Bodza la Mashia lonena kuti pali umboni woti Ali radhia Allahu anhu ndi Khalifa woyamba osati Abu Bakr radhia Allahu anhu

 185- حتى لا ننخدع حقيقة الشيعة

Pamene ma Swahaba wonse anagwirizana za utsogoleri komanso ulowammalo wa Abu Bakr, ‘Umar, ‘Uthman, kenako Ali radhia Allahu anhum, palibe lemba lolondola lomwe likunena kuti Ali anatsutsa za utsogoleri wa Abubakr, Umar ndi Uthman kuti unali wolondola monga mmene ma Shia analembera mmabuku mwawo. Ndipotu zimenezi anavomereza mmodzi wa ma ulamaa akuluakulu a Shia, yemwe anali muzaka za mma 19th century pompano,

عبد الحسين شرف الدين الموسوي العاملي

mu buku lake lodziwikanso pakati pa ma shia, ndipo amalinyadira kwambiri buku limeneli, lotchedwa المراجعات, ndipo الموسوي anayankhula pa المراجعة 102, page 302 .. malinga ndi buku lomwe linapangidwa print ndi kugulitsidwa ndi مؤسسة الوفاء بيروت لبنان. Akunena kuti:

Komanso Imaam Ali radhia Allahu anhu mwiniwake, anayankhula momveka bwino mu buku lotchedwa نهج البلاغة lomwe linapangidwa print ndi دار المعرفة بيروت  komanso دار الكتاب اللبناني page 366, Ali radhia Allahu anhu anati:

 “Ndithu anthu omwe anavomereza za utsogoleri wanga ndiomwenso anavomereza za utsogoleri wa Abu Bakr Umar ndi Uthman, ndipo panalibe kuti yemwe sanapezekepo asankhe, kapena yemwe anapezekapo akane; koma kuti Shura ya ma Muhaajineen ndi ma Answaaru ndi imene inachitika.. iwo amati akagwirizana kuti munthu akhale mtsogoleri wawo, zimenezo ndizimene Allah amasangalala nazo. Ndipo wina akawukira izi ponyoza kapena kubweretsapo zachilendo, anali kukanidwa. Ndipo ngati angakanire, anali kulimbana naye ndithu kamba ka kutsata kwake njira yosemphana ndi Okhulupilira…”

Ndipo Ali radhia Allahu anhu anachita kulumbira, kuti iye sanali kulakalaka utsogoleri, izi ndizomwetu analemba الشريف الرضا mu نهج البلاغة 2/184 kuti:

“Wallahi ine sindinali kulakalaka utsogoleri, koma inuyo munandiitanira ndikunditsenzetsa”.

Taonani mmene akuyankhulira Ali radhia Allahu anhu mchitabu chimenechi, mawu oyamba aja akutsimikizira za kusankhidwa pa utsogoleri kudzera munjira ya Shuraa, yomwe inali kuchitika ndi Abu Bakar ndi ena onse. Mawu achiwiriwa akutsimikizira zonena kuti anthu ndamene anamusankha iye kukhala mtsogoleri, osati zoti Mtumiki ndamene anamusankha! Ali radhia Allahu anhu sakudziwa nkhani yopeka imeneyi, yomwe ma Shia anamupekera nkudzadzitsa mmabuku mwawo zopanda umboni! Ndipo ma ulamaa a Shia oyambilira, analongosola momveka ndithu, kuti munthu woyambilira kunena zoti Mneneri aliyense amakhala ndi waswiyyu wake, ndi Abdullah bun Sabai. Ndipo kuchokera pamenepa, ma Shia anamutenga Ali kukhala waswiyy wa Mtumiki Muhammad salla Allahu alaih wasallam. Ali radhia Allahu anhu ndamene anali kudziwa za iye kuposa ma imam onse omwe anadza pambuyo pake (ma imam a shia). Lero tikamanena kuti yemwe anayambitsa mpingo wa Shia ndi Abdullah bun Sabai, timatanthauza kuti ndikumene ma Shia anatengera zikhulupiliro zawo zikuluzikulu, monga zimenezi zongompachika Ameerul Mu’mineena utsogoleri mnthawi yake isanakwane. Kodi inu ma Shia, pakati pa inu ndi Ali ozindikira kwambiri ndi ndani? Nchifukwa chani mukumabisa zomwe mwini wake anayankhula?

Ma Shia akuti Ahlu Sunnah Onse ndi makafir

Izi zili choncho chifukwa choti chikhulupiliro cha Ahlu Sunnah chimakana zoti u imaamah ndi imodzi mwa mapata a Deen. Komanso chifukwa choti Ahlu Sunnah amawakonda Abu Bakr, Umar, Uthman, Aisha, Hafsa ndi ena onse omwe ma Shia amawada.

