(Olemba: Ibn Muwahhid)
Chuma chomwe timapelekera Zakaat tutha kuchigawa patatu. 1. Ndalama 2. Katundu 3. Za ulimi Tiyamba kuona gulu lilironse bwinobwino kuti ndiziti zomwe ziperekedwe mmagawo amenewa 1. Ndalama Ndalama zomwe munthu uli nazo zimayenera kuperekedwa Zakaat koma potengera mlingo wa golide ndi siliva. Izi zili choncho chifukwa choti ndalama monga timaidziwira lero, poyambilirapo imakhala value ya golide ndi siliva. Nthawi ya Mtumiki ndalama yawo yomwe amayendera amaitcha dinar ndi dirham Masiku ano pali maiko ena omwe amagwiritsa ntchito maina amenewa pa ndalama yawo monga dziko la Kuwait (dinar). Koma kuti ma dinar a nthawi ya Mtumiki ndi pano ndi osiyana; a nthawi ya Mtumiki amakhala ma silver ndithu kapena golide ndithu. Pomwe za masiku ano imangokhala dzina chabe. Ndiye tikalowa bwinobwino tiona kuti ndalama amawelengera bwanji Zakaat ndipo kuno kwathu ku Malawi tayenera kupereka makwacha angati. Pa nkhani ya ndalama zomwe zili golide ndi siliva, Allah wanena kuti:

وَالَّذِينَ يَكْنِزُونَ الذَّهَبَ وَالْفِضَّةَ وَلَا يُنفِقُونَهَا فِي سَبِيلِ اللَّهِ فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

Omwe akusungila golide ndi siliva nkusamapereka mu njila ya Allah asangalatseni ndi chilango chowawa. Surah At-Taubah, Verse 34 Umenewu ndi umboni woti Zakaat iperekedwe pa ndalama zomwe zimatenga value ya golide ndi siliva. 2. Katundu Katundu yemwe munthu ali naye akuyenereka kupereka Zakaat pa condition yoti katunduyo akhale wa business. Katundu yemwe ukugwiritsa ntchito pa umoyo wako, ameneyo ayi, koma yekhayo yemwe ukupangira business. Pali mau awa omwe anayankhula Samrah

كان رسول الله صلى الله عليه وسلم يأمرنا أن نخرج الصدقة من الذي نعده للبيع – رواه أبو داود بسند ضعيف

Akuti mtumiki amatilamula kuti Zakaat tizipeleka pa zomwe timagulitsa Vuti ndiloti mauwa chain chake ndi chofooka, koma tawabweretsa apa chifukwa pali ma Hadeeth owona omwe akuikira kumbuyo zimenezi, mwachitsanzo mtumiki ananena kuti

‏ ﻟَﻴْﺲَ ﻋَﻠَﻰ ﺍﻟﻤُﺴْﻠِﻢِ ﻓِﻲ ﻓَﺮَﺳِﻪِ ﻭَﻏُﻼَﻣِﻪِ : ﺻَﺪَﻗَﺔٌ ‏- رواه ﻣﺴﻠﻢ ‏

Palibe kupeleka Zakaat kwa nsilamu pa chokwela chomwe amakwela kapena nyamata wake (kapolo)* Zimenezi zikuonetsadi kuti Zakaat isaperekedwe pa zinthu zomwe munthu akugwiritsa ntchito, koma zomwe akupangira business poti nkomwe kuli profit. Note: Zimenezi zoti upereke Zakaat pa za business zokha ziri pa katundu pokhapa osati pa ndalama. Apa tikutanthauza kuti ndalama even usazipangire business koma ngati ziri zokwana mlingo ndipo zakwana nthawi yake, uperekebe Zakaat. Umboni wa mawu amenewa tikuupeza pa hadeeth yomwe timakambilanako mmbuyomu Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti:

ابتعوا بأموال اليتامى لا تأكلها الصدقة – رواه الدارقطني، وله شاهد في الموطى للمالك

Pangilani business chuma cha ana amisiye kuopela kuti chingathe kudyedwa ndi zakaat Umboni wina ndiwoti mayi athu UmmU Salamah anavala chibangiri cha golide ndikumufusa Mtumiki ngati nkoyenera kupereka Zakaat pa golide ameneyo, ndipo Mtumiki anati:

ما بلغ أن يزكي فزكي – رواه أبو داود

Chomwe chafika pa mlingo oti upereke Zakaat basi wayenera kupereka Zitsanzo za katundu yemwe tiyenela kupeleka Zakaat kumalawi kuno
  • Ma nyumba ndi malo a rent
  • Ma galimoto a business komanso a hire (hayala)
  • Makina ndi katundu yemwe timabweleketsa nkumalipilitsa
  • Akatundu omwe timagulitsa
  • Inshaallah tizakamba bwino kapelekedwe ka zakaat pa zimenezi
3. Za ulimi Za ulimi kumbali ya Zakaat tizigawenso pawiri: A) Mbewu B) Ziweto (zifuyo) A) Mbuwu Allah wayankhula mu Quran kuti:

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَنفِقُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا كَسَبْتُمْ وَمِمَّا أَخْرَجْنَا لَكُم مِّنَ الْأَرْضِ

Oh inu anthu okhulupilila perekani chopereka mu zabwino zomwe mwapeza komanso zomwe takutulutsirani mu nthaka. –  Surah Al-Baqara, Verse 267 Pa verse lina Allah atafotokoza kuti ndibiye yemwe anatipatsa zomwela anazati

وَآتُوا حَقَّهُ يَوْمَ حَصَادِهِ وَلَا تُسْرِفُوا إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُسْرِفِينَ

Pelekani gawo lake la chopeleka tsiku lokolora ndipo musaononge ndithu Allah sakonda oononga – Surah Al-Anaam, verse 141 In shaa Allah pamenepa tizalongosolaso kuti ndi zomera ziti zomwe tiyenera kupereka Zakaat komaso mlingo wake. Tisanachoke apa tinene kuti pa verse iyi ya Surah Al Baqarah (267) pomwe Allah akuti Takutulutsilani mu nthaka Ma Ulamaa ena ananena kuti migodi komanso uchi omwe umapangidwa mmapiri ndi njuchi komanso chuma chokumbidwa pansi choti chinakwilirika tayenera kupereka Zakaat. Tidzakambaso zimenezo in shaa Allah mongodutsa poti kwathu kuno sizili zodziwika. B) Ziweto Ziweto zomwe ziyenera kuperekedwa Zakaat ndi zomwe anthu timaweta komanso za miyendo inayi izi: 1. Ngamira 2. Ng’ombe 3. Mbuzi ndi  Nkhosa Mutha kuona kuti ziweto zake ndi zakudya zokhazokha. Nyama zina zosakhala zimenezi zomwe timaweta ngati nkhuku, abakha kaya nkhanga, palibe Zakaat. Ngakhalenso zitakhaka za miyendo inayi ngati Abulu Agwape etc, palibe Zakaat pokhapokha ngati ziri zogulitsa. In shaa Allah tidzakamba bwinobwino pamenepa za kaperekedwe kake. Koma ife tidzangokamba za Ng’ombe, Mbuzi ndi Nkhosa basi.

Gawo Lotsatira (Likubwera in sha Allah)