Nkhani ya zithunzi ndi yaitali chifukwa imakhudza mbali zambiri zomwe zimakhala zosiyana zigamulo zake,  monga kukhala zoletsedwa kapena zololedwa kapena kuletsedwa kotheratu, mopanda kupatula komanso kuletsedwa kopatula.
Pali ma aayah a mu Qur’an komanso ma Hadith ambirimbiri amene amakamba za zifaniziro zimene zimapangidwa munjira izi:
a. Zifanizo zosemedwa (mafano/idols)
b. Zifanizo zojambulidwa (photograph)
c. Zifanizo zoseweretsa (ana ngakhale akuluakulu omwe)
d. Kuika mnyumba komanso mma social network
Ndipo ndikukhulupilira kuti mafunso onsewa akuzungulira pamenepa.
Ndiye in sha Allah tidzikamba pang’onopang’ono mpaka pa mapeto.
Ndisanapite patali, tione kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati chani pa nkhaniyi. Kuzera mma hadith omwe ali mmusiwa,  tiona tokha kuti kukhonza ma images (zifaniziro) a zinthu za moyo zokhala ndi mizimu ndi HARAM.  Komanso kuvala, kupachika mnyumba  zifanizo zimenezi ndi HARAM. analoleza kapena analetsa.
Choncho pomaliza tiona izi:
* Cholinga choletserako kapena kulolezako.
* Mtundu ya zifanizirozi (images).
* Zomwe zili zoletsedwa komanso zomwe zili zololedwa.
* Pa mapeto tiona kuti ma ulamaa ena anati chani pa nkhami ya ma images.
“Anthu omwe akalangidwe kwambiri tsiku la Qiyaamah ndi opanga ma image”. Al- Bukhari (5950), Muslim (2109).

“Ndithu amene akumapanga ma image azidzalangidwa tsiku la Qiyaamah ndipo azidzauzidwa kuti “zipatseni moyo zomwe munali kulenga zija”. Al Bukhari (5951), Muslim (2108)

“yemwe amapanga ma image pa dziko pano adzakakamizidwa kuti awuzire mzimu tsiku la qiyaamah, koma sadzakwanitsa kutero ndipo adzapatsidwa chilango cha jahannam” Sharh Sahih Al-Bukhari ‘Fat’hul Baari’ (#5618)

“Angelo samalowa mnyumba momwe muli ma image (a zinthu za moyo monga anthu ndi zinyama) ndi galu” Sahih Muslim 4042

“Jibril (Mngelo wamkulu) ananena kwa Mtumikmi salla Allah alaih wasallam kuti “ndithu ife sitimalowa mnyumba momwe muli agalu ndi zifanizo za zinthu zamoyo” Al Bukhari (5961), Muslim (2107)

Usamah bin Zaid analowa mu ka’bah ndipo anaona Mtumiki, ataona chifanizo cha munthu chitajambulidwa, anaitanitsa ndowa ya madzi ndikumadzithira uku akuyankhula kuti “Allah awalanga anthu awa omwe ANAPANGA zoti sangalenge”. Sunan Al-Tirmidhi vol.3 p.211 #856

“Ali radhia Allah anhu ananena kwa Abi alHiyaji alAsadi kuti: ndikuuze zomwe anandiuza Mtumiki, usasiye chifanizo chilichonse koma USWE komanso manda omwe anyamulidwa kwambiri pokwilira uwachepetse”. Muslim (969)

Amenewa ndi ma hadith a omwe amapanga zifanizo za zinthu zamoyo zokhala ndi mizimu.
Koma omwe amapanga zinthu zopanda  mizimu monga mitengo, mapiri, ma galimoto nyumba ndi zina zotero, palibe vuto lirilonse.
~~~~~~~
Kuchokera mma Hadith amene tamva aja komanso ena ambiri pa nkhani imeneyi, tipeza kuti kupanga images (zifanizo) za zinthu zokhala ndi moyo ndi koletsedwa. Komanso kupachika mnyumba kapena kuvala ndi zoletsedwa.
