Kuyamikidwa ndi kwa Allah ndipo mtendere ndi madalitso zikhale pa Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam,,,amma ba’d Mukuona kwanga ndapeza kuti chiwelengero cha Asilamu ambiri sakumapereka Zakaat kuno ku Malawi. Ndipo izi sichifukwa choti anthuwo sangakwanitse ayi, koma pa zifukwa zitatu izi:

  1. Asilamu ambiri aku Malawi timaona ngati zakaat ndi chinthu chovuta kwambiri koti anthu oti apereke ndi Asilamu olemera kwambiri zedi. Ndiye timapezeka tikupeza chuma chokwanira kupereka Zakaah, kumangopereka ma Sadaqah wamba basi kumaona ngati popereka Zakaat sitinafike.
  2. Asilamu ambili aku Malawi sitidziwa kufunikira kwa Zakaat. Timaona ngati Zakaat siyofunika kwambiri ngati mmene iliri Swalah kapena Swaum. Sitimadziwa kuti Zakaat ndi nsichi ndithu ya Chisilamu ngati mmene ziliri Swalah ndi Swaum.
  3. Asilamu ambiri aku Malawi sitimadziwa malamulo a Zakaat mmene timadziwira za nsichi zinazi ngati Swalah ndi Swaum. Nawoso ma Sheikh athu (Allah awadalitse) samatikambira kwambiri nkhani zokhudza kaperekedwe ka Zakaat; amangotiuza za chopereka in general koma osati tsatanetsatane wa Zakaat.

Zifukwa zitatu zimenezi kuchotsapo (umbombo ndi kusakwanitsa) ndi zomwe Asilamu aku Malawi sakumapelekera Zakaat kwambiri, ndipo akapereka akumangopereka swadaqah yomwe penanso ikumakhala yoposa mlingo wawo pa Zakaat. Kupanga Sunnah kusiya Faradh! Choncho ndakubweretserani phunziro la Zakaat (FIQH ZAKAT), ndipo sindipanga target Zakaat yonse ayi, koma ndipanga target Zakaat pa level ya anthu aku Malawi kuno basi. Apo ndikutanthauza zinthu zoti ku Malawi kulibeko sindizikhunza ayi, koma zingokhala za ku Malawi kokha kuno, kuti tifulumire kuimvesetsa Zakaat mantha atichoke, In shaa Allah

  1. Kodi Zakaat ndi chani?
  2. Kusiyana kwa Zakaat ndi swadaqah
  3. Position (status) ya Zakaat mu chisilamu
1. Kodi Zakaat ndi chani
Mau oti Zakaat – الزكاة pa chilankhulo cha Arabic chabe amatanthauza matanthauzo angapo monga
Kuchulutsa 
Kuyeletsa
Kapena kukuza chinthu
Mu Quran mau oti Zakaat agwilitsidwa ntchito kwambiri pa chiyankhulo ngati kuziyeretsa, Mwachitsanzo Allah anati
قد أفلح من تزكي
Wapambana amene waziyeletsa Surah Al A’la verse 14
Pa verse limeneli maw awo oti kuziyeletsa, Allah wagwilitsa ntchito Arabic yoti TAZAKKAPomwe tikabwera ku malamulo a chisilamu (Shariah), mau oti Zakaat ali ndi katanthauzidwe kosiyaniranako ndi pa chiyankhulopa. 
Ku shariah Zakaat imatanthuza chopereka chokakamiza chomwe munthu ayenera kupereka mu nthawi yoikika, mu mtundu wa chuma oikika, komaso pa mlingo okhazikika.
Tikamapitiliza mmusimu ma lessons akubwelawa tizakhala tikuphwanya tanthauzo limeneli kuona kuti gawo lirilonse likutanthauzanji.
Malingana ndi ma ulamaa a Chisilamu a history kalekale chopereka sichinali chokakamiza komanso choikika ayi; aliyense amapereka mmene wafunira komanso panthawi yomwe akukwanitsa. Izi zinakhala zikuyenda kufikira pomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anasamuka kupita ku Madina ndikutha zaka ziwiri.
Mu chaka cha chiwiri chimenecho mpomwe Allah anapanga Zakaat kukhala chikakamizo. Allah wanena mu Qur’an Yolemekezeka kuti
… خذ من أموالهم صدقة
Tenga kuchokera mu chuma chawo Swadaqah chopeleka … Surah Attawbah verse 103
Uku kunali kulamula tsopano kuti chopeleka chikhake chokakamiza. 
Koma zodzabwitsa ndizoti Allah choperekacho akuchitchula kuti Swadaqah, koma matengedwe ake akukhala olamula.
Kodi Swadaqah iripo ina yokakamiza ngati Zakaat?
Mpomwe tikufika pa mfundo yathu yachiwiri yoti:
2. Kusiyana kwa Zakaat ndi Swadaqah
Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa zinthu ziwiri zimenezi ku Chisilamu?
Msilamu aliyense akuyenera kudziwa (tikhake tcheru) kuti ku Chisilamu kwathuku chopereka chagawidwa pawiri motere:
a. Swadaqah. 
b. Zakaat.
a. Swadaqah ndi chopereka in general chosakhanzikika mlingo kapena nthawi, kapenaso mtundu wa chopereka.
Imeneyi nde swadaqah, moti generally speaking, titha kunena kuti Zakaat ndi mtundu umodzi wa Swadaqah.
Icho nchifukwa chake Qur’an pajapa yatchula chopereka chokakamiza kuti Swadaqah mmalo mwa Zakaat.
Mtumiki salla Allah alaih wasalam anagwiritsapo ntchito kanenedwe kameneko pomwe ankamutumiza ophunzira wake Muadh ibn Jabal ku Yemen kukafalitsa Chisilamu.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
…. فأخبرهم أن الله قد فرض عليهم صدقة…
رواه البخاري
Ukawauze kuti Allah wakakamiza kwa iwo kupereka chopeleka
Apo Mtumiki salla Allah alaih wasallam akukamba za chopereka chokakamiza koma wagwiritsa ntchito kayankhulidwe koti “Zakaat”.
Pamenepa tikutha kuona kuti Zakaat ndi mtundu umodzi wa Swadaqah. Swadaqah ili general pomwe Zakaat ili ya specific
Titha kunenanaso kuti:
Zakaat iliyonse ndi Swadaqah koma sikuti Swadaqah iliyonse ndi Zakaat
Ndikhulupilira taona kusiyana kwake, ndipo zimveke bwino ndi chitsanzo ichi:
Munthu anadzamupempha Haroon zakudya ndipo Haroon wamutapira mulu wathochi nampatsa
Muchitsanzochi munthu anabwera pa nthawi yake kudzapempha, ndipo operekayo wangopereka mulingo uliwonse; sanasankhe mtundu wa chopereka.
Ndiye kuti apo tiyamike wapereka Swadaqah osati Zakaat
a. Zakaat imakhala ndi malamulo ochulukira makamaka kumbali ya
  • Nthawi yopereka
  • Mlingo 
  • Mtundu wa zopereka
Popanda zimenezi ndiye kuti siikhala Zakaat, koma ikhaka swadaqah
Pa Zakaat sitipereka chitsanzo chifukwa ndipomwe tikhake tikukambirana bwino bwino kutsogoloku in shaa Allah.
3. Position (status) ya Zakaat mu chisilamu
Kodi Zakaat ili ndi gawo lanji mu Chisilamu?
Kodi munthu ukapereka Zakaat uzidzimva kuti wakwaniritsa gawo lanji? nanga ukasiya udziti waphwanya lamulo lanji?
Pitani mu gawo lachiwiri kuti tipitirize in sha Allah Tili ndi magawo 17 mu phunziro la Zakaat
……………
……………