Ma Shia amati Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti pambuyo pake padzabwera ma imam 12 ochokera m’banja la Ali radhia Allahu anhu. Izizi Ahlu Sunnah wal Jamaah tilibe nazo umboni wokwanira ndipo pachifukwa ichi, sitimakhulupilira. Choncho, ma Shia anawapanga Ahlu Sunnah kukhala makafir chifukwa cha kusagwirizana ndi mfundo imeneyi. Taonani zomwe anayankhula wamkulu wawo pa nkhani ya ma Hadith, Muhammad bun Ali bun Al Husain bun Babawaih Al Qummi, yemwe amamutcha الصدوق, mu kabuku kake kotchedwa الإعتقادات page 103مركز نشر الكتب الإيران 1370, akunena kuti:

“Ndipo chikhulupiliro chathu kwa amene wakanira utsogoleri wa Ali bun Abi Taalib ndi ma imam omwe adadza pambuyo pake, ndichoti ali ngati yemwe wakanira uneneri wa aneneri onse, ndipo yemwe wakhulupilira utsogoleri wa Ali yekha ndikukanira utsogoleri wa mmodzi mwa ma imam odza pambuyo pake, ali ngati yemwe wakhulupilira aneneri onse ndikukanira Mneneri Muhammad salla Allahu alaih wasallam”. Mawu awa akupezekaanso mu chitabu chawo cha بحار الأنوار, vol. 27 page 61.

Iwo amamupachika Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti ananena kuti: “ma imam pambuyo panga adzakhala 12 ndipo woyambilira adzakhala Ali bun Abi Talib, womaliza adzakhala Al Mahdi; yemwe angawamvere amenewa ndiye kuti wandimvera ine, ndipo yemwe angawakane amenewa ndiye kuti wandikana ine. Yemwe angamkane mmodzi wa iwo ndiye kuti wandikana ine”. Izi zikupezeka mubuku lomwe lija. Ndipo الصدوق izi anakopera kuchokera kwa Sheikh wawo محمد
باقر المجلسي mu chitabu chake cha بحار الأنوار, vol. 27 page 61-62:

Ndipo ma Shia akunenetsa kuti ife Ahlu Sunnah tikalowa kumoto ndipo tikakhala kumeneko muyayaya. Iwo akuti yemwe sakhulupilira za utsogoleri wa Ali ndi ma imam ochokera mwa ana ake, mmalo mwake ndikumawakonda achina Abu Bakr, akalowa kumoto muyaya. Izi akuyankhula Muhammad Baqir Al Majlisi mu بحار الأنوار 23/390, chitabu chija momwe mukupezeka zimatalasimu zoopsa chija!

Makaafir akuwapanga Asilamu kuti akalowa ku moto, ndipo iwowo akalowa ku Jannah.
Izitu n’chifukwa chake ma Shia amati ndizololedwa kuwapha Ahlu Sunnah wal Jamaah. Ndithu izi anatsimikiza Sheikh wawo wamkulu komanso mufassir, ابن بابويه القمي, muchitabu chake علل الشرائع  page 601 ط النجف munkhani yochokera kwa داود بن فرقد, yemwe  ananena kuti:

“Ndinati kwa Abi Abdillah alaih salaam:  Mukuti bwanji za kumupha Naaswibi (Ahlu Sunnah)? Ndipo anayankha kuti: “Magazi ake ndiololedwa kukhetsa, koma usamale, ngati ungakwanitse kutembenuza mistake kuti ikhale ya iyeyo, kapena kumumiritsa mmadzi kuti pasapezeke umboni, chita”. Ine ndinati: Nanga ukuwona bwanji chuma chake (ndichololedwa kulanda)? Anati: “wononga momwe ungathere”.

Report lonyansa ngati lomwelinso analitchula sheikh wawo wa وسائل الشيعة komanso wa Anwaaru Nu’maniyya.