CHOLINGA CHOLETSERA
Cholinga choletsera zithunzi komanso zosema ndi kupewa kunfananitsa pakati pa zolengedwa za Mulungu, monga mmene tamvera ma hadith aja, akutanthauza kuti anthu amene akumapanga ma image omwe Allah anaikamo mzimu, amenewo akumayerekeza ndi zolengedwa za Mulungu zomwe iwowo sangakwanitse kupitiriza kuti zikhale mmene ziliri zenizeni. Choncho adzakapitiriza tsiku la Qiyamah pamene adzawauza kuti awuzire mzimu, koma adzalephera ndipo akaponyedwa ku moto.
Komanso cholinga china choletsera ndi kupewa kupembedza mafano munthu usakudziwa, komanso kuteteza chikhulupiliro cha bwino chomwe chingaonongeke pambuyo poganizira kwambiri chithunzicho, monga kholo lomwe linamwalira nkulipachika pa khoma kuti tidziona daily polikumbukira, zimatha kulowera kwina kwake mosazindikira, monga mmene kalelo zopembedza mafano zinayambira.
Komanso Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: “anthu amenewo (a nthawi ya Nooh) amati akafa mmodzi wa iwo ochita zabwino, amamanga mzikiti pa manda ake, kenako amajambula ndikumakaika mnyumba zawo. Anthu amenewa ndi omwe adzakhale oipisitsa pamaso pa Mulungu Tsiku la Qiyaamah”
Kuchokera mu Buku la Rawaai’il Bayaan Fi Tafseer Aaayaatil Ahkaam, alongosola chiyambi cha zithunzi ndi mafano, komanso chifukwa chani zili haram…mwachidule pa nkhani ya anthu a Nooh, tidziwe kuti zopanga zithunzi zinachokera pa anthu amenewa ndipo zopembedza mafano zinachokera kumeneko. Zimafano zomwe anayambira kupembedza anthu a Nooh alaih salaam ndi zomwe Allah wadzitchula mu Qur’an Surat Nooh 23 (Wadda, Suwaa, Yaghutha, Ya’uka ndi Nasra), zinali za anthu  oti sankapanga shirk koma anali kupembedza Mulungu Modzi  ndipo anali okhulupilira mu Utumiki wa Nooh alaih Salaam. Atafa anthuwa, anawapangira zithunzi, komanso anawasemera zimafanao kuti adziwakumbukira pa zintchito zawo zabwino zomwe anali kuchita asanamwalire. (mmalo motengera momwe ankachitira eni akewo). Choncho anathu obwera pambuyo pawo anali kubweretsa malemekezedwe oposera anzawo ncholinga chofuna kuoneka kuti iwo ndiolemekeza kuposa ena aja…ndipo anayamba kumapempha madalitso ndi chikhululuko kwa Allah kuzera ma zithunzi ndi mafano aja…
Al Tha’labi anakamba kuchokera kwa Abdullah Ibn Abbas polongosola Aayah ya mu Surat Nooh pamene Allah anati: “Ndipo (olemera) adanena (kwa otsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu: musamusiye Wadda, Suwaa, Yaghutha, Ya’uka ndi Nasra (Maina amafano awo).”  Ndiye anati: mafano amenewa ndi maina a anthu omwe anali kuchita bwino mu gulu ala anthu a Nooh, ndipo atamwalira, kunadza shaytan kwa anthu otsala aja ndipo anawanyengezera kuti akhonze zimafano pa malo awo omwe ankakhala, ndipo adzipatse maina a anthu aja…(monga mmene zimachitikira masiku ano munthu akamwalira amampangira chifano nkuchiimika pa malo ena ake, kapena kutenga chithunzi chake nkuchipachika mnyumba kuti adzimkumbukira…Kamuzu for example). Zimenezo ndi shirk, haram ndipo mayambidwe ake zinayamba choncho kalelo, panopa dziko likutha mudziona tikubwerezanso zomwe zinkachitika kalekale, kuyambiranso. Koyamba sizinkapembedzedwa koma anthu omwe anapanga zimenezowo atatha, omwe anafika pambuyo pawo anayamba kudzipembedza monga mmene ndanenera kale kuti zinali ngati mpikisano.… #end_quote.
