(Olemba: Ibn Muwahhid)

Mavuto omwe alipo kwa munthu yemwe sapereka zakaat, komanso wina mwa maubwino omwe alipo popereka zakaat

Monga mmene tamveramo, zikuonekeratu kuti kumbali ya chuma anthu tagawanikana pawiri:

1. Anthu opeleka
2. Anthu osapeleka.

Pali mau a Mtumiki salla Allah alaih wasallam awa omwe atilonjelere magulu a anthu awili amenewa, Mtumiki wathu salla Allah alaih wasallam anati:

ﻣَﺎ ﻣِﻦْ ﻳَﻮْﻡٍ ﻳُﺼْﺒِﺢُ ﺍﻟْﻌِﺒَﺎﺩُ ﻓِﻴﻪِ ﺇِﻻَّ ﻣَﻠَﻜَﺎﻥِ ﻳَﻨْﺰِﻻَﻥِ ﻓَﻴَﻘُﻮﻝُ ﺃَﺣَﺪُﻫُﻤَﺎ ﺍﻟﻠَّﻬُﻢَّ ﺃَﻋْﻂِ ﻣُﻨْﻔِﻘًﺎ ﺧَﻠَﻔًﺎ ، ﻭَﻳَﻘُﻮﻝُ ﺍﻵﺧَﺮُ : ﺍﻟﻠَّﻬُﻢَّ ﺃَﻋْﻂِ ﻣُﻤْﺴِﻜًﺎ ﺗَﻠَﻔﺎً ‏

رواه البخاري

Palibe tsiku lirilonse lomwe akapolo a Allah kumawachela kungopatula kuti angelo awili amatsika, ndipo mmodzi wa iwo amati: “Oh Allah mpatseni amene akupeleka kupitilira kwa chuma”. Ndipo winayo amati: “Oh Allah mpatseni yemwe sakupeleka kuonongeka kwa chuma”

Maduwa amenewa amachitika tsiku lirilonse, ndipo opemphawo ndiye ndi Angelo omwe ali omuopa Allah ndipo palibe kufunsa kuti ma duawa amayankhidwa kapena ayi. Omana yembekezerani zimenezo ndipo opereka sangalalani.

Pambuyo poti alandira ma dua oipawa, kenako Allah akunena kwa anthu omana kuti

ِ… وَالَّذِينَ يَكْنِزُونَ الذَّهَبَ وَالْفِضَّةَ وَلَا يُنفِقُونَهَا فِي سَبِيلِ اللَّهِ فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

Ndipo anthu amene akusungira golide ndi siliva (chuma) nkusamachipereka mu njira ya Allah; asangalatseni ndi chilango chowawa. Surah At-Taubah, Verse 34

Kodi chilango chowawa chake chidzakhala chotani??

Allah akupitiliza kuti

يَوْمَ يُحْمَى عَلَيْهَا فِي نَارِ جَهَنَّمَ فَتُكْوَى بِهَا جِبَاهُهُمْ وَجُنُوبُهُمْ وَظُهُورُهُمْ هذَا مَا كَنَزْتُمْ لِأَنفُسِكُمْ فَذُوقُوا مَا كُنتُمْ تَكْنِزُونَ

Tsiku (la Qiyaamah) limene chumacho chidzatenthetsedwe kenako azidzaotchedwa nacho pa mphumi, munthiti komaso mmisana mwawo (uku akuuzidwa kuti) zimenezi ndi zija munkasungira zija. Talawani zomwe munkasungira zija. Surah At-Taubah, Verse 35

Chimenechi ndi chilango special chimene Allah anasunga kwa anthu osapeleka zakaat. Koma sizokhazo ayi

Allah akunenaso kuti

وَلَا يَحْسَبَنَّ الَّذِينَ يَبْخَلُونَ بِمَا آتَاهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ هُوَ خَيْرًا لَّهُم بَلْ هُوَ شَرٌّ لَّهُمْ سَيُطَوَّقُونَ مَا بَخِلُوا بِهِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ..

Anthu omwe akupanga umbombo pa zomwe Allah wawapatsa mu ubwino wake asaganize kuti nzabwino kwa iwo, ayi koma nzoipa kwa iwo, azakolekedwa nazo pakhosi zomwe amapanga nazo umbombozo pa Qiyaamah. Surah Aal-e-Imran, Verse 180

Chuma chikasinthidwa ndikukhala ngati goli ndikuikidwa pa khosi pa anthu a umbombo kuti azikavutika nacho. Uku akudikira kukaotchedwa nacho

Chinthu chinaso chowawa kwambiri chikachitika kwa anthu omana Zakaat pa Qiyaamah. Tanvani mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam anayankhulira za anthu omana omwe azikaotchedwa pa Qiyaamah ndi chuma chawo:

… كلما بردت أعيدت له في يوم كان مقداره خمسين ألف حتي يقضى بين العباد فيرى سبيله إما إلى الجنة وإما إلى النار  رواه مسلم