Mukabwelera nane mbuyo mumbiri ya mautsogoleri a Chisilamu (Khilaafa), mupeza kuti mu دولة عباسية, chifukwa cha ubwino wa Ahlu Sunnah, anasankha nduna yachi Shia ”Muayyidu Ddeen Ibn Al Alqami “ ndipo iye ndichinyengo komanso udani wake ndi Ahlu Sunnah, anaphetsa ma thousand a Asilamu a Ahlu Sunnah…

Abale anga Ahlu Sunnah wal Jamaah, Mukaferedwa, musaitane pamaliro anu ma Shia!
Chifukwa ma Shia amatembelera maliro a Ahlu Sunnah, ndipo izi zili mmalamulo awo monga mmene ananenera Sheikh wawo Muhammad bun Al Nu’man, yemwe amadziwika ndi dzina loti Al Mufeed, mu buku lake lotchedwa المقنعة page 85 مؤسسة النشر الإسلامي قم إيران, anati:

 “Sizololedwa kwa aliyense mwa anthu a imaan (ma Shia) kusambitsa osemphana ndi haqq pa u imaam (Ahlu Sunnah) akamwalira, komanso asapephelere janaaza yawo, kupatula ngati alibe kuchitira mwina, pamenepo apanga koma mobisa choona chawo, choncho awasambitse masambitsidwe a makafir ndipo akaima pa swalat ya janaza aziwatembelera osati kuwapangira ma dua.”
Mawu omwewanso anayankhula Sheikh wawo Abu Jafar Muhammad bun Al Hasan Al Tousi mu chitabu chake chotchedwa تهذيب الأحكام 1/335 ط3 طهران kapena page 338, potsimikizira kunyansidwa komanso kudana ndi omwe sali munjira ya shia, akunena kuti:

Mmene ma Shia amanyozera ndi kuwapanga ma Swahaba a Mtumiki kuti ndi makafir 

Mashia amatanthauzira ma aayah omwe akukamba za makafir ndi ma munafiq pa ma Swahaaba a Mtumiki, ndithu amatanthauza kuti ma kafir ndi ma munafiq omwe akutchulidwa mma aayahu ndi ma Swahaaba komanso onse omwe amawatsatira ma swahaaba amenewaa. Ndipo kudzra mu chikhulupiliro chawo cha taqiyya, amawatchula ma Swahaba atatu (Abu Bakr, Umar ndi Uthman) ndi zizindikiro komanso mawu ena osamveka ncholinga choti tisazindikire mwachangu ifeyo. Koma lero tiwulula ndithu taqiyya imeneyi.

Ma Swahaba atatuwa amawatchula pogwiritsa ntchito mawu awa: الفصيل kutanthauza Abu Bakr, رمع kutanthauza Umar, ndipo نعثر kutanthauza Uthmaan. Ndiye alinso ndi mawu ena omwe amawagwiritsa ntchito pa iwowa monga الأول، والثاني، والثالث (Woyamba, Wachiwiri, Wachitatu) kutanthauza kuti Abu Bakr Umar ndi Uthman. Alinso ndi maina ena monga حبتر، دلام kutanthauza Abu Bakr ndi Umar, kapena Umar ndi Abu Bakr. Komanso ali ndi dzina lonyansa ili lomwe amawatchulira Abu Bakr ndi Umar, صنما قريش. Maina ena ndi monga فرعون و هامان kapena عجل الأمة والسامري akutanthauza Abu Bakr ndi Umar. Penanso amatha kumawatchula kuti فلان و فلان  kutanthauza Abu Bakr ndi Umar!

Abale anga Asilamu, kodi chipembedzo cha mtundu wanji ichi chonyoza ma Swahaba akuluakulu komanso okondedwa ndi Mtumiki swalla Allah a;aih wasallam? Iye anawatchula kuti akalowa ku Jannah mugulu la anthu 10, koma ma Shia amatsutsa … kumutsutsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam! Ma kaafir ndindani pamenepa?

Tatiyeni tioneko momwe amatanthauzilira ma Aayah a mu Qur’an potukwana ma Swahaba akuluakuluwa, ndikupatsani ma Aayah ochepa chabe:

الكليني mu buku lake lalikulu la الكافي vol. 8 nkhani ya number 532, akunena kuti:

Nayenso المجلسي analemba mu chitabu chake chotchedwa مرآة العقول volume 26 p.488, popanga sharh الكافي pa liwu loti –هما, iye anati:

Komanso mu تفسير العياشي  1/121 ndi البرهان  2/208, komanso الصافي  1/242, akunena kuti:

Komanso mu تفسير العياشي momwemu, 2/355, البرهان  2/471, الصافي  3/246, akunena kuti:

Komanso mu Aayah ina,  تفسير العياشي1/422, anatanthauzira motere:

Ndipo mu Tafsir yomweyi, 2/240, komanso البرهان  2/309, akuti Umar radhia Allahu anhu ndi Shaytwaan, pakutanthauzira kwawo Aayah iyi:

Tisiyire pamenepo, mwachidule, ma Aayah onse omwe amakamba za ma kaafir komanso ma munaafiq, ma Shia amatanthauzira kuti ma kaafir ndi ma munaafiq amenewa ndi Abu Bakr, Umar ndi Uthman radhia Allahu anhum.