Mugawo ili tilongosola zinthu izi:

1. Zakaat ya ulimi

2. Mbuzi zomwe ziyenera kuperekedwa Zakaat

Pambuyo poti tamaliza kuona zakaat ya ndalama komanso ya business ndipo takamba bwinobwino ndi maumboni komanso zitsanzo za kaperekedwe kake, tiyeni tipitirize gawo lina la Zakaat ya ulimi.

Zakaat ya ulimi

Pamene timapanga introduction ya chuma chomwe tiyenera kupereka Zakaat, tinatchula za ulimi kuti kumenekonso kuli zakaat.

Tidziwe kuti ulimi umagawidwa pawiri

A) ulimi wa ziweto
B) ulimi wa mbewu

Magawo awiri onsewa ayenera kuperekedwa Zakaat motsata ndondomeko yomwe abwana anaphunzitsa.

Tinakambaso mu gawo la m’buyomu kuti ziweto zomwe tiyenera kupereka Zakaat zili m’magawo atatu:

1. Mbuzi
2. Ng’ombe ndi
3. Ngamila

Mukukamba kwanga za Zakaat ya ziweto, ndipanga target mbuzi, nkhosa ndi ng’ombe poti ndizomwe zikupezeka mochuluka ku Malawi.

Zakaat ya mbuzi ndi nkhosa

Pa Arabic mbuzi zili ndi maina angapo koma limodzi mwa omwe amatchuka amati Shaat (شاة) ikakhala imodzi, ndipo Shiyaah (شياه) zikakhalapo zingapo.

Nazo nkhosa zili ndi maina angapo ndipo lotchuka amati Kabsh (كبش).

Komano anzathu a Chiluya mbuzi ndi nkhosa amaziika gulu limodzi lomwe amalitcha Al Ghanam (الغنم). Kwa iwo akatchula mau amenewa amaphatikiza ziwili zonsezi.

Mbuzi/nkhosa zomwe tikuperekela Zakaat zikhale kuti zikukwanira ma condition awa:

1. Mbuzizo zikhale kuti zikuwetedwa kuti ziziberekana kapena kuti zizitulutsa mkaka. Mbuzi zomwe ziri za business sizikuyenera kuperekedwa Zakaat ngati tinakambira muja.

2. Zikhale zoti akumakazidyetsera ku malo odyera osati akumachita kuzigulira zakudya ayi.

Pamene Mtumiki anali kukamba za mtundu wa mbuzi anati:

في صدقة الغنم في سائمتها… 📚 رواه أبو داود

Ndipo pa zakaat ya mbuzi/nkhosa zomwe zikumadyetsedwela kumalo odyetseledwa zipelekedwe motere …

Hadeeth imeneyi Abu Bakr analongosola mu kalata yomwe anamulembera Anas Bun Maalik pa nkhani ya Zakaat mmene iyeyo anamvera kwa Mtumiki

Ndipo pa nkhani ya mbuzi umo ndi mmene anakambira.

Nisaab ya Zakaat ya mbuzi

Mbuzi zoweta ziperekedwe Zakaat pamene mlingo wake zafika 40

Abu Bakr mu kalata yake ija anati

فإذا كانت سائمته الرجل ناقصة عن أربعين فلا شاة شاة واحدة فلا شيء فيها إلا إن شاء ربها – 📚 رواه البخاري

Ngati mbuzi/nkhosa zomwe zikumadyetsedwera kumalo odyetseredwa ziri zopelewera pa 40 ndi mbuzi/nkhosa imodzi, ndiye kuti palibe kupereka Zakaat mpaka mwini wake afune (kuti ikhale sadaqah)

Kuchokera mu Hadeeth imeneyi ma Ulama anena kuti mbuzi/nkhosa ziperekedwe pokhapokha ngati zakwana 40. Ngati zikuwetedwa koma sizinafike pa 40 kapena zili pa 39, palibe Zakaat pamenepo. Koma zikafika 40 nkumachulukira, ndiye kuti mwini wake azipereka mbuzi imodzi pakutha pa chaka chirichonse mpaka pomwe zidzafike 120 … zikazafika pamenepo maperekedwe a Zakaat adzasintha.

Kodi maperekedwe adzasintha motani? Nanga zidzapitilira motani?

Gawo 12