(Olemba: Ibn Muwahhid)
Monga tinakambila mu gawo loyamba muja kuti Zakaat simangopelekedwa kwa aliyense koma pali anthu special omwe ali pa list yolandira zakaat. Allah anaikiratu list limenelo motere:

إِنَّمَا الصَّدَقَاتُ لِلْفُقَرَاءِ وَالْمَسَاكِينِ وَالْعَامِلِينَ عَلَيْهَا وَالْمُؤَلَّفَةِ قُلُوبُهُمْ وَفِي الرِّقَابِ وَالْغَارِمِينَ وَفِي سَبِيلِ اللَّهِ وَابْنِ السَّبِيلِ فَرِيضَةً مِّنَ اللَّهِ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ

Ndithu chopeleka (Zakaat) chipelekedwe kwa 1. Amphawi (fuqaraa)  2. Osauka (masaakeen)  3. Oigwilira ntchito  4. Anthu ofewa mitima  5. Akapolo ofuna kumasulidwa  6. Angongole  7. Oyenda mu njira ya Allah  8. Anthu a munjira, chikakamizo kuchokera kwa Allah ndipo Allah ndi odziwa komanso wanzeru. Surah At-Taubah, Verse 60 List limenelo ndilomwe limatchedwa kuti أصناف الثمانية Magulu 8. Ndipo okhawa ndamene akufunika alandire zakaat. Choncho tikakhala tikuliwona gulu lilironse palonkha 1 & 2)  – Amphawi ndi Osawuka Magulu awili awa tiwakambira limodzi chifukwa ndi ofananirako. Pa Chichewa chathu umphawi ndi kusauka ndi chimodzimodzi. Koma ku Arabic akati ma fuqaraa amasiyanako ndi ma miskeen. Ngakhale kusiyana kwake kusali kwakukulu koma kulipo ndithu. Ma ulama akuti: Akati faqeer yomwe ndi singular ya fuqaraa, akuti awa ndi anthu omwe ali osawuka kwambiri koti mpaka amasowa chakudya cha patsiku ndipo amavutika kuchipeza. Pomwe akati miskeen yomwe ndi singular ya masaakeen awa ndi osawuka koma awa ndi abolaniko kusiyana ndi oyambawo. Amenewa ngakhale kuti amakhala zina ali nazo komabe amakhala kuti ali ndi zofunika zambiri zomwe akusowekera. Ma ulama afotokozaso kuti ma fuqaraa ndi amene ali ma main target a zakaat. Izi zili choncho chifukwa ma hadeeth ena pokamba zogawa zakaat amangotchila ma fuqaraa basi Mtumiki akumutumiza Muadh ibn Jabal ku Yemen pankhani ya zakaat anati:

تؤخذ من أغنيائهم وترد علي فقرائهم …  رواه البخاري

Chumacho chitengedwe kwa olemela awo ndipo chibwezedwe kwa osawuka awo… Chinaso chomwe tikumva pa hadeeth ya Muadh imeneyi ndichakuti osauka akukambidwa apa ndi a chisilamu osati azipembedzo zina ayi. Chifukwa mtumiki wanena kut *Olemela awo* komanso *osauka awo* kusonyeza kuti asilamu okhaokha Ndiye kut munthu oti si Msilamu koma osauka chabe sakulowa mu gulu ili Fuso nkumati.. Osaukawa alandire mlingo ochuluka bwanji? Ma ulama afotokoza kuti alandire mokwanila ndi mmene zofuna zawo zilili komaso malingana ndi kuchuluka kwa zakaat zapezekazo. Zimenezi ziwapangitse kuti iwo asakhake opemphapempha komaso kangachepe athe kumazitukula pang’ono pang’ono. Wallahu A’lam. 3) Oigwilira ntchito Tisanawafotokoze awa tidziwe kuti ndizotheka zakaat munthu kungotenga wekha nkupeleka kwa anthu oti alandirewa ngati wawapeza. Koma nthawi zina poti kuwapeza anthu oti alandire kumavuta chisilamu chimaikaso ndondomeko yoti anthu ena azitolera zakaat nkumazisonkhanitsa then ndikumawapatsa osauka and mmenemo ndi momwe zimakhalira mu boma la chisilamu. Tsopano ngati pali anthu special omwe aikidwa kuti azitolera zakaat amenewo ayenela kuoatsidwa gawo mu zakaat mo ngati salary. Koma ngati apatsidwa kale salary ndekuti salandilaso gawo la zakaat. Izo zili choncho chifukwa chiti awa amapatsidwa gawoli ngati malipiro pa ntchito yawo yotolera osati ngati kuti akufunikira ayi. Tidziwenso kuti anthu oigwilira ntchito zakaat wa alandire ndithu malipiro awo posaona kuti ndi olemera kaya osawuka. 4) Anthu ofewa mitima Mwachidule ndamasulira kuti anthu ofewa mitima. Koma mawu a mu Quran mmene abwelera literally a kutanthauza kuti omwe mitima yawo ikufewetsedwa Ma ulama atanthauza mau amenewa kut awa ndi anthu oti, pakuwapatsa zakaat zioangitsa kuti mitima yawo ifewe. Ndipo awagawa mmagawo atatu awa A) Anthu omwe sali asilamu koma akuonetsa kuti mitima yawo ikuoendekera ku chisilamu ndipo atati apatsidwa Zakaat ndekuti mosakaika monse alowa chisilamu. Chitsanzo cha apa chitha kukhala omwe akufuna kulowa chisilamu koma mavuto a zachuma akuwabweza mmbuyom. Komanso ena oti mukawapatsa zakaat basi alowa chisilamu ndi mtima onse. B) Anthu omwe sali asilamu oti mukawapatsa zakaat mitima yawo idekha ndipo akhala owachitila zabwino asilamu. Chitsanzo cha bwino chingakhale anthu omwe sali omwe ali ndi mphanvu zopatsa vuto asilamu ngati sapezapo kanthu. C) Anthu omwe ali asilamu ndipo akapatsidwa zakaat zipititsa patsogolo usilamu wawo Example yabwino Kwambiri ndi anthu akumachinga aja amatuluka chisilamu chifukwa chokopeka ndi zopeleka za makafir aja. Komaso apa pakulowa kuwapatsa asilamu kuti tokope anthu owazungulira kui awone ubwino wa chisilamu. NOTE: Mtsogoleri wa asilamu ndamene akuyenela kupanga decide ngati gulu ili lilandile zakaat chifukwa nthawi zina gulu ili silifunika kulandira Monga mu nthawi wa Umar, uthmaan komaso Alie anthu awa anasiya kupatsidwa zakaat – Al bayhaqee. 5) Akapolo omwe akufuna kumasulidwa Apa sitikamba zambili chifukwa akapolo kulibe nde paja tinati format yathu tipanga target ummah wachimalawi. 6) Angongole Apa akulowa angongole a magawo awili Oyamba wa ngongole amene wakongola ndalama payekha ulu ali nsilamu nde zavuta ndipo akukanika kubweza Ndipo wangongole wachiwili ndamene wazigwetsela mu ngongole kamba koti ayanjanitse anthu Qabisah yemwe anazigwetsela mu ngongole kut ayanjanitse anthu anakanena kwa mtumiki za situation yake ndipo mtumiki anati

أقم حتى تأتيا الصدقة فنأمر لك بها –  رواه مسلم

Dikila kaye mpaka pomwe tilandire zakaat ndipo tilamula kuti ulandilepo. 7) Oyenda mu njila ya Allah Ma ulama ambili atanthauza kut apa akukamba za anthu omwe akumenya nkhondo jihad yovomelezeka mu chisilamu Ngat mmene Allah wanenela kuti

وقاتلوا في سبيل الله

Menyelani nkhondo mu njira ya Allah – Surah Al Baqarah verse 190 Koma ma ulama ena amaonjezera kuti apa akulowaso anthu ena omwe akugwila ntchito mu njila ya Allah ngati ofuna maphunziro ndi ena otero. 8) Anthu amunjira Apa ma ulama akuti zikuimila anthu asilamu omwe ali pa ulendo zinthu zawavuta ndipo sangathe kupitiliza ulendo wawo kamba ka chuma Ibn Abbas ndi ma ulama ena anati munthu yu apatsidwe chithandizo choti mpaka chikamufikitse kwawo.

Pitani gawo lotsatira