Kuchokera mu Minhaajul Qaaswideen fi Fadhlil Khulafaai Rraashideen page 187, tidziwa kuti nawo ma Khawaarij amadana ndi ena mwa ma Swahaba.

Khawaarij ndigulu la anthu omwe anali limodzi ndi Ali radhia Allah anhu pa nkhondo zake, koma anamutuluka ndikumuwukira pamene anavomera chigamulo cha pakati pa iye ndi Mu’awiya; iwo sanasangalale ndi chigamulo chapakati pamagulu awiriwa, ndipo anati “chigamulo ncha Allah osati anthu”, kuchokera m’Mawu ake onena kuti:

إِنِ الْحُكْمُ إِلَّا لِلَّهِ

“Ndithu kuweruza kuli kwa Allah” Surah Al-An’aam 57

Ndipo anamupanga Ali ndi Mu’awiya komanso onse omwe anagwirizana ndi chigamulochi, kuti ndi makaafir, chifukwa cha mawu awa:

وَمَنْ لَمْ يَحْكُمْ بِمَا أَنْزَلَ اللَّهُ فَأُولَئِكَ هُمُ الْكَافِرُونَ

“Ndipo yemwe saweruza ndizomwe Allah anatsitsa, oterowo ndi okanira” Surah Al Maaidah 44

Pamene anapatukana ndi gulu la nkhondo la Ali radhia Allah anhu, anasamukira mmudzi wina mu Kufa, wotchedwa Hurooraa, ndipo anatchedwa kuti ma Al Hurooriyya, komanso anatchedwa kuti Al Khawaarij. Al-Milal wa Nnihal (Asshahrastaani) vol.1/114-117.

Kenako dzina ili linasanduka kukhala la aliyense yemwe watuluka ndi kuwukira gulu komanso atsogoleri.

Gulu limeneli, lomwe linasiyana ndi Ali radhia Allah anhu, linali lopanga ibaada kwambiri, komanso lokonda kuwerenga Qur’an, ndipo linali lolimbitsa za Chipembedzo pomwe alibe ilm.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawasimba anthu amenewa komanso anakamba za kupezeka kwawo mwa ife, mu Hadith yomwe anailandira Al Bukhari ndi Muslim.

Mfundo 6 Zomwe Ma Khawaarij Amayankhula Pa Ma Swahaba
Ma Khawaarij amatsimikiza za utsogoleri wa Abu Bakr ndi Umar radhia Allah anhu, ma shaa Allah.
Koma amaona kuti iwo anavutika ndi Uthmaan radhia Allah anhu kumayambiliro kwa utsogoleri wake, kenako anachita zinthu zoyenera kumuchotsa utsogoleri ndi kumpanga kukhala kaafir, mpaka anamupha (monga mmene ndinalongosolera mu nkhani ya “Kodi Uthman anaikidwa kuti?”

Ma Khawaarij amakhulupilira kuti utsogoleri wa Ali radhia Allah anhu unali chisanabwere chigamulo (tahkeem), ndipo amakanira utsogoleri wake kuyambira pambuyo pa chigamulo komanso anamupanga kukhala kaafir, ndipo amawapanga ma kaafir ma judge awiri a chigamulochi, Abu Musa ndi Amru bun Al ‘Aas, komanso amampanga Mu’aawiya kukhala kaafir. Amenewo ndiye ma Khawarij.

Ena mwa iwo amaona kuti kufr yomwe anawapanga Uthman ndi ma judge awiri aja, ndikufr ya shirk, pomwe ena amaona kuti kufr imeneyo inali ni’ma osati shirk. Maqaalaatil Islamiya Lil Ash’ariy vol.1/203, vol.2/141,143

Ma Khawaarij amaona kuti utsogoleri (u Khalifa) akhonza kutenga aliyense osati ma Quraysh okha, bola akhale munthu woyenera. Al Firaq Baynal Firaq pge 55

Sheikhul Islam Ibn Taymiya anati: “ndipo ma Khawarij onse amamupanga Uthman, Ali ndi otsatira awo radhia Allah anhum kuti ndi ma kaafir.” Majmu’l Fatawa vol.13/35