TANTHAUZO LA IMAGES NDI MITUNDU YAKE
Ma ulamaa anagawa ma images mmagulu awiri:
Zifanizo zomwe zimakhala ndi zithunzithunzi zopangidwa kuchokera ku gypsum/plaster, copper kapena mwala. Zimenezi ndi ZIMAFANO (IDOLS).
Zifanizo zomwe zilibe zithunzithunzi zojambulidwa pa pepala, kapena kugoba pa khoma kapena zojambulidwa pa carpet, pa mattress kapena pa pillow, ndi zina zonse. Zimenezi ndi ZITHUZI (PICTURES)
Tsopano FANO, ndi chomwe chimati ukachiimika chimatha kukhala ndi chithunzithunzi, kusonyeza kuti chimakhala ngati munthu kapena chinyama.
Ndipo CHITHUNZI, ndi chomwe sichimatheka kuchiimika kotero kuti sichimakhala ndi chithunzithunzi, monga kujambula pa pepala, pa nsalu etc.
Choncho tiona kuti FANO lirilonse limatha kukhala Picture pomwe PICTURE iliyonse siingakhale FANO. chifukwa
Mu Lisanul Arabi (dictionary imeneyo (Arabic-Arabic)), anati FANO ndi picture ndipo chithunzithunzi cha chinthu chilichonse ndi chifanizo chake. FANO ndi dzina la chinthu chomwe chapangidwa pofanizira chomwe chinapangidwa ndi Mulungu.
Tikaonesetsa, tikugwiritsa ntchito liwu loti FANO >>FANIZO>>KUFANIZIRA….Fanizo silingatheke kulipanga popanda chofanizira, choncho zinthuzo zikamakhonzedwa zimakhonzedwa pofanizira zomwe zilipo kale…ndiye ndi zomwe Allah analenga, komwe kuli kulakwitsa.
MAFANO KOMANSO ZITHUNZI ZOMWE ZILI ZOLETSEDWA (ZA HARAM)
FANO  la chinthu chokhala ndi moyo monga munthu, chinyama…zimenezi ndi haram, kuchokera mu Hadith ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam yomwe anati: “ndithu Angelo salowa mnyumba momwe muli galu komanso chithunzi…” galu tikumudziwa. Koma chithunzi apa akutanthauza cha munthu, chinyama (chojambulidwa kapena kusemedwa).
CHITHUNZI chojambulidwa ndi manja pofanizira zinthu zomwe zimakhala ndi mzimu monga anthu ndi nyama – ndi haram, kuchokera mu hadith iyi: “ndithu eni ake a zifanizo izi adzalangidwa tsiku la Qiyaamah ndipo adzauzidwa kuti apereke mizimu ku zomwe analengazo” komanso Hadith iyi: “Yemwe angajambule chithunzi adzalamulidwa kuti awuzire mzimu tsiku la Qiyaamah komabe sadzakwanitsa kutero” ndipo adzaponyedwa ku moto.
CHITHUNZI chikakhala chokwanira bwinobwino kotero changotsalira kuti chikhale ndi mzimu – ndi haram, monga mmene ananenera Mtumiki salla Allah alaih wasallam mu Hadith ija: “…adzalamulidwa kuti awuzire mzimu tsiku la Qiyaamah…”. Komanso mu Hadith ya Aisha radhia Allah anha: ” Mtumiki analowa mnyumba ine nditadziphimba ndi chomwe chinajambulidwa ndipo anakwiya ndikugwira chophimbacho nkung’amba ndip anati: “ndithu anthu omwe adzalangidwe koopsya ndi amene amafanizira zolengedwa za Allah”. Aaisha anati: “ndiye ndinachotsa zigawo zina za chithunzicho kotero kuti sichinakhale chithunzi chokwana.” Kuchokera pamenepa, ma Ulamaa anatengapo umboni woti PHOTO YA CHINYAMA KAPENA MUNTHU IKAKHALA KUTI NDI YOSAKWANIRA KUKHALA CHINTHUCHO, SI HARAM..monga kukhala chopanda chiwalo chomwe chimachititsa kudziwika komanso kusokoneza, monga mutu.
