhulidwa. Ndipo gawo lalikulu likhala lochokera mu ma buku awo omwe chifukwa iwowa sangakhulupirire zonena za Sunnah (akuyenera kupatsidwa umboni kuchokera mu zolemba zawo zomwe). Mu buku ili muli zonse zofunikira kuti munthu achidziwe chi Shī’ah. Ndipo ndi thandizo kwa yemwe akufuna kudziwa komanso ali ndi mtima wofuna kuphunzira. Allaah akuyankhula motere mu Buku lake lopatulika
إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَذِكْرَىٰ لِمَن كَانَ لَهُۥ قَلْبٌ أَوْ أَلْقَى ٱلسَّمْعَ وَهُوَ شَهِيدٌ
“Ndithudi, m’menemu muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima kapena yemwe akumvetsera uku ali ndi chidwi.”
Ndikupempha kwa Allaah kuti awupange uthengawu kukhala umodzi mwa zida zotetezera Chisilamu kuno ku Malawi. Aamiin.
Pangani download PDF
Gawo Loyamba >>
Your Comments