“Akalowa bwanji ku ng’anjo ya moto akadaulo, akatswiri komanso anthu ena amene anachita ndi kugwira ntchito zopambana, ndizopititsa patsogolo umoyo wa anthu pa dziko lino lapansi?.

– Anthu okanira amene anagwira ntchito yotamandika pa dziko lapansi, sanagwire ntchito imeneyi ndi cholinga chofuna kupeza malipiro abwino (thawab) kuchokera kwa Mulungu. Koma amapanga zimenezi ndi cholinga chofuna kukhala apamwamba ndi olemekezeka pamanso pa anthu kapena kufuna chuma ndi kutchuka. Ndipo izi zinatheka kwa iwo monga mmene Allah Subhanah wataala akunenera mu buku lolemekezeka la Quran.

مَن كَانَ يُرِيدُ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا وَزِينَتَهَا نُوَفِّ إِلَيْهِمْ أَعْمَالَهُمْ فِيهَا وَهُمْ فِيهَا لَا يُبْخَسُونَ (15) أُولَٰئِكَ الَّذِينَ لَيْسَ لَهُمْ فِي الْآخِرَةِ إِلَّا النَّارُ ۖ وَحَبِطَ مَا صَنَعُوا فِيهَا وَبَاطِلٌ مَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (16)
“{Amene akufuna dziko lapansi ndi zokometsera zake tiwapatsa pompo pa dziko lapansi (malipiro a) zochita zawo mokwanira, ndipo iwo m’menemosachepetseredwa chilichose}” (15) “{ Iwo ndi omwe sadzakhala ndi kanthu tsiku la chimalizirokoma moto basi, ndipo zimene adachita m’menemo zidzaonongeka, Ndiponso ndizopanda phindu zimene ankachita}” (16) Surah Hud ayah 15:16

– Ndipo ngati anthu amenewo ali ndi ubwino pa anthu pa dziko lino lapansi ifeyo ndi amene tikufunika kuwalipira, koma iwowo pamanso pa Mulungu alibe ubwino ulionse (Mulungu atichitire chifundo) ndipo iwowo ali ofunika kubweza ubwino wa Mulungu pa iwowo kuponsa wina aliyense. Chifukwa Mulungu anawapatsa maphunziro,nzeru komanso kuthekera kumeneko ndipo sanapatse wina aliyense kupatula iwo okha. Komabe anali okanira ubwino umene Mulungu anawapatsa. Ndipo anazisintha zimenezi ndikukhala ngati zimachitika mu mphamvu zawo. Ndichifukwa chofuna kuzikweza pa dziko lino lapansi.

Kwa anzathu achisilamu amene amawapemphera zabwino (R.I.P)anthu okanira akamwalira chifukwa cha malo amene anali pa dziko lino lapansi kapena zimene anachita ali moyo tikufunika kumadziwa malamulo achipembedzo chathu cha chisilamu tisanachite kanthu.