Wapita mwezi wa madalitso, Mwezi wa mapemphero, mwezi wa Qur’an, mwezi opeleka Chopeleka, Mwezi ochulukitsa zabwino, wapita basi mwezi umene oluza aluza opambana apambana, apambana amene adasala mwa chikhulupiliro natsatira ziphuzitso za Sharia zakusala, apambana amene adasala ndi lilime lawo ku zinthu za Haram,amene adasala ndi ziwalo zawo ku zinthu zimene Allah adaletsa kuzichita Masana kapena usiku, moonekera kapena mobisika, ndiye pambuyo pakupita kwa mwezi opambanawu ndi chiyani chimene Msilamu akuyenera kumachita kwa miyezi yatsalayi kukafika mu Ramadhan ina Inshallah?
Inde Ramadhan yapita koma idabwera kudzatiphunzitsa kuopa Allah pakukhala kuti Cholinga chakusala mu mweziwu ndi kuopa Allah
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آَمَنُوا كُتِبَ عَلَيْكُمُ الصِّيَامُ كَمَا كُتِبَ عَلَى الَّذِينَ مِنْ قَبْلِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ
Eeh inu okhulupilira kwakakamizidwa kwa inu kusala ngati momwe kukakamizidwira kwa anthu akale,kuti mukhale owopa Allah. Qur’an 2:183.
Kodi kuopa Allah ndi chiyani ? kumuopa Allah kudatanthauzilidwa mu njira zosiyanasiyana, koma matanthaunzo onsewo pothera pake ndi kuchita zi ntchito zabwino (momusangalatsa Allah) ndikusiya zauchimo,Kuopa kumeneku ndi kumene kudzamuteteze munthu ku Moto wa Jahena,umene Allah akuyankhula
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ قُوٓاْ أَنفُسَكُمْ وَأَهْلِيكُمْ نَارًا وَقُودُهَا ٱلنَّاسُ وَٱلْحِجَارَةُ عَلَيْهَا مَلَٰٓئِكَةٌ غِلَاظٌ شِدَادٌ لَّا يَعْصُونَ ٱللَّهَ مَآ أَمَرَهُمْ وَيَفْعَلُونَ مَا يُؤْمَرُونَ.
Eeh inu okhulupilira, dzitetezeni nokha ndi mawanja anu ku Moto umene Nkhuni zake ndi anthu ndi miyala,Kuli Angelo owuma mtima (opanda Chisoni pokwanilitsa lamulo la Allah) amphamvu, samunyozera Allah pazimene awalamula,ndipo amapanga zimene alamulidwa.Qur’an 66:6.(choncho kuopa Allah ndi chitetezo chodzakutetezani ku Moto wa Jahena, mukasiya kuopa Allah ndiye kuti mwasiya chodzakutetezani)
Allah akuyankhula:
وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّكُمْ مُلَاقُوهُ وَبَشِّرِ الْمُؤْمِنِينَ
Ndipo Muopeni Allah,ndinso dziwani kuti Ndithu mudzakumana naye (kuyambira tsiku la Imfa yanu ndi tsiku la chiweruzo) ndipo uwasangalatse okhulupilira ochita zabwino (Kuti adzakhala ndi malipiro abwino aku Jannah). Qur’an 2:223.
Choncho Ramadhan ndi Sukulu imene idangobwera kudzatiphunzitsa kumuopa Allah kuti tipitilire nako kwa miyezi imene yatsalira,chifukwa ena amaona Ngati mu Ramadhan ndi mochita zabwino monga kupemphera, Ramadhan ikatha kusiyaso kupemphera, kuwerenga Qur’an kenako Ramadhan ikapita kusiya kuwerenga … mpaka ena mu Ramadhan adasungira zauchimo ndikumati mwezi uno ndi wa Ramadhan tidzapanga Ramadhan ikatha…kukhala ngati mu Ramadhan zinthu za Haram zimakhala za Haram, ndipo Ramadhan ikatha zimaloledwa kuzichita, kukhala ngati Msilamu wamasuka … ayi si choncho mwezi wa Ramadhan ndi mwezi opambana ndipo ntchito ya bwino imene Msilamu amayichita mu mweziwu imakhala ndi malipiro ochuluka Kwambiri kuposera miyezi ina,ndipo tchimo limene Msilamu amalichita mu Ramadhan limakhala lalikulu Kwambiri kuposera miyezi ina, pakukhala kuti wanyalanyaza kulemekezeka kwa Ramadhan ndikusaona kupambana kwake pakusefukira kwake ndikupyola malire pochita zauchimo,koma sikutathauza kuti Ramadhan ikatha ndiye kuti Msilamu wamasuka ayi,Zaharam zidzakhalabe zaharam mu mwezi ulionse.
Choncho chomwe Msilamu akuyenera kutenga mu Ramadhan ndi makhalidwe amene amene adali nawo mu mweziwu,kusunga lilime ku zinthu zaharam, kusunga maliseche ku zinthu zaharam, kusunga maso ku zinthu, kupemphera limodzi ndikusala kwa Sunnah mmene munthu angakwanitsire,kutsatira ziphunzitso za chisilamu pang’ono panzake,ndikusautengera mtima Ndi zofuna za Shaytan.Timalize ndi mawu a Mtumiki Muhammad madalitso ndi zikhale pa iye
عن ابى سعيد الخدري رضي الله عنه قال :قال صلى الله عليه وسلم: «اتقوا الدنيا واتقوا النساء»؛ رواه مسلم
Hadith ikuchokera kwa Abu Said Al-khudriyy Allah asangalale naye adati: adayankhula Mtumiki Muhammad madalitso ndi zikhale pa iye Kuti: liopeni dziko lapansi ndipo awopeni akazi.
Ndi zoonadi tikuyenera kuliopa dziko lapansi,mayesero ndi osayamba ndipo sikalikonse kamene anthu akuchita kuti ndi koyenera kuchita nawo,pakuti Allah adanena kale mu Qur’an kuti anthu ambiri ndi ochimwa,izi ndi zoona zake ,titati tiwerenge ma percent a Anthu abwino ndi owonongeka ndi owononga, achuluke ndi anthu owonongeka, abwino Alipo koma si ambiri,ndi chifukwa chake Mtumiki adanena kale kuti idzafika nthawi imene kugwiritsitsa ziphunzitso za chipembedzo kudzakhale kovuta Ndi kopweteka ngati kugwira khala la Moto,Tipemphe Allah kutitetezera ku zoipa za dziko lapansi ndinso atipatse mitima yowopa.
Your Comments