Nisaab ya Zakaat za mbewu ndi zomera:
Kapelekedwe ka zakaat za mbewu zimenezi.
Pambuyo poti taona kuti ndimitundu iti ya mbewu yomwe Allah walamula kupereka Zakaat, ndipo tapeza kuti chimanga komaso mpunga mpira mawere ndi zina zomwe ambiri timalima kuno ku mudzi zili mu gulu la mbewu zoti tizichotsapo zakaat,
Tsopano tiyeni tione mitundu ya ulimi ndi kaperekedwe ka Zakaat.
Kumbali ya kapelekedwe ka Zakaat ya ulimi wa mbewu titha kugawa pawiri motere:
A) ulimi wa mbewu zomwe madzi ake akubwela mwa chilengedwe mmundamo kaya mu dimbamo.
B) ulimi wa mbewu zomwe madzi ake akubwera chifukwa cha anthu mmundamo kapena mudimbamo.
Magawo awiri amenewa tawagawa motere popeza kuti kaperekedwe ka zakaat kamasiyana malingana ndi mmeme madzi amafikira mmundamo.
Tiyeni tiyambe kuwona gawo loyamba:
A) ulimi wa mbewu zomwe madzi ake akubwela mwa chilengedwe mmundamo kaya mu dimbamo
Apapa tikutanthauza mlimi uja amene amangodalira madzi amvula kuti agwe kumwamba nkumakulitsa mbewu zake.
Pamenepa pakulowaso alimi omwe minda yawo ili m’mbali mwa mtsinje kaya dambo loti nthaka imanyowa yokha automatically ndipo sipafunika mphanvu kuti nthaka inyowe.
Alimi amenewa Zakaat amapereka mochulukirapo monga mmene ikukambira hadeeth iyi:
Jabir analongosola kuti Mtumiki anati:
فيما سقت السماء والعيون أو كان عثريا العشر
📚 رواه البخاري
“Pa mbewu zomwe zathililidwa ndi nvula, mitsinje kapenaso timakhwawa ta madzi achilengedwe papelekeke 1/10 (kapena kuti 10%)”
Pomwe gawo lachiwiri lomwe talitcha:
B) ulimi wa mbewu zomwe madzi ake akubwela chifukwa cha anthu mmundamo kapena mudimbamo.
Apa tikutanthauza opposite ya gawo loyambalo kapena kunena kuti anthu amathilira okha mmundamo kapena mu dimba; kumatunga madzi mutsinje kaya mu nyanja ngakhale mu zitsime kaya ndima tradle pump etc.
Ulimi uwu womwe tingautche kuyi wamthilira (irrigation) Zakaat yake imakhala yocheperako ngati mmene Mtumiki ananenera:
Jabir uja anatiso Mtumiki anati
وما سقي بالسنية نصف العشر
📚 رواه مسلم
Pa mbuwu zomwe zathililidwa ndi gamila papelekedwe theka la 1/10 (kapena kuti 5%)
Amenewa nde magawo a ulimi omwe Zakaat imasiyana kaperekedwe.
Tatiyeni tione tsopano za Nisaab ya Zakaat za mbewu
Malingana ndi kufotokoza kwa Mtumiki, Nisaab ya Zakaat ya mbewu ndi imodzi posatengela kuti ulimi unali wa irrigation kapena wamadzi a chilengedwe.
Abu Saeed Al khudriyy anati mtumiki anati
ليس فيما دون خمسة أوسق صدقة
📚 رواه البخاري
Zakaat siziyenela kupelekedwa pa mbewu zochepela ma wasq okwana asanu 5
Nkhani apa ndiyoti kodi ma wasq ndi mlingo wochuluka bwanji?
Tatiyeni tiwone:
Ma ulama a zofufuza za mlingozi anena kuti:
Wasq = pafupifupi 130500 grams
Ndiyek titakhaka tikufuna tipititse can mulingowu ku ma kilograms (Kgs) tigawa ndi 1000
Yomwe ili = 130.5kgs
Ndiye hadeeth yanena kuti
Zakaat iyenela kuperekedwa mbewu zikafika 5 wasq
Ndiyek ikhala 130.5kgs × 5
Yomwe ili 652.5kg
Ndiye kuti mbewu zathu tikakolola ndikufika ma Kgs ake amenewa (652.5kg) tikuyenera kupereka Zakaat ndipo imeneyo ndiye Nisaab ya Zakaat ya mbewu.
Koma kaperekedwe kake kakhale kotani? Tipereke nthawi yanji? Kodi pakuyenera padutseso chaka?
Mafuso amenewa ayankhidwa pomwe tibweretse ndi ma example omwe.
Your Comments