Kapelekedwe ka Zakaat ya ndalama.

  1. Kodi Nisaab ya ndalama ndi zingati?
  2. Chaka chimazungulira bwanji pa Zakaat za ndalama?
  3. Ndi ndalama zingati zomwe umapeleka pa ndalama yomwe ulinayo?

Tinalongosola mu chigawo chapita kuti Zakaat ya ndalama imachokera pa golide komaso siliva

Tatiyeni lero tione mwa tsatanetsatane kuti zimachokera pati

Gawo Loyamba: Golide

Mama athu okondedwa Aisha Allah akondwe nawo anati:

إنه كان يأخذ من كل عشرين مثقالا نصف مثقال – رواه إبن ماجة

Iye anali kutenga pa 20 mithqaal iliyonse ½ (half) ya mithqaal

1 mithqaal imapanga pafupifupi 4.25 grams ya golide. Ndiye kuti tipeze 20 mithqaal mma grams, tipanga

20 X 4.25 = 85grams

Imeneyo ndiye nisaab ya golide.

Ndiye kuti, kuti tipeze Nisaab ya ndalama potengela golide tipeze kuti

Kodi 85grams ya golide ndi makwacha angati?

Makwacha tipeze pamenepo ndiye mulingo oyambira kupereka Zakaat malingana ndi golide

Gawo Lachiwiri: Siliva

Abu Saeed Al Khudriyy anati mtumiki anati:

وليس فيما دون خمس أواق صدقة – رواه البخاري

Palibe kupeleka Zakaat pa siliva ochepela pa 5 awaq

5 awaq imapanga pafupifupi 595 to 640 grams ya siliva; ndiye ife tingotenga 640 grams

Ndiye kuti tipeze kuti 640 grams ndi makwacha angati

Ndalama tipezeyo nde poyambila kupeleka Zakaat ya ndalama malingana ndi Siliva

Note: Ma grams tikuika apa ndikumati pafupifupi chifukwa chonena kut anthu amaika ma grams osiyanasiyana potengera kuti ndizovuta kupeza value imodzi yokhazikika.

Anthu kale analibe ma scale oyezela ngati masiku ano ndiye zoyeza zawo zimakhala zosiyanako pang’ono. Koma ma value ndaikawo ali mu range yokhanzikika ndipo ngosakaikitsa ndithu.

VUTO LIMABWELA APA TSOPANO

Kale nthawi ya Mtumiki 20 mithqaal ya golide yomwe tati ndi 85grams value yake inali yofanana ndi 5 awaq ya siliva yomwe tati ndi 640 grams.

Ndipo umatha kugulira chinthu chofanana ma siliva anali ma dirham ndipo ma golide anali ma dinar just as kwacha ndi tambala.

Koma chifukwa cha kupita kwa nthawi zinthu zinasintha; value ya golide inakwera kwambiri kuposa siliva

Moti lero 85 grams ya golide = MK 3,000,000 (pafupifupi)

Pomwe 640 grams ya siliva = MK 221, 000

Choncho ma Ulamaa anasephana maganizo kuti kodi tizigwiritsa ntchito Nisaab ya golide Kapena ya siliva.

Alipo ena mwa iwo omwe anati tizitenga ya golide ndipo anatchula zifukwa zawo. Mbali inayi aliponso omwe anatchula kut tizitenga ya siliva ndipo anatchula zifukwa zawo.

Nkhani ndiyoti onse amagwiritsa ntchito ijtihaad (kulimbikira kwawo) monga mmene mwamvera mmene zinthu zinakhalira.

Sitingakambe bwinobwino maganizo a ma Ulamawo mwatsatanetsatane, koma panopa titenga kudzera value ya Siliva chifukwa ndi minimum ya value ya ndalama yomwe ikutchulidwa. Ndiye to be on a safe side bola kutenga imeneyo. Koma yemwe angatengere value ya golide sikuti walakwa, iyo ndi ijtihaad yake.

NDIYE MUNTHU AMENE ALI NDI NDALAMA YOKWANA MK221, 000 ATCHELE KHUTU:

Tilowe limodzi gawo lachiwiri lomwe ndi kutha chaka (Al hawl)

Tinanena kale m’banjamo kuti Mtumiki anati

من استفاد مالاً فلا زكاة عليه حتى يحول علىه الحول عند ربه  – رواه الترمذي وصححه الألباني

Munthu yemwe wapeza chuma palibe kupeleka Zakaat kwa iye mpaka chitazungulira chaka pamaso pa mbuye wake

Kuzungulira kwa chaka uku timawelengetsera chaka cha Chisilamu choyendera mwezi. Ndiye kuti ngati MK221,000 unayipeza pa 11 Muharram chaka chino ndipo sinapunguke mpaka chaka cha mawa pa 11 Muharram, uchotsepo ndalama ya zakaat.

Kenako ndalama yazungulira chaka atengepo ndalama zingati zoti apeleke ngati zakaat? Apa Mtumiki anati

في الرقة ربع العشر – رواه البخاري

Pa mlingo wa siliva ipelekedwe ¼/0.25 (quota ya 10)

Qouta ya 10 kuti tiike mma percentage ndiye kuti

0.25÷10 × 100

= 2.5%

Ndiye kuti pa ndalama yokwana Nisaab ija 221000 ikatha chaka achotsapo 2.5%

Chitsanzo:

Funso: Ahmad ali ndi ndalama zokwana MK500,000 zomwe wakhala nazo kuchokera chaka chatha, Kodi apeleke zakaat ndalama zingati?

Yankho: Ndalama zokwana 500,000 ndiye kuti zapitilira pa Nisaab kutengera value ya siliva. Ndipo ngati wakhala nayo kuchoka chaka chatha ndiye kuti yazungulira chaka (hawl). Pamenepo ndiye kuti akuyenera achotsepo 2.5% ndipo ayipelekere Zakaat motere:

2.5% × 500000 = 12500

Ndiye kuti Ahmad adzatenga MK12,500 pa MK500,000 yomwe yazungulira chaka ndikupereka Zakaat.

Ndikudziwa kuti kwa ambirife kuti tiwatsate masamuwo zitha kufunika kuti tikhale pa class yomveka bwino koma chophweka kusunga nchakuti: pa ndalama yomwe yakwana MK221,000 ndipo yazungulira chaka, tizitengapo 2.5% ndikupeleka Zakaat.

Note; Ndalama iyo 221,000 imasintha malingana ndi mmene mitengo ya siliva ikusinthilra pa msika ku Malawi kuno, mutha kumaona magazine ya Al-Haqq amapanga update mtengo wa siliva wa Nisaab mwezi ulionse.

Gawo Lotsatira