Yusha alaih salaam anali chidzukulu chachikulu cha Mneneri Musa alaih salaam. Anali ndi agogo akewo pa ulendo waukulu wochokera mu Egypt.

Musa alaih salaam anali kumkonda mzukulu wakeyu kotero anampatsa ntchito zofunikira zambiri. Anayenda mu chipululu kwa zaka zokwana 40.

Pamene Mneneri Musa anamwalira, Mneneri Yusha alaih salaam analowammalo mwa utsogoleri wa kwa Israel.

Anayenda masiku ochuluka mpaka anafika mbali mwa mtsinje wa Yorodani.

Yusha alaih salaam anatsogolera anthu ndipo anawoloka mtsinje mpaka kufika mumzinda wa Yeriko. Yeriko unali mzinda wokongola ndi nyumba zitalizitali komanso makoma akuluakulu. Anthu a mumzindawu anali akulu matupi ndi amphamvu. Koma atsogoleri awo anali oipa, komanso achinyengo kwambiri; anali kuwanyenga osauka ndikulambira mafano. Koma Allah sanafune kuti anthu amenewa adzilamulira mzindawu.

Choncho Allah analamula Mneneri kuti atenge anthu ake ndikulanda mzindawo. Mneneri anasonkhanitsa achinyamata ochokera mu anthu ake kuti alande mzinda wa Yeriko.

Anatenga anthu ake ndikukhonza zolanda mzinda wa Yeriko tsiku Lachisanu. Nawo atsogoleri a Yeriko anakhonza gulu lawo lankhondo.

Yusha alaih salaam ndi anthu ake anamenya nkhondo mwamphamvu ndimodzipereka. Anamenyana ndi asilikali aja mamawa wonse mpaka masana ndi madzulo.

Pamene dzuwa linayamba kulowa, Mneneri anayamba kudandaula; anadziwa kuti tsiku lotsatira ndi Loweruka, tsiku la Sabata lomwe linali tsiku lolemekezeka kwa iwo. Anthu ake sangamenye nkhondo tsiku la Sabata, choncho anapemphera kwa Allah subhanahu wa Ta’ala: “E Allah, lichedwetseni dzuwa kuti lisalowe” anapemphera motero.

Zinachitika zozizwitsa, dzuwa silinalowe kwa maola angapo ndipo linangoima malo amodzi. Mneneri ndi anthu ake anamenya nkhondo koopsa mpaka anapambana.

Tsopano kuchokera mu chitsanzo cha Menerei Yusha alaih salaam, tikutha kuona mmene Allah amapereka kupambana kwa omwe akhonzeka.

Pambuyo pa imfa ya Mneneri Yusha alaih salaam, Mneneri Hezqeel alaih salaam analowammalo mwake ngati Mneneri wa ma Israel.

Patadutsa nthawi yaitali chimwalilire Mneneri Yusha alaih salaam, ma Israel anali kukhala tsopano ku Palestine. Imeneyi ndi nthawi yomwe mliri unagwira mudzi ndipo anthu anali kufa paliponse moti aliyense anali ndi mantha.

Anthu anasonkhanitsa mawanja awo ndi katundu ndikutuluka mmudzimo. Allah anali okwiya pamene anaona anthu akuthawa mliri.

Iwo anayenda kwa masiku ambiri ndipo kenako anakhanzikika pa malo ena okwera.Pomwepo Mngelo wa imfa adawayitanira kuti: “Ifani nonsenu!”Aliyense wa opulumuka ku mliri kuja anafera pomwepo tsiku lomwelo.

Zaka mazanamazana zinadutsa ndipo malo omwe anthu aja anafera anatchedwa kuti Damardaan. Malo ajaanadzadza ndi mafupa a anthu akufa.

Tsiku lina Mneneri Hizqeel alaih salaam anali kudutsa