Kodi zoona ndi ziti pa nkhani ya kuwerenga zitabu za bid’ah komanso kumvera ma audio a ma Sheikh a bid’ah?
Sizololedwa kwa munthu oyamba kumene kuphunzira, kapena yemwe sakuzindikira mokwanira; kuwerenga zitabu za bid’ah (zitabu zomwe zikukamba zosemphana ndi Qur’an ndi Sunnah, zomwe mkati mwakemo mukupezeka zopeka komanso za shirk. Sizololedwanso kwa anthu amenewa kumvera ma audio awo a anthu a bid’ah. Kupatula yekhayo yemwe ali ozindikira ndipo akuwerenga ncholinga chofuna kuchenjeza ma bid’ah omwe akupezeka mzitabumo kapena mma audiomo.
Tsopano ongoyamba kumene kuphunzira, komanso yemwe sakuzindikira (awa ndi anthu oti sangathe kusiyanitsa pakati pa bid’ah ndi sunnah), kapenanso omwe amangowerenga pofuna kudziwa zinthu basi osati pofuna kuchenjeza ena ndikulongosola kuopsa kwake; anthu amenewa sakuloledwa kuwerenga zitabu zimenezi chifukwa zikhonza kuwabweretsa chikaiko mumtima ndikuwatembenuza mosavuta, mapeto ake kuyamba kudziikira kumbuyo zomwe akuwerengazo.
Sizololedwa kuwerenga zitabu za anthu a bid’ah kupatula yemwe ali ndi kuzindikira pofuna kuchenjeza anthu ena za mabuku amenwewo. Chimodzimodzinso ma audio.
Ma Ulamaa oyambilira komanso akumapeto kuno akhala akutichenjeza kuti tipewe anthu opeka zinthu mu deen, omwe amayendera maganizo awo:
Abu Al Qilaabah: “Musakhale ndi munthu wa bid’ah … chifukwa adzakumiritsani muchisokeretso chake kapena kukusokonezani mitu pa zoona zomwe mukudziwa kale.” Al Bida’u wa Nnahyu ‘anha, Al I’tiswaam.
Ibrahim Al Nakha’i: “Musakhale ndi munthu wa bid’ah ndipo musamuyankhule, chifukwa ine ndikuopa kuti mitima yanu ingabwelere kusiya njira yowongoka” Al Bida’u wa Nnahyu ‘anha, Al I’tiswaam
Abu Qilaabah: “E iwe Ayyub (Assikhtiyaani), usamvere anthu a bid’ah” Al Laalakani (1/134)
Al Fudhail bun ‘Iyaadh: “Ukakumana ndi wa bid’ah panjira, sintha njirayo ndipo utenge ina”. Al Ibaanah 2/475
Abu Zur’ah atafunsidwa za Al Haarith bun Asad Al Muhasibi ndi zitabu zake, anayankha kuti: “Zitalikire zitabu za munthu ameneyo; ndithu zitabu zimenezo ndi za bid’ah komanso zadzadza ndi zisocheretso. Tenga kuchokera mma hadith”. Ofunsa uja anati: “Komatu muzitabu zimenezi muli maphunziro abwino…” iye anati: “(mmenemo ndi momwe) anthu amafulumilira kutenga ma bid’ah” Al Tahdheeb (2/117), Tarikh Baghdad (8/215). 
Tingotchulapo ma imaa ochepa mwa ambiriwo.
Mmenemo ndimomwe Msilamu okhulupilira Qur’an ndi Sunnah amayenera kuchitira ndi anthu a bid’ah pa zitabu zawo komanso ma ulaliki awo فإن شقشقة الكلام في الأشرطة أخطر akutero kuti chifukwa kusokosera kwawo mma audio ndikomwe kuli koopsa kwambiri kuposa zolemba zawo.
Aliyense yemwe amachita bid’ah ndikumadziwa kuti akuchitayo ndi bid’ah, ali mchitsime chamatope ndipo tisamusekelere.
Ndipo aliyense adzipempha Allah kuti amutalikitse ku bid’ah
الأجوبة المفيدة عن أسئلة المناهج الجديدة س48 ص125