Mu gawo lapita lija taona Nisaab ya ndalama komaso ndalama zomwe umafunika kupereka ngati ndalama zokwana pa Nisaab zazungulira chaka.

Mmene tinaonela muja, Nisaab imapezeka kuti ndi MK 221,000 potengera nisaab ya siliva. Zomwe zimaonetsa kuti anthu ambiri tili mu gulu la anthu oti tipereke zakaat koma sitimadziwa.

Tilipo ambiri omwe ma business athu tikupangira mipamba yoposa pa Nisaab ya ndalamayo. Ma business’wo ndiye tinayambira kale koma zakaat sitimapereka poganiza kuti ndizopereka omwe akuyendera magalimoto odula okhaokha komanso za okhawo ali ndi zima shop zikulu zikulu.

Alhamadulillah lero tazindikira kuti zinthu sizili mmene timaganizira ayi, chofunika apa kuti tizikumbukira nchakuti Zakaat iyi ndi compulsory ndithu zoti osapanga wapeza machimo.

Tinanena mmbuyomu kuti Allah anati pomulamula Mtumiki

خذ من أموالهم صدقة تطهرهم وتزكيهم بها

Tenga mu chuma chawo Swadaqah (chopeleka) kuti uwayeletse ndi kuwatsuka nacho…. Surah At-Taubah verse 103

Tiuzane apa kuti yemwe chuma chake chakwana mlingo ndi nyengo ya Zakaat koma sanapereke, ameneyo akudya ndalama zina zoti sizake.

Munjira ina, akudya chuma cha Haraam chomwe sakufunika kuti achidye.

Tidziweso kuti munthu ameneyo amakhala osayera komanso chuma chakecho chimakhala chosayera.

Pambuyo pa zimenezi tiyeni tione mfundo zina zingapo zokhudza Zakaat ya ndalama zimenezo ndipo tidzidziika ngati mafuso ndikumawafotokoza:

1. Kodi ndingamapange bwanji kuti Zakaat yanga ndisamaphonye ndipo ndizipeleka mwadongosolo?

Yankho:

Chofunikila Msilamu amene wapeza chuma chokwana nisaab kapena kuposera apo, wachipeza chumacho ndipo pali kuthekera koti ndi chokhanzikika, akuyenera achipange record pena pake polemba.

Chisilamu chathu chimalimbikitsa kulemba nkhani ya ndalama ndalamayi kaya ngongole kaye even munthu wasungitsidwa chuma cha masiye. Zimalimbikitsidwa kuti alembe komaso anthu awili achitilepo umboni.

Chimodzi modzi yemwe wapeza chuma chambili choti chikukwana nisaab alembe

Mwachitsanzo

Ndili ndi ndalama zokwana MK 300,000 pa 15 Muharram, 1440.

Kulemba kumeneko kuthandiza kuti azidziwa azayambila bwanji kuwelengela zakaat.

Kodi ndikapeza chumacho ndikuyenela kuyika niyyah yapadela kumayambiliro kwa chaka kuti ndapeza ndalama yomwe ndikufuna kuzapeleka Zakaat?

Yankho

Ayi palibe kuika niyyah yapadela kumayambiliro kwa chaka. Kungolemba ndi kusunga mlingo wa chuma chako kumayambikiro kwa chaka zikuwanila pa zinthu zokonzekela kupeleka Zakaat

Kumayambiliro kwa chaka ndinali ndi ndalama zokwana Nisaab ya zakaat kenako chaka chisanathe ndalama zija zapunguka, olo Kapena value ya siliva yakwela ine ndipo ndalama zanga zikuchepela kodi ndipelekebe zakaat?

Yankho

Ayi apo palibe kupeleka Zakaat tinanena mamam Aishah ananena monveka bwino kuti

لا زكاة في مال حتى يحول عليه الحول

 رواه ابن ماجة

Palibe Zakaat pa chuma mpaka chaka chizungulire

Nde apo zikuoneka kuti chaka sichinathe ndekut apo si papelekedwe zakaat.

Kumayambiliro kwa chaka ndinali ndi ndalama yokwana Nisaab bwino bwino mpaka mmene chaka chikutha ndalama sinasinthe koma Value ya siliva yakwela kodi ndipelekebe zakaat?

Yankho

Tiziwe kuti Nisaab simasintha imakhla fixed (paja tinati ukumatengela value ya golide ndi siliva) . Koma kuti ndi ndalama zomwe zimasintha ndizomwe zimakhala zachuluka Kapena kuchepa.

Now ngati value ya ndalama yatsika Kwambiri ndekutu usapeleke zakaat bas Nisaab sikukwana. Koma ngati zasiyana pang’ono ndi mwina 1 to 2 thousand apo utha kupeleka Zakaat mu ndalama yo (remember tinati mtengo sumakhala exact)

nanga munthu yemwe amalandila pamwezi apange bwanji

Yankho

Tinanena mmbuyomu kuti Zakaat ndalama zimafunika zizungulire chaka ngati sizinazungulire palibe Zakaat.

Ndalama ya salary imakhala ya pamwezi nde olo utaipeza yopitilira Nisaab palibe kupeleka Zakaat unless ngati umasevako nde yosevayo yakwana nisaab ndikuzungulira chaka ili yokwana

Munthu umakhala ndi ndalama zambili zodutsa Nisaab koma sumadziwa kuti ukuyenela kupeleka Zakaat nde waona kuti ndalam zako pa Nisaab zinafika kalekale kodi ungapeleke zakaat pompo?

Yankho

Ayi usapeleke pompo koma kuti pempha chikhululuko kwa Allah pa zakaat zomwe samapeleka kenako yamba kupanga record chaka chako cha tsopano chikazatha uzapeleke zakaat