3. Position (status) ya Zakaat mu chisilamu
Kodi Zakaat ili ndi gawo lanji mu Chisilamu?
Kodi munthu ukapeleka Zakaat uzidzinva kuti wakwaniritsa gawo lanji? nanga ukasiya udziti waphwanya lamulo lanji?
Kumbukirani kuti tinanena kuti Asilamu ena samapeleka Zakaat chifukwa choti samadziwa kufunikila kwa Zakaat, ndipo amatenga Zakaat ngati chinthu wamba choti olo kuchisiya palibe vuto kweni kweni ayi. Koma nkhani si choncho.
Tiyambe ndi kuona hadeeth iyi yomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam analongosola kuti:
بُنِيَ الْإِسْلَامُ عَلَى خَمْسٍ: شَهَادَةِ أَنْ لَا إلَهَ إلَّا اللَّهُ وَأَنَّ مُحَمَّدًا رَسُولُ اللَّهِ، وَإِقَامِ الصَّلَاةِ، وَإِيتَاءِ الزَّكَاةِ…
رواه البخاري ومسلم
Chisilamu chamangidwa pa nsichi zisanu 5
1. Kuikila umboni kuti oyenela kupembedzedwa mu choona ndi Allah ndipo Muhammad ndi mtumiki wake
2. Kuimika mapemphero (Swalah)
3. Kupeleka Zakaat …
Hadeeth imapitilira pamenepo koma ife tilekeza pamenepo.. anailandila Al Bukhari ndi Muslim.
Mau oti Nsichi kapena kuti zipilala, Mtumiki sanatchule mau amenewa mu Arabic yake mu hadeeth imeneyi, koma anangoti Chisilamu chamangidwa pa 5, ndipo potengera kuti pa nsichi kapena nsanamila mpomwe chinthu chimamangidwa, ma Ulama amamasulira choncho mmene taneneramo.
Pa hadeeth imeneyo munthu utha kuona kut Zakaat si chinthu wamba mu Chisilamu ayi, koma kuti ndi chinthu chomwe chamanga Chisilamu. Munjira ina Zakaat ikagwa, Chisilamu chizakhala ngati building yopendekera mbali imodzi.
Allah akamayankhula mu Qur’an zolimbikitsa kupemphera samalepera kukakambaso zoti anthu apereke zakaat. Allah amanena kuti
وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ….
Imikani mapemphero komaso pelekani zakaat
Ndipo ndi ma verse ochuluka kwambiri zedi omwe Allah amanena kanenedwe kake kameneka.
Tidziwe ndithu kuti pali gulu lina la ma Ulama a Chisilamu omwe ali pa ganizo lonena kuti munthu osanena Shahada ndikumaswali koma nkumakana kupereka Zakaat, ndiye kuti iweyo ndiwe kafir oyenela kukuthira nkhondo. Iwo amagwiritsa ntchito ndime izi za mu Qur’an Yolemekezeka:
Allah amafotokoza mu Qur’an pa nkhani ya anthu ma mushrikeen omwe anaphwanya pangano lawo la (Hudaybiyah) ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti
 فَإِن تَابُوا وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَآتَوُا الزَّكَاةَ فَإِخْوَانُكُمْ فِي الدِّينِ…
*Ngati iwo angalape nayamba kuswali komanso kupeleka Zakaat ndekut akhala abale anu mu chipembedzo*….
Surah At-Taubah, Verse 11
Api tikamva mosemphana,(mafhoom mukhaalaf) tiwona kuti omwe alapa ndikuswali koma osamapeleka Zakaat ndekut sitili limodzi mu deenimu. Nchifukwa chaketu gulu la ma Ulama limeneli linati kusiya Zakaat popanda chifukwa ndiwe kafir
Ma ulama amenewa amapereka umboninso wa Abu Bakr Swiddeeq radhia Allah anhu, atalowa pa udindo wa u Khalifa Asilamu ena anati ife tipitilira kukhala Asilamu koma kuti Zakaat zokha sitizipeleka. Abu Bakr anati
لأقاتلن من فرق بين الصلاة والزكاة…
Ndimenyana nkhondo ndi aliyense amene asiyanitse pakati pa Swalah ndi zakaat
Ma swahaba ena anayesa kukamba naye Abu Bakr kut asinthe maganizo koma sanalore ndipo mpaka enawo anagonjera ku maganizo ake.
Zimenezi zikutisonyeza kuti Zakaat si chinthu choseweletsa mu Chisilamu mwathumu. Ndipo aliyense amene akuchita chibwana pa nkhani ya Zakaat adziwe kuti akuchita phada ndi Usilamu wake.
Kodi munthu amene akunyozera kupereka Zakaat koma oti atha kukwanitsa ayembekezele zotani kwa Allah?