Idris Al Maghribi anali Msilamu waku Morocco ndipo atakumana ndi da’wah ya ma Shia, anaganiza zosiya Chisilamu nkulowa Shia.

Pa mwambo wa “kusinguka” (kutuluka mu chipembedzo china kuliwa mu chipembedzi china), pamene Yaasir Al Habib yemwe ndi mmodzi mwa akuluakulu oyendetsa Shia ku London, akulowetsa Msilamu chi Shia.

Choncho, monga tichitira Asilamu pomulandira munthu ku Chisilamu, timamuyankhulitsa shahaada ya Tawheed komanso ya Utumiki, poti anali ku Shirk, chimodzimodzi ma Shia, munthu akamalowa Shia amamupangitsa shahada yawo monga mmene tikuoneramo. Kutanthauza kuti kwa Iwo Msilamu ndi mushrik ndipo akuyenera kupanganso shahaada Shia akatuluka Chipembedzo cha Chisilamu nkulowa chipembedzo cha Shia.

Shahaada ya ma Shia yomwe anamuyankhulitsa munthu yemwe akulowa chipembedzo cha Shia

Brother yankhulani ndi madalitso a Allah Tabarak wa Ta’ala:

Ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu wopembedzedwa mwachoonadi koma Allah, Mmodzi yekha, alibe wothandizana naye ndipo alibe wofanana naye.

Ndikuikira umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Allah swalla Allah alaih wa aalih. Ndikuikiranso umboni kuti iye ndi bwana wa aneneri komanso wotsiriza wawo ndipo ndiwabwino pa zolengedwa zonse.

Ndikuikiranso umboni kuti Mtsogoleri wa Asilamu Aliyy ndi bwenzi la Allah.

Ndikuikiranso umboni kuti Fatima Azzahraa ndi ana ake otetezedwa ku zolakwika, ndimaumboni a Allah.

Ndikuikiranso umboni kuti Abu Bakr, Umar, Uthman, Aisha (Mkazi wa Mtumiki komanso mwana wa Abu Bakr) ndi Hafswa  (Mkazi wa Mtumiki komanso mwana wa ‘Umar) ali kumoto.

Ndikuthawirawira kwa Allah ndi Mtumiki wake (podziteteza) kuchokera kwa Abu Bakr, ‘Umar, Uthman, Aisha, Hafswa ndi adani onse a akubanja la Mtumiki swalla Allahu alaih wasallam.