CHITHUNZI chomwe chili choonekera ndipo chili pa malo oti munthu amalemekezedwa nacho kapena kupatulika chifukwa cha chithunzicho, monga malaya ojambula mkango kapena chimbalame kapena china chake chosonyeza kulemekezeka kapena kuopsa kwa yemwe wavalayo, zimenezo ndi haram.
MAFANO NDI ZITHUNZI ZOMWE ZILI ZOLOLEDWA (ZA HALAAL).
ZOSEMA (MAFANO) kapena MA PICTURE (ZOJAMBULA NDI MANJA) zomwe zilibe mizimu monga mwala, mtengo, phiri, nyanja, ndi zina zotero zopanda moyo – ndizololedwa. Ibn Abbas anafunsidwa ndi munthu kuti ine ndikujambula izizi ndiye tandilangizeni kuti deen imati bwanji? Anamuyankha ndi hadith ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo anamuuza kuti: “ngati ukufuna kujambula, jambula mtengo kapena chilichonse chopanda mzimu”.
CHITHUNZI cha chiwalo cha chinthu cha chinthu cha moyo chomwe  sichinalumikizidwe ndi chinthucho, monga mkono, diso khutu ndi zina, kudzijambula pazokha ndikololedwa chifukwa sizili pathupi lomwe lajambulidwanso. Monga hadith ya Aisha ija pamene anadula gawo lina la chithunzi.
ZIDOLE zopangidwa ku zinthu zomwe tadzitchula munthunda muja kuti zimatha kuimitsidwa nkukhala ndi chithunzithunzi – ndi zololezedwa.
KODI NANGA ZIDOLEZI ZINALOLEZEDWA BWANJI KUMACHITA ZIMAKHALA MU CHIFANIZIRO CHA CHINYAMA MONGA MPHAKA, KALULU, GALU etc ZOMWE ZILI ZOLETSEDWA?
Ma Ulamaa analankhulapo pa nkhaniyi kuti ZIDOLE zinalolezedwa pa chifukwa choti atsikana akamakhala nazo zimawathandiza kupanga practice magwiridwe ndi masamalidwe a ana omwe adzakhale nawo akadzakwatiwa. Komanso mwana akakhala yekha, amatha kumacheza nacho ndipo kuchezako kumamchepetsera nthawi yodandaula kapena kuliralira chifukwa cha kusungulumwa, choncho amakula motakasuka. Chimodzimodzinso zomwe zimapangidwa design pa ma sweet komanso mu tizida togwiritsa nthito ana.
Aaisha radhia Allah anha mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam ankamufunsira banja ali wamng’ono anali ndi chidole ndipo anakhala nacho mpaka anakula nkumutenga ngati mkazi wake, chidolecho anali nachobe. Mtumiki anamwalira Aaisha ali ndi zaka 18 ndipo anali nachobe chidole chakecho.
MA ULAMAA  ANATI CHANI POIKIRA NDEMANGA PA NKHANI YA KUJAMBULA
Pali ma ulamaa ena sanagwirizane nazo zoti zithunzi zina ndi zololedwa, pomwe ena anagwirizana nazo.
Al Qaadhi Ibn Al Arabi anati: “ma Hadith onse akuletsa zithunzi, koma kupatula zomwe zili zongolemba pa chovala monga number kapena mtengo ndi zina….komano zimenezi ndi makrooh (zonyansa) chifukwa choti zimatha kusokoneza munthu pa ibadah yake…” ndipo anagwiritsa Hasith ya Aisha yomwe taitchula ija.
Abu Hayyan anati: kujambula mu shariah ndi haram ndipo chilango choopsa chalonjezedwa kwa yense ojambula. Ngakhale ma ulamaa ena apatula zina mwa izo, koma mu hadith ya Sahal bun Haneef: Allah watembelera ojambula, koma Mtumiki sanapatule.
Al Aalusi anati: Zoona zake nzoti kuletsa kwa kujambula zinyama zatunthu sikunali koletsedwa mu shariah ya Sulaiman, koma mu shariah yathuyi. Ndipo palibe kusiyana kuti image ya chinyamayo ndi yojambulidwa ndi manja kapena yosema, kapena chochita kugoba pa mtengo kaya pa khoma kaya pa chiwiya …. zonsezo ndi haram ndipo chilango choopsa chalonjezedwa kwa opanga zimenezi. Choncho lamulo ndi limenelo kuti kujambula, kusema kapena kugoba chinyama china chilichonse ndi haram ndipo palibe kupanga debate pamenepo chifukwa Mtumiki ananeneratu mopanda kupatula.
