Kodi kuimba ma Nasheed ndikololedwa?
Allah atipatse kuzindikira
**********************
Ma nasheed omwe akuimbidwa mzaka zathu zino, ambiri ndi oletsedwa chifukwa akupezeka kunja kwa malamulo (ma condition) a nyimbo zololedwa omwe anabwera kale.
 
Nasheed ndi yololedwa kuimba kapena kumvera. Koma ikhale yopanda zinthu za haram izi:
 
Asagwiritse ntchito chida chilichonse kuonjezera pa mau a mkamwa.
Subhana-Allah lero akati nasheed, yopanda instrument siikoma. Ma hadith ambiri akuletsa zimenezo koma ife tikudzinjoya. Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanaloleze kupanga da’wah pogwiritsa ntchito zinthu za haraam! Da’wah yopanga pogwiritsa ntchito zomwe zinaletsedwa, imeneyo si da’wah ya ku chiwongoko, koma kuchisokeretso, ngakhale zitamaoneka kuti zikuyenda!
 
Maimbidwe asatengere nyimbo za chikunja
(Ma choir, kapena oimba ena omwe amaimba za haraam). Oimba ena a Chisimu anayamba kuimba chifukwa cha kumveramvera nyimbo zakunja kwa Chisilamu, zoimbidwa ndi okumwa mowa komanso oimba za haram. Anali kukonda kumvera nyimbo zawo za uve zija mpaka kupangidwa influence kuyamba kuimba. Koma poti iwowo ndi Asilamu, anayambitsa akuti “Islamic Music” “Islamic Hip Hop” ndi zina zotero. Islamic?? Allah akuwongoleni ma brothers.
 
Musapezekemo mau kapena nkhani zomusocheretsa Msilamu, kumpititsa ku bid’ah, komanso musaimbe za chipani cha ndale.
Ma Duf. Ndizoletsedwa mwamuna kugwiritsa ntchito chida chirichonse, koma pokhapo sitimamva. Mwamuna ndi oletsewa kugwiritsa ntchito duf. Palibe umboni wololeza kutero koma kuletsa.
 
Mau a akazi asapezeke mu nyimboyo
Subhana-Allah, lero akazi akuimba limodzi ndi anyamata, akuti ‘brother featuring sister…’ komanso atsikana akumatulutsa nyimbo zawo atsikana okhaokha nkumajambulitsa akuvina uku akuimba nyimbo akuti za Chisilamu … ife ndevu pepeya-pepeya kumaonera ndikumvera ndikumanjoya nazo. Allah Ta’la ndiye analetsa mkazi kukweza mawu pagulu. Powayankha anthu amene akutichenjeza ndi ma aayah komanso ma hadith nkumati “tikupindula ndi ulaliki womwe uli mkati mwakemo.” Kodi inu mungamwe mowa chifukwa choti mkati mwakemo muli sugar wa halal?
 
Nyimboyo isakhale ndi uthenga woipa, uthenga wobweretsa fitna, uthenga wonyoza kapena uthenga wabodza monga tinkhani topeka topanda umboni.
Nyimbo zimenezo ndiye nzambirimbiri … akumatenga tinkhani tabodza nkumaimba, akuti kufalitsa uthenga…akufalitsa bodza.
 
Nyimbozo zisampangitse munthu kusiya kuwerenga Qur’an ndi ma Hadith. Zisampangitse kusiya kuphunzira za Deen. Komanso zisampangitse kuchita ulesi pa ibaada chifukwa cha kumvera nyimbozo.
Zachisoni masiku ano anthu akuloweza nyimbo zomwe sizingawathandize padziko pano ngakhale ku Akhira, akumasiya kuloweza Qur’an yomwe idzawapemphere chikhululuko tsiku la Qiyaamah. Munthu kukhala busy kuloweza ma script a nyimbo ndi ndakatulo kuti akajambulitse, agulitse apeze ndalama, koma mmutu ngakhale Surat Al Fatiha mulibemo. Mkati mwa nyimboyo akaikamo liwu loti Muhammadun Rasulullah akulephera kutchula bwinobwino … mmalo mophunzira, akuthamangira kujambulitsa nyimbo kuti adziwasocheretsa anthu nkudzisocheretsa mwiniwake. Akuti kulalikira mu nyimbo,,, ulalikira bwanji za deen munthu ulibe ‘ilm iriyonse kupatula yopeka nyimbo?
 
Kuchuluka kwa nyimbo ndi oimba ma nasheed kukupangitsa kuti anthu asaphunzire Qur’an, asamvere Qur’an.
Ena amanena kuti “mmm nanga munthu ukhalire 24 hours kumvera Qur’an yokhayokha, kumapangako refresh…” Subhaanallah, Allah akuwongoleni ndithu. Inu mukuitenga Qur’an ngati nyimbo zomwe mukumverazo chifukwa cha kusaidziwa. Iphunzireni ndipo simudzatopa kuimvera. Qur’an ukamamvera umapeza thawaab, Ukamawerenga umapeza thawaab 10 pa chilembo chirichonse. Qur’an idzakupulumutsa tsiku la Qiyaamah. Pomwe nyimbo, mumvera mumvetsedwa kukoma basi zathera pompo. Oimbawo sakupatsani kalikonse pokulipirani kuti mwamvera nyimbo. Ena amati ma nasheed oterowo amabweretsa imaan… Dziwani kuti imaan si chinthu choseweretsa. Imene imakufikaniyo si iman koma kungokhunzidwa mumtima chabe.
Imaan ya Allah simabwera pa zinthu za haraam mkati make.
Dziwani kuti kugwira ntchito iriyonse yodzitchingira kapena kuwatchingira ena ku Quran ndi Sunnah, ndi haram.
Phunzirani deen musanayambe kuifalitsa