Kuzikongoletsa zinthu za haram nkuzisandutsa kukhala za halaal popanda umboni kuchokera mu Qur’an ndi Sunnah:
KUIMBA NDI KUMVERA NYIMBO

Abu Turaab Adhwaahiri analemba article mu magazine yotchedwa Al-Raaid kuti: Qur’an ndi Sunnah sizinaletse nyimbo, komanso sizinaletse kugwiritsa ntchito zida zanyimbo ngakhale kumvera. Analongosola izi pogwiritsa ntchito ma hadith komanso nkhani zina zololeza nyimbo potsatira imam wake Abu Muhammad ibn Hazm Adhwaahiri. Komanso anagwiritsa ntchito zoyankhula za imam wake Abu Muhammad Ali yemwe anawapanga ma Hadith onse omwe akuletsa nyimbozi kuti ndi ofooka, ndipo sanasiyire pompo koma anatsindika polankhula monyoza kuti ma hadith amenewo ndi opeka. Ma aayah komanso ma Hadith ambiri omwe ndi oona opanda chikaiko chirichonse alongosola za kuletsedwa kwa nyimbo za zida, koma ma imam amenewa anakanira, ndipo anawalimbikitsa anthu kutsutsa ma ayah ndi ma hadith amenewa.

Ndikupempha chikhululuko cha Allah Ta’la komanso atidalitse pakuyankhula zabwino ndikupewa kuyankhula zopanda nazo kuzindikira kulikonse, ndipo atitalikitse ndikupanga halal za haram popanda umboni wochokera kwa iye ndi Mtumiki wake.
Ma ulamaa odalirika anatsutsa kale zoyankhula za imam ameneyu ndipo anachenjeza za kutenga zoyankhula zake zonse, chifukwa zambiri mwa izo zinasokoneza Ummah ndipo ena mwa otsatira zimenezo ndi omwe akuchita makani panthawi ino potsutsana ndi ma ayah ndi ma Hadith oletsa nyimbo. Fitna inakwanira pakati pathu chifukwa cha ma sheikh osocheretsa, omwe amati akayankhula kapena kulemba mma social mediamu ena nkunena kuti nzolakwika, anthu ena amafunsa mafunso ngati awa: “kodi sheikhwo sankadziwa koma inu? Kodi inuyo ndiye ophunzira kuposa sheikhwo?..”

Konseko kumakhala kusapota bodza lomwe akulalikiralo, komanso kukomedwa ndi zinthu za haraam zomwe sheikhwo akuzipanga kukhala za halal.Allah atiteteze ku fitna imeneyi.
Allah Ta’la anachenjeza za kumuyankhulira zinthu zomwe tilibe nazo kuzindikira komanso anatiletsa kuloleza ndi kulesa zinthu popanda umboni. Iye (Allah Ta’la) anatichenjeza kuti imeneyo ndi ntchito ya shaytwaan yemwe amanka nakongoletsa zoipa pakati pa anthu:

قُلْ إِنَّمَا حَرَّمَ رَبِّيَ الْفَوَاحِشَ مَا ظَهَرَ مِنْهَا وَمَا بَطَنَ وَالْإِثْمَ وَالْبَغْيَ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَأَنْ تُشْرِكُوا بِاللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِ سُلْطَانًا وَأَنْ تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ

“Nena (kwa iwo): “Ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu zauve zoonekera ndi zobisika, ndi machimo, ndi kuwukira (atsogoleri) popanda choonadi, ndi kumphatikiza Allah ndi chomwe sadachitsitsire umboni (wakuti chiphatikizidwe ndi Iye); ndiponso (waletsa) kumunenera Allah zimene simukuzidziwa.” Al A’raaf #33

وَلَا تَقُولُوا لِمَا تَصِفُ أَلْسِنَتُكُمُ الْكَذِبَ هَذَا حَلَالٌ وَهَذَا حَرَامٌ لِتَفْتَرُوا عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ إِنَّ الَّذِينَ يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ لَا يُفْلِحُونَ * مَتَاعٌ قَلِيلٌ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ

“Ndipo musanene chifukwa chabodza lomwe malirime anu akunena (kuti) “Ichi nchololedwa; ichi ncholetsedwa (popanda umboni).” Kuopera kuti mungampekere bodza Allah. Ndithu, amene akupekera bodza Allah, sangapambane. Ndichisangalalo chochepa (cha m’dziko lapansi chimene chikuwachititsa zimenezo); ndipo iwo adzapata chilango chowawa.” Al-Nahl 116-117

يَا أَيُّهَا النَّاسُ كُلُوا مِمَّا فِي الْأَرْضِ حَلَالًا طَيِّبًا وَلَا تَتَّبِعُوا خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُبِينٌ إِنَّمَا يَأْمُرُكُمْ بِالسُّوءِ وَالْفَحْشَاءِ وَأَنْ تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ

“E inu anthu! Idyani zabwino zimene zili m’nthaka zomwe zili zololedwa; Ndipo musatsate mapazi a satana. Iye kwa inu ndi mdani woonekeratu. Iye akukulamulani kuchita zinthu zoipa ndi zauve. Ndikuti mumnamizire Allah pomunenera zimene simukuzidziwa” Al Baqarah 168-169

Allah Ta’la akuchenjeza akapolo ake mma aayah amenewo pa zakuloleza zinthu zomwe Iye analetsa kapena kuletsa zomwe Iye analoleza, mopanda kuzindikira. Ndipo Allah walongosola kuti kuyankhula kopanda nako ‘ilm ndikoopsa. Allah anachenjeza akapolo ake kuti shaytwaan amawakonda pamene akuyankhula zokhunza Allah mopanda kuzindikira, ndipo amawalamulira kutero nthawi zonse mchipembedzo, mmakhalidwe komanso mmisonkhano yawo.

Zomwe zili zofunika kwa Msilamu aliyense ndiye kupewa kuyankhula zokhunza deen pomwe alibe ‘ilm pazinthuzo, komanso azimuopa Allah ndikuwonesetsa kuti zomwe akuzitchula kuti ndi haram kapena halal zizichokera mu Qur’an kapena Sunnah. Osangoti izi haraam, iziz halal.

Msilamu aliyense apewe kutsatira ma imam osocheretsa, apewe kutsatira zoyankhula mu deen zopanda nazo umboni.

Msilamu yemwe ali ozindikira (ophunzira za Deen), asabise ‘ilm chifukwa chakuopa kuti awasokoneza anthu, chifukwa zomwe akubisazo, kusazidziwa kwa anthu nkomwe kukupangitsa kuti Chipembedzo chizisokonekera. ‘Aalim asawasiye anthu mu umbuli chifukwa choti zomwe akuyenera kuwalongosolerazo n’zachilendo kwa iwo, koma alongosole deen kuti zaumbuli zomwe anazololwera anthuzo asiye. Osawasiyira anthu shirk chifukwa choti anazolowera. Osaopa kuwaphunzitsa anthu haqq chifukwa choti sanazolowere.

Ndikupempha Allah Ta’la apereke chilimbikitso kwa ma ulamaa athu ndi ma sheikh onse, komanso apereke kugonjera mmitima mwa onse omwe akuphunzira deen.