Al Qurtubi anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anatembelera ojambula ndipo ananena kuti ndithu eni ake a ma image amenewa akalangidwa ku moto ndipo akauzidwa kuti adzipatse mizimu koma akakanika kutero.
Al Imam Al Nawawi anati: zithunzi zimene zikuloledwa ndi za zinthu zomwe zili zopanda zithunzithunzi, zomwe zimatha kupondedwa kapena kugwiritsidwa ntchito monga zojambulidwa pa pillow.
Ibn Al Hajar mu Al Bukhari (Fathul Baari) anati: kujambula koletsedwa ndi komwe zimajambulidwa zinthu zokhala ndi matupi komanso mizimu. Koma ngati chinthucho chajambulidwa mbali ina monga khutu, palibe vuto. Ndipo analoleza zidole za ana.
Buku lomwe nkhanizi zachokera: Rawaai’il Bayaan Fi Tafseer Aaayaatil Ahkaam Yolembedwa ndi Ustaaz Muhammad  Ali AlSaabuni, Ustaaz wa Faculty of Sharia ku Makkati Mukarramah
KODI NANGA ZITHUNZI ZATHU ZOMWE TIKUMASUNGIRA MASIKU ANOZI ZILI PATI?
Ma photograph/photo/picture/pic, zomwe zimajambulidwa  pachifukwa, monga PASSPORT PHOTO, ID PHOTO, DRIVING LICENCE PHOTO, kapena  kujambula zigawenga ncholinga chokachitira umboni ku police, ndi zina zotero – ndi ZOLOLEDWA.
Ma photograph/photo/picture/pic, zomwe zimabweretsa fitna (mayesero) ndipo zotsatira zake zimakhala kumugwetsera munthu ku haram, monga zopereka chikoka mmitima ya ena, zosavala, ndi zina zonse zomwe mukuzidziwa zija, ndi HARAM.
Tsopano zithunzi zomwe zimajambulidwa ngati chikumbutso (remembrance), monga za pomaliza maphunziro (graduation), pa ulendo (trip), kapena kujambulitsa ndi family yako, anzako, ndi zina zonse zomwe zikufana ndi zimenezi, … pali HARAM ndipo pali HALAL, malinga ndi mmene ma Sheikh akuluakulu anaonera.
Sheikh Muhammad bun Ibrahim, Sheikh Nasruddin Al-Albaani komanso Committee yoona za Iftaa (fatwa) ku Saudi motsogozedwa ndi Sheikh Ibn Baaz ndi ma sheikh ena odziwa kufufuza, anati zithunzi ngati zimenezi ndi HARAM chifukwa zithunzi zimenezi palibe chimene chingavute kupanda kukhala nazo. Komanso chifukwa cha ma hadith omwe tawerenga aja, kuti Mtumiki anati chithunzi cha chinthu chomwe chimakhala ndi mzimu ndi HARAM ndipo sanapatule.
Ma Ulamaa ena anatsutsana ndi ma sheikhwa ndipo akuti ndizololedwa ndipo sizikubwera gulu la zithunzi zoletsedwa. Mwa ma Ulamaa amenewa ndi Sayyed Saabiq – mwini buku la Fiqh Sunnah, Sheikh Najeeb AlMutwee’i komanso Sheikh Muhammad Mutawalli Al Sha’rawiy.
Koma pa kusemphana kulikonse mu deen, pamapezeka chinthu chimodzi chogwira chomwe magulu onse amatha kuyendera mopanda kusemphana, chifukwa Chisilamu ndi chokwana ndipo sitingangosiya chithu kuti awa anati haram awa anati halal, koma tikuyenera kupeza zoti tiyendere. Choncho nkhani imeneyi zoona zake zoti chithunzicho chikhale chopanda zomwe zingampangitse munthu kugwera mmayesero kapena kuchimwa kumene.
TANGOKAMBA ZA KUJAMBULITSA. KODI NANGA KUGWIRITSA NTCHITO KWAKE KUDZIKHALA KOTANI??
a. Kuti chithunzi chidzikhala haram kuika mnyumba zinakhala bwanji?
Funso limeneli yankho lake ndikhulupilira mwalipeza mumtundamo.
Kodi nanga kuika mma social network nkololedwa?
Funso limeneli yankho lake likupezeka mu mfundo ya mmwambayo pa “…ZOMWE TIKUMASUNGIRA MASIKU ANOZI…
Koma kumbali ya munthu wamkazi, kuika zithunzi mma social network ndi HARAM popanda kupatula. Chifukwa zimasemphana ndi lamulo la hijab yawo, ngakhale zikhale kuti wavala hijab, koma kungoika pa display kokhako kumachotsa imaan ya hijab mwa iye.  Ndipo amuna amatha kupanga download nkumasungira, komanso amatyha kutaya nthawi yao kumapanga comment mpaka nthawi ya swalat kudutda pomwe mwini wakey akuswali. Zimapangitsanso anthu kuchimwa chifkwa cha ma comment monga kulemba kuti “angel”, Mulungu anatenga nthawi pokulenga, mmene akuteromo kusonyeza kuti waona zomwe zamuchitiktsa mtima wake kunyamuka ndipo wayamba kuganiza zambiri. Zithunzi za atdikana zimapangidwanso download ndi anthu opanga edit nkumadziwgiritsa ntvhito mma maganize a zolaula, ndipo amagwiritsa ntchito dzina loti Muslim Bitches/Sexy muslims/Hot Hijabis ngati title ya magazine. Koma inu simumadziwa chifukwa magazine amaenewa amagulitsidwa kutali. Izi sikuti ndingabweretse umbioni wa hadith koma ndinaona ndekha kunoko zitamuchtikira mtsika wina…komanso wina wa ku India anaika chithunzi chake atavala hijab yokwnanam anamupangira download nkumupanga edit kupezeka kuti ali maliseche ndipo anagwiritsa ntvhito dzina lake la pa facebook popanga introduce photoyo mmagazine. Anthu oterewa akapangapanga zimenezo pic iliyonse imawadyetsa 10 dollars. Nchifukwa chake mkazi akuyenera kupewa kuika zuithunzi pa facebook ngakhale whatsapp.
Nanga zithunzi zoti zili pa calendar nkupachika mnyumba nzololedwa?
Kupachika zithunzi (za pa calendar kapena za pa zokha) pa khoma mnyumba/mu office/mchipinda/mkalasi ndi malo ena – ndi HARAM.  Mwaona kale mumtundamu kuti Angelo samalowa mnyumba momwe muli zithunzi, ndiye ngati angelo salowa, amalowa ndi ma shaytan ndipo nyumba imakhala yopanda madalitso. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati “musapange nyumba zanu kukhala manda” kutanthauza kuti mukuyenera kumachulukitsa kudwali sunna mnyumba mwanu. Tsopano ngati muli zithunzi zomwe zikuletsa angelo kulowa komanso zomwe zili haram, mungaswali bwanji?? Nzomvetda chisoni timaona nyumba ya msilam kapena chipinda chake, wapachika zithunzi za achina 2PAC, Rihanna ndi azinzawo, khoma la pa bedi ya mtsikana zithunzi za chibwezi chake zili thoo, akamagona nkumapanga Bismika Allahuma amootu wa ahya…madalitso abera ndi ndani poti mgero ndiye wamthamangitsa??
Nkhaniyi ikuchokera mu Majmu’ Fataawa Allajnati Al Daaimah, Fatwa No. 125629
KUSUNGA ZITHUNZI MU PHONE, MU CD, MU COMPUTER  .. ETC
Malinga ndi buku la AlFiqh wa Usuuluh, Sheikh Saleh alMunajjad alongosola poyankha funso la masungidwe a zithunzi ndipo malinga ndi mmene tanenera muja, kupachika pena pake ndi haram. Koma ngati muli ndi zithunzizo mu phone kapena mu CD kapena mu computer ndi malo ena okhala ngati amenewa, palibe vuto kusungira chifukwa digital photo siikutenga forma ya photo yomwe yatulutsidwa pa pepala.