(Chuma chomwe azikatenthedwa nachocho) chizikati chikazizila chizikatenthetsedwaso kachikena kuyambilaso kuotchedwa nacho, zimenezi zikachitika kwa nthawi yotalika zaka 50,000. Akakhala akuotchedwabe mpaka judgment ikathe pakati pa akapolo a Allah kenako mpomwe akaone njira yake kuti akalowa ku moto kapena ku jannah

Hadeeth ili mu Muslim. Ziwophyerenji zokhoma zokumana nazo anthu osapereka Zakaat

Allah atiteteze tiyambe kupeleka

Sitingamalize kukamba za kuopsa kosapereka Zakaat tisanakambe hadeeth iyi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam yomwe imadetsa nkhawa ukailingalira mofatsa:

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anafotokoza kuti

مَنْ آتَاهُ اللَّهُ مَالاً، فَلَمْ يُؤَدِّ زَكَاتَهُ مُثِّلَ لَهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ شُجَاعًا أَقْرَعَ، لَهُ زَبِيبَتَانِ، يُطَوَّقُهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ، ثُمَّ يَأْخُذُ بِلِهْزِمَتَيْهِ ـ يَعْنِي شِدْقَيْهِ ـ ثُمَّ يَقُولُ أَنَا مَالُكَ، أَنَا كَنْزُكَ.. رواه البخاري

Munthu amene Allah wamupatsa chuma nkusamapeleka zakaat, chumacho chidzasandutsidwa chinjoka chachimuna chadanzi chiri ndi madontho akuda mmwamba ma maso, chinjoka chimenecho chiczamukulunga pakhosi ndikumamuluma mmatsaya kwinaku chikuyankhula kuti “ndine chuma chako umasunga chija”…

Tangoganizani chinjoka chamaonekedwe otere chikukupanga zimenezo ndipo palibe okulanditsa komanso ulibe kothawira.

Komanso chinjokacho chiziyankhula kuti udziwe kuti sichili pamenepo by chance. Ndizosakhala bwino

Tiyeni timalize  gawo ili poona ubwino omwe ali nawo opereka zakaat.

Kupatula kupangiridwa dua ndi Angelo mmawa uliwonse kuti chuma chako chitetezeke, Mtumiki salla Allah alaih wasallam watchula zinthu zingapo zokoma kwa munthu opereka zakaat… Taonani ma hadeeth awa:

Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti

ما نقص مال من صدقة  … رواه مسلم

Chuma sichimapunguka chifukwa cha kupereka chopereka

Moti munthu asaope kuti ndikapereka ndisauka, ayi. Mukuyankhula kwina Mttumiki salla Allah alaih wasallam anati:

يا إبن آدم أنفق تنفق عليك  … جامع الصحيح لسيوطي و صححه الألباني

Iwe munthu, pereka chopereka, ine (Allah) ndizakupatsa iweo

Zimenezi zabwino za padziko panotu. Sizodabwitsa kuona nthawi zambiri anthu opereka Zakaat ndi omweso amachita bwino kwambiri pa nkhani ya chuma.

Zaosadabwitsa ndi mmene wakambila Mtumiki salla Allah alaih wasallam apa, tiyeni tione za kumwamba:

Mtumiki akufotokoza mu Hadeeth yokoma kuimva iyi kuti

‏”‏ مَنْ تَصَدَّقَ بِعَدْلِ تَمْرَةٍ مِنْ كَسْبٍ طَيِّبٍ ـ وَلاَ يَقْبَلُ اللَّهُ إِلاَّ الطَّيِّبَ ـ وَإِنَّ اللَّهَ يَتَقَبَّلُهَا بِيَمِينِهِ، ثُمَّ يُرَبِّيهَا لِصَاحِبِهِ كَمَا يُرَبِّي أَحَدُكُمْ فَلُوَّهُ حَتَّى تَكُونَ مِثْلَ الْجَبَلِ ‏” … رواه البخاري 

‏‏Yemwe angapereke chopereka cholinana ndi tende choti wachipeza mu njira ya bwino – chifukwa Allah amalandira zabwino zokhazokha – Allah amachilandira choperekacho ndi dzanja lake la manja (right) kenako amachiweta (chopereka chija) kumuwetera mwini wake ngati mmene mmodzi wa inu amawetera mwana wa hatchi mpaka chimakula ngati phiri

Kameneko kopereka kuchepa ngati tende, kodi nanga kwa omwe akapereka zambiri ngati Zakaat, zimakhala motani??

Zabwino za kupereka zilipo zambiri koma tilekeze pamenepa kaye.

Pamenepo ndi pamtsiriziro pa chiyambi cha kudziwa za Zakaat, ndipo tikuyamba ysopano zambiri zomwe tikuyenera kudziwa

Pitani tsamba lotsatira