(Olemba: Ibn Muwahhid)

1. Anthu omwe ali oyenela kupeleka Zakaat

2. Anthu omwe akuyenela kulandila Zakaat.

Monga tinafotokozera pa tanthauzo pa Zakaat lija (mutha kuona gawo loyambilira) zinaonetselatu kuti si munthu aliyense amene angapeleke zakaat ayi.

Zakaat ndi ibaadah, ndiye sangapange aliyense, komaso kuonjezera apo Zakaat ili ndi malamulo ake posiyanitsa ndi Swadaqah. Choncho monveka bwino titha kunena kuti:

Zakaat ndi yokakamizidwa kupereka kwa Msilamu, wammuna kaya wamkazi, mwana kaya wamkulu oti wafikila Nisaab komanso chuma chake chazungula chaka*

Mu ma qualities omwe takambawo tiyamba kuphwanya imodzi imodzi malingana ndi mmene Qur’an komaso ma Hadeeth akutiphunzitsira:

Msilamu

Monga takambira kuti Zakaat ndi ibaadah, kutanthauza kuti ndi mwambo wa Chipembedzo. Ndiye mwambo wa Chipembedzo cha Chisilamu samapanga munthu wamba koma Msilamu basi

Akapanga ibaadah munthu wamba asali Msilamu, ibaadahyo silandiridwa

Allah akuti

وَمَنْ أَرَادَ الْآخِرَةَ وَسَعَى لَهَا سَعْيَهَا وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَئِكَ كَانَ سَعْيُهُم مَّشْكُورًا

Koma amene akufuna (kukalipidwa) moyo winawo nagwila ntchito yake (yoti akalioidweyo) uku ali okhulupilila, okhawo ndiomwe ntchito yawo ikathokozedwe (ikalipidwe) Surah Al-Isra, Verse 19

Moti tikafuna kugawa uthewa wa chisilamu kwa osakhulupilira tisawauze kuti apeleke zakaat kaye, koma tiwauze akhulupilire kaye kenako akakhulupilira kenako nkumazawauza za zakaat mu nthawi yake.

Wammuna kaya wankazi

Pankhani ya kapembedzedwe chisilamu sichimasiyanitsa pakati pa amuna ndi akazi kupatula zokhazo zomwe Allah ndi Mtumiki watiuza kuti izi apange awa okha

Allah akuti

وَمَن يَعْمَلْ مِنَ الصَّالِحَاتِ مِن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَى وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَئِكَ يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ وَلَا يُظْلَمُونَ نَقِيرًا

Ndipo yemwe ati agwile ntchito yabwino kaya wammuna kaya wankazi uku ali okhulupilila amenewa azalowa ku jannah ndipo sazapondelezedwa even pang’ono Surah An-Nisa, Verse 124

Pankhani yopereka specifically Allah ananena kuti

… والمتصدقين وَالْمُتَصَدِّقَاتِ…أَعَدَّ اللَّهُ لَهُم مَّغْفِرَةً وَأَجْرًا عَظِيمًا

… Opeleka chopeleka achimuna ndi achikazi… Allah wawakonzera chikhululuko ndi malipiro akulu Surah Al-Ahzab, Verse 35

Kupita ngati off-topic pang’ono anthu ena amaona ngati azimayi akuyenela kumapeleka zakaat.

Koma si choncho ayi nzimayi ayenela kupeleka Zakaat ngati akukwaniritsa zomwe tikambe apazi

Mtumiki anawauza azimayi kuti

يامعشر النساء تصدفن ، فإني رأيتكن أكثر أهل النار  رواه البخاري

Inu azimayi! Muzipeleka chopeleka chifukwa ndinakuonani kuti ambili a inu akalowa ku moto

Mwana kaya wankulu

Ku Chisilamu ma ibaadah ambili amafunika kuti ochitayo akhale wamkulu okhwima nzeru, izi ndi monga swalah, kusala ndi zina. Koma Zakaat mwanaso amayenera apeleke. Mtumiki ananena kuti

ابتعوا بأموال اليتامى لا تأكلها الصدقة رواه الدارقطني وله شاهد في الموطى للمالك

Pangilani business chuma cha ana amisiye kuopela kuti chingathe kudyedwa ndi zakaat

Kuchokera mu Hadeeth imeneyi tikunva kuti ngakhale chuma cha mwana ndiye kuti payenela kuchotsedwapo ndalama ya zakaat ngati chili chofika mlingo. Nchifukwa chake Mtumiki akulangiza osunga chuma cha ana kuti azichipangila business. Otherwise akapanda kutero kuchotsa zakaat kutha kupungula kwambiri chumacho mpaka mwina kutha.

Nisaab

Nisaab (النصاب) ndi mlingo wachuma oti chuma chikafika pamenepo chiyambe kaperekedwa Zakaat.

Nisaab imasiyana malingana ndi mtundu wa chuma ndipo tikhala tikuona bwino za nisaab kutsogoloko in shaa Allah

Chuma chomwe sichinafike pa Nisaab zakaat sikuyenereka kuperekedwa. Mmalo mwake mwini wakeyo angopereka Swadaqah wamba basi

Kuzungulira chaka

Mtumiki anati

من استفاد مالاً فلا زكاة عليه حتى يحول علىه الحول عند ربه رواه الترمذي  وصححه الألباني

Munthu amene wapeza chuma palibe kupereka Zakaat kwa iye mpaka chitazungulira chaka pamaso pa mbuye wake

Chaka pa nkhani ya Zakaat chimawerengedwa kudzera mu calendar ya chisilamu yoyendela mwezi yotha miyezi 12

Munthu akapeza chuma chokwanira Nisaab adikire mpaka chithe chaka kuchokera tsiku lomwe anachipezalo mpamene adzalamulidwe kupereka Zakaat. Koma ngati chaka sichinathe, palibe Zakaat. 

Zimenezi ndizomwe zikuyenera kuti zikhalepo kuti Zakaat iperekedwe.

Pitani Gawo Lotsatira