In shaa Allah tiona za kaperekedwe ka Zakaat pa business yopanga rent katundu monga nyumba magalimoto komanso malo.

Mugawo lomwe lapita tinakamba za kaperekedwe ka Zakaat pa ma business omwe tinawatchula kuti business wamba.

Komanso business yomagulitsa ma galimoto, malo komanso nyumba. Ndipo mwachidule tinati

Zakaat iperekedwe pa capital komanso ma profit omwe akwana Nisaab komanso kuzungulira chaka.

Ndipo tinapereka zitsanzo.

Lero tisanapite ku gawo lomwe tinasiya lija ndimafuna tinvane kaye

Kutsogoloku tikamba za Zakaat ya ziweto komanso mbewu za ulimi In shaa Allah, ndipo limenelo lizakhala gawo lapadera la alimi a ziweto ndi mbewu

Koma pali anthu ena omwe si alimi koma amagulitsa ndi kugula mbewu komanso ziweto

Kodi amenewa ali gawo liti? La alimi kapena a business?

Yankho ndilonema kuti

Anthu amenewa akuwerengedwa ngati a business osati alimi, ndipo kaperekedwe kawo ka Zakaat kadzatengera mmene akupelekera a business, komapeleka Zakaat pa capital komanso profit yomwe yazungulira chaka komanso yafika pa Nisaab.

Ndipo Nisaab yawo awerengere Nisaab ya ndalama osati ya ziweto ndi mbewu ayi.

Tsopano tibwere ku gawo lathu la lero.

Kapelekedwe ka zakaat pa ma nyumba, malo, galimoto ndi katundu wina wa rent

Apa choyamba choti timve ndichoti munthu yemwe tamutchulayu sakugulitsa katundu, koma kuti akupangitsa rent basi.

Ndiye kuti business ya munthu ameneyu ndiyopereka ma service basi ndipo ndalama akulandira iyeyu ndiya kugwiritsa ntchito anthu akugwiritsa katundu wakeyo.

Tsopano potengera mau a Mtumiki aja oti:

ليس ﻋَﻠَﻰ ﺍﻟﻤُﺴْﻠِﻢِ ﻓِﻲ ﻓَﺮَﺳِﻪِ ﻭَﻏُﻼَﻣِﻪِ : ﺻَﺪَﻗَﺔٌ ‏- 📚 رواه ﻣﺴﻠﻢ

Palibe kupereka Zakaat kwa Msilamu pa chokwera chomwe amakwera kapena nyamata wake (kapolo)

Ma Ulamaa akuti Zakaat ya munthu ameneyu sapereka pa assets (katundu yemwe ali nayeyo, monga nyumba, malo kapena galimoto lopangitsa rent lo ayi) koma azipereka Zakaat pa ma profit omwe akupeza kuma service omwe a kupanga offer wo.

Ndiye tiona zitsanzo zitatu zomwe zitithandize kumvetsa bwino mmene Zakaat ya gawo limeneli imaperekedwera pamenepa

Chitsanzo 1

Ahmad ali ndi nyumba ya yomwe anayuza 3.5 million kuimanga ndipo akumapangitsa rent ndikumalandila 30,000 pa mwezi.

Ndalama yomwe amalandila ku rent yo samasunga ndipo simatheka kuzungulira chaka kodi apeleke bwanji zakaat?

Yankho

Apo palibe kupeleka Zakaat chifukwa Zakaat ikufunika iperekedwe pa ndalama ya rent yo ngati ikukwana Nisaab ikazungulira chaka zomwe apa sizikuchitika

Ndiy ekuti Ahmad sapereka Zakaat pamenepa.

Chitsanzo 2

Ahmad ali ndi ma Mazda Bongo atatu omwe anagula 10 million pakamodzi, omwe amatchukumila. Ndipo kuyambira mu Sha’baan chaka chatha akumasevako ma profit omwe amapezeka ku business yakeyo ndipo 350,000 yazungulira chaka.

Kodi apereke bwanji zakaat?

Yankho

350,000 yomwe amaseva kuma profit ndiyomwe ayenera kupereka Zakaat motere:

350,000 ×2.5%
= MK 8,750

Ndiye kuti imeneyo ndi ndalama yomwe Ahmad apereke Zakaat

Pitani ku Zakaat (11)