1. Imaam kupanga dua ya pagulu pambuyo pa swalat Janaazah. 
Palibe chiphunzitso choti imaam akaswalitsa swalat Janaazah apange dua anthu nkumavomera kuti Ameen. 
2. Kuimba kapena kupanga ma adhkaar mokweza poperekeza kumanda
Imeneyi si sunnah ya Mtumiki ndi ma Sahaba ake. Zomwe zili sunnah ndizoti anthu aziyenda mwakachetechete poperekeza maliro kumanda; asaimbe ngakhale mau oti laa ilaaha illa Allah,  chifukwa muChisilamu mulibe zoterozo,  ndipo ngati anthu amachita ndiye kuti amatengera zomwe akhristu amapanga poimba nyimbo za m’baibulo lawo. 
Nthawi Imeneyi ndi nthawi yoti munthu adziyenda mwakachetwchetw kulimgalira za imfa, maina mawa ndi ine. Mmalo mokhala busy kuganizira zoti titulutse bwanj  mau kuti zoimbazi zimveke bwino. 
Choncho ngati mungafume lupanga ma dua pa ulendo was ku manda,  ndibwino kumanena chamumtima may omwe aja; Allahummah ighfir lahu, Allahumma thabbit’hu.
Chimodzodzinso palibe dhikr kapena nyimbo ya pokwilira manda.
Zofunika kwambiri ndikutsatira zomwe anaphunzitsa Mtumiki ndipo ma Sheikh, anthu sakuyenera kuyendera njira zawozawo zowaletsera anthu kulongolola poperekeza jeneza. Awaphunzitse kuti akuyenera kumatani popita kumanda osati kuwaphubzitsa kuimba zosemphana ndi chiphunzitso cha Mtumiki. Zikanakhala kuti zoimbazo nzabwino bwenzi Mtumiki atatiuza kuti tidzitero. Choncho tisachuluke nzeru kuposa Mtumiki.
Tikamaperekeza jeneza tidziyenda mwakachetechete uku tikulingalura za imfa komanso kuganizira Tsiku lalikulu lomwe tidzakumane ndi munthu omwalirayo. Tidzichulukitsa kumpangira munthuyo istighfaar (kumpemphera chikhululuko) komanso kumuchitira ma dua chamumtima. Osati kuimba pagulu mau monga “laa ilaaha illa Allah Muvammadun Rasulu’Llaah”.
Nzachisoninso ambiri amangoimba samadziwa kuti akuimbazi nzichani,  mapeto ake amangophwanya mau aakulu ngati amenewa.
3. Kusangalatsa maliro. 
Azimai ena amapita kumaliro ncholimga choti akasangalatse polira mokongoletsa komanso kunenelera. Ichi ndi chikhalidwe chimene chinalipo nthawi ya kale shari’ah isanabwere ndipo itabwera inachithetsa. 
4. Kupanga Adhan ndi iqaamah pa manda. 
Eyetu izi zimachitika mmadera ena akamaika maliro. Izi mChisilamu mulibe ndipo ndi bid’ah. 
5. Kupanga talqeen pambuyo pa kukwilira manda.
Akuti kumukumbutsa munthu omwalira kuti akabwera Angelo kudzamufunsa kuti man Rabbuka,  ayankhe kuti Allah Rabbi… 
Imeneyo si talqeen. Talqeen ndi kumuyankhulitsa munthu ndipo, adzibwereza zomwe mukumuyankhulitsazo. Choncho talqeen sikhalapo kwa munthu wakufa.
6. Kuwerenga Surah Al Fatiha, Yaasin,  ndi zina zotero pambuyo pakuika maliro mmanda.
Imeneyi ndi bid’ah. 
7. Kudzala mtengo kapena kuika zimasamba za mtengo wa tende (kanjedza) pamanda
Zimenezinso ndi bid’ah; mu Chisilamu mulibe zimenezo. 
8. Kusonkhana kunyumba ya maliro, 
kapena kunyumba ya wina wake,  kapena mall aliwonse ncholinga chopanga ta’ziya ndikumawerenga Qur’an ndi ma dua. Ta’ziya si choncho. Ena mpaka anaisandutsa ta’ziya kukhala ngati chikondwelero kapena chikumbutso;  ndiye amagula chakudya,  kukhonza malo okhala anthu ndikubweretsa zonunkhiritsa zija, basi nkumawerenga ma dua ndi Qur’an pamenepo, uku azimai akuphika thobwa ndi nsima. 
9. Kuphikira chakudya anthu omwe abwera pa maliro. 
Ndi sunnah kwa anthu oyandikana ndi nyumba yomwe kwachitikira maliro, kukhonzera chakudya anthu omwe achokera kutali. Chifukwa eni ake pakhomopo amakhala kuti ali pa mavuto. 
Ndiye timaona masiku, ano zosemphana ndi sunnah, chakudya chimakhonzedwa ndi anamfedwa,  ndipo ena amapita kumaliro kuja patatha masiku atatu kuti akamwe nawo tea.
10. Kusonkhana pakutha pamasiku angapo,
anthu nkumawerenga Qur’an ndipo eni ake pakhomopo amapereka ndalama kwa owerenga Qur’an. 
11. Kuwerenga Qur’an zija amati khitma, 
posonkhanitsa anthu ndikuwagawanitsa zuj imodzi imodzi mpaka Qur’an yonse kutha. Zimenezo ndi bid’ah. 
12. Kunyamula manda pokwilira.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsa kunyamuka manda pokwilira.  Sitimayenera kubwezeretsa dothi lonse lomwe lakumbidwa, chifukwa tikatero timakhonza kachulu kamene Mtumiki analetsa. 
13. Kukhonza masiku opangira ziyaarah kumanda,
monga tsiku loyandikana ndi la Eid, ysiku lachisanu, masiku a Dhul Hijja… 
14. Kupanga phwando pakutha pa masiku atatu (taatu), seven (saba) komanso 40 (arbaeen).
Izi Mchisilamu mulibe ndipo zinayambitsidwa nthawi ya a Farao ku Egypt kenako nkufalikira ngati za Chisilamu. 
Amene amaphika sadaqa pakutha masiku 40 nkumati arbaeen, amatsatira sunnah ya kumoto ya Fir’aun. 
15. Kukhonza ma sadaqa mmwezi wa Dhul Hijjah (nthawi ya Qurbaan) pokumbukira anthu amene anamwalira.
Ndiye amatemga list la anthu omwe anamwalira dera, limenelo nkumatchula dzina limodzi limodzi pambuyo pa dua yoti: *Allahumma ighfir lahu warhamhu wasakkinhu makaanan fil Jannah*, uku akuthudzulira ubani pamoto. Pambuyo pake kudyelera mphunga,  nsima,  ndikumwelera thobwa. 
Chisilamu sichinaphunzitse zimenezo. Dua Imeneyi kumainena pambuyo pa kuika mmanda pamene, mwaima chozungulira manda musanabalalike. Osati after 40 days munthu wakwapulidwa kale manda amupanapana kale. 
Ma bid’ah a pamaliro ndi ambiri kuposa zomwe ndatchulazi. 
Choncho ndizofunikira Msilamu kutsatira sunnah za Mtumiki ndipo asayambitse zakezake,  zidzamubwelera Tsiku la Qiyaama ndipo adzatenga nsambi za onse omwe atsatira zimenezo. 
Masiku ano ambiri akauzidwa kuti, akhonze zolakwika zimenezi amanena kuti tinawapeza azigogo anthu akupanga ndiye sitingasiye. Mmalo moti tivomereze kuti azigogo athuwo ankalakwitsa ndipo tiwapemphere chikhululuko chifukwa mwina ankachita asakudziwa, tikudzipitiriza ndikumawaonjezera machimo ndi mavuto ammanda ndi Tsiku la Qiyaamah. 
وإذا قيل لهم اتبعوا ما أنزل الله قالوا بل نتبع ما ألفينا عليه آباءنا أولو كان آباؤهم لا يعقلون شيئًا ولا يهتدون} (البقرة:170). ويقول في موضع آخر
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti tsatirani zomwe Allah anatsitsa,  amanena kuti ‘koma ife tikutsatira  kuchokera kwa azigogo anthu’, kodi sakudziwa kuti azigogo awowo sanali kuzindikira kalikonse komanso sanali mchiwongoko? Surah Al Baqarah 170.
وإذا قيل لهم تعالوا إلى ما أنزل الله وإلى الرسول قالوا حسبنا ما وجدنا عليه 
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti idzani ku zomwe Allah ndi Mtumiki wabweretsa, amanena, kuti ‘zatikwanira ife zomwe tinawapeza nazo azigogo anthu’. Surah Al Maaidah 104