Tsopano tikhala tikuona gawo lachiwiri la Zakaat ya ulimi womwe ndi ulimi wa mbewu ndi zomera.

Nnenemu tiona kuti ndi zomera ziti zomwe tikuyenera kupereka Zakaat.

Tinamaliza kuwona Zakaat ya mbuzi, nkhosa komaso ng’ombe ngati ziweto zomwe amalawi timakhala nazo kuno ndipo tasiya ngamira powona kuti kuno sizipezeka ndithawi yoti tigwele ku gawo la za ulimi.

Pomwe magawo ena aja gawo la za ulimi wa mbewu ndi lomwenso ambiri timapezekamo chifukwa timapezeka tikulima ndithu.

Tinadzanena kuti Allah walimbikitsa zopereka Zakaat pa zomera pomwe wanena mu Qur’an kuti:

Surah Al-Anaam, Aayah 141

.. كُلُوا مِن ثَمَرِهِ إِذَا أَثْمَرَ وَآتُوا حَقَّهُ يَوْمَ حَصَادِهِ…

Idyani zipatso zake zikapatsa komaso pelekani gawo lake (zakaat) tsiku lomwe mwakolora

Monga mmene tikudziwira kuti alimi amalima zosiyanasiyana monga zipatso, zamasamba kaya zanjere monga mpunga nyemba chimanga ndi zina zotero,

Kodi ndi ziti mu zomera zimenezi zomwe zikuyenera kuperekedwa Zakaat?

Ma ulama afotokoza kuti sikuti ndi mbewu zonse zomwe ziyenera kaperekedwa Zakaat.

Zomera zomwe zikuyenera kuperekedwa Zakaat zayenera kukhala ndi mbiri ziwiri awa:

1. Zikhale zoti zitha kusungika moumitsidwa.

Apa tikutanthauza kuti zokolola zoti tikakolola ndiye zauma zitha kusungika kaya mmatumba, koma mopanda kuthandizira ndi zithu zamakonozi ngati fridge ndi zina zotero.

Taonani mtumiki akuti

ليس فيما دون خمسة أوساق من حب ولا تمر صدقه

📚 رواه مسلم

Zakaat siikuyenera kuperekedwa pa tende ndi njere zomwe zachepera pa 5 awsuq

Mtumiki akutchula minimum kapena kuti Nisaab ya mbewu komanso watchula mbewu zake, iye wati:

Tende ndi njere

Njere ndi tende ndi zinthu zoti timaumitsa ndikusunga.

Zitsanzo zanthu ku Malawi kuno apa zitha kukhala zinthu monga:

1. Chimanga
2. Nyemba
3. Mpunga

Zimenezi tikakolola, zikauma timasunga bwino bwino.

Quality yachiwili yomwe iyenera kupezeka mu zomera zomwe ziyenera kuperekedwa Zakaat ndiyakuti:

2. Zikhale zoti zitha kumayezeka

Zoperekazo zikhake zoti titha kuziyeza mwa simple kaya mma Kg kaya mma Grams ndipo zisakhale zinthu zoti siziyezeka ngati zachimamasamba.

Pali ma Hadeeth omwe abwera pa zimenezi ambiri, koma kuti ochuluka ndiofooka monga yomwe imanena kuti:

ليس في الخضروات صدقة

Zakaat siziyenera kuperekedwa pa zinthu zamasamba

Monga mpiru, repu ndi Zina zotero, komanso tomato mabilinganya ndi zina.

Ngakhake kuti ma Hadith amenewa ndiofooka koma poona kut zimenezo ma Swahaba samapereka Zakaat, ma Ulamaa anagwirizana kuti zimenezo sizoti Zakaat iperekedwere.

Imam Ahmad ibn Hanbal anati

ما كان مثل الخيار والقثاء والبصل والرياحين فليس فيه زكاة

Zinthu zokhala ngati zinkhaka, anyezi … sipakuyenela kuperekedwa Zakaat