Pakukhala kuti Chisilamu chidaunikira mbali zonse za umoyo, Mu Qur’an ndi Mahadith (zoyankhula za mtumiki). Ndipo masahabah Adagwira ntchito yotamandika yotulutsa khokwe za maphunziro kuchokera mu Qur’an ndi Mahadith, pambuyo pawo padabweraso Ma Imam ndi anthu ophunzira bwino malamulo a sharia amene adagwira ntchito yotambasula bwino Zomwe zidabwera mu Qur’an ndi Mahadith,choncho tipeza kuti ma scholar samagona kapena kupuma Chifukwa chotangwanika ndi kutulutsa nkhokwe zakuzindikira mu Qur’an ndi Mahadith Nalemba mabukhu ochuluka ofotokoza mbali zonse za umoyo wamunthu padziko lapansi ndi zomwe adzazipeze ku umoyo omaliza.
Kutanthauza kuti KUUNIKIRA sikuti izibweretsa zithu zachilendo koma kuti izifotokoza zithu kuchokera mmabukhu omwe adatisiyira Ma Imam athu (كتب التراث الإسلامي) ndi anthu ophunzira bwino anthawi ino.Ulendo uno Tatiyeni Tioneko mbali yamalonda ndipo malonda ake ndi kuwoda katundu nkumusunga kuti udzagulitse nthawi ina mitengo itakwera, timaona anthu ena akuwoda chimanga mu nthawi yokolora Kapena Ntundu wambewu ulionsewo,akatero amazisunga nkudzagulitsa nthawi yokwera mitengo pamene Mbewu zimakhala zasowa monga miyezi ya December, January ndi miyezi ina, kodi Malonda otero ndi ololedwa Mchisilamu?
Anthu ophunzira (scholars) adagwirizana zakuletsedwa (haram) kwamalonda amenewa Ndipo Munthu ogula katundu wamalonda nkumamusunga kuti adzagulitse mitengo itakwera ndi wamachimo,Chifukwa Kugula katundu pamtengo okwera zimapeleka vuto kwa anthu kumbali yachuma , *Kotero Kusunga katundu nkudzagulitsa atakwera mitengo* ndi Ntchimo Chifukwa ndi nkhanza kwa anthu omwe ali ochepekedwa,Chisilamu chimalimbikitsa kuchitirana Chisoni nthawi zonse ndi kukondana.
Ndipo mtumiki adaletsa malonda oterewa 
عن أبي هريرة رضي الله عنه قال: قال رسول الله ﷺ: «منِ احْتَكَرَ حِكْرَةً يُريدُ أن يُغْلِيَ بها علىٰ المسلمينَ فهو خاطِئٌ» أخرجه الهيثمى فى مجمع الزوائد.
Hadith idachokera kwa Abu Hurairah Allah asangalale nawo adati: adayankhula mtumiki Muhammad madalitso ndi mtendere zikhale pa iye Amene angasunge katundu ndi cholinga choti adzawakwezere mitengo Asilamu (powagulitsa) Ameneyo ndi ochimwa*
Mwina ofunsa atha kumati mu Hadith yi mtumiki sadaletse koma wangotchula zakuti ndi Ntchimo, Dziwani abale olemekezeka kuti Mtumiki akatchula liwu la tchimo kapena thembelero pa Ntchito ina yake zimatathauza Kuti ntchito yo ndi yoletsedwa,Chifukwa munthu sangatembeleledwe kapena kuchimwa kupatula pa zithu zomwe zili Zoletsedwa kuzichita.
Mu kuyankhula kwina kwamtumiki akuti 
– يقول النبي ﷺ: «لا يحتكر إلا خاطئ» أخرجه مسلم.
Sangasunge Katundu wamalonda nkuzamugulitsa mitengo itakwera kupatula yekhayo yemwe ali ochimwa.
Abale olemekezeka dziwani kuti malonda oterewa ndi oipa Ndipo ndi nkhanza komaso ndi kusonyeza zakusangalatsidwa kuti wina azivutika,Ndipo ndi chiyambi chosowekera chilungamo m’dera kapena m’dziko.
Pachifukwa ichi ndi Zoletsedwa kuchita malonda amenewa,Ngati munthu umagulitsa chimanga uyenera kumagulitsa Nthawi zonse kwa miyezi Yonse,pomwe kuwoda chimanga kapena mpunga nkuzisunga kudikira kuti Afike January kapena February nde udzazigulutse pamtengo okwera ndi Zoletsedwa mchisilamu,Aliyense opeza chuma munjira imeneyo adziwe kuti Akudya chuma cha Haram chopondeleza.
Lamuloli likulowa pa katundu wamalonda aliyenseyo njere kapena sinjere,ngakhale atakhala mankhwala Sizololedwa kuwoda nkudzagulitsa mitengo itakwera.Ndi udindo waboma kuthana ndi malonda oterewa,Kuti aliyense adzikhala ndi umoyo osangalala komaso osachitirana Kaduka, Ndipo ndi udindo wa aliyense m’dziko kupewa malonda oterewa choncho Anthu angathe kukhala okondana ndi ofunirana zabwino ndinso osachitirana msanje ngati wina akutukuka,chifukwa Munthu akamachita malonda oterewa zimadzetsa msanje mmitima mwa anthu ndi kudukidwa ndi kusowekera kwachikondi pakati pa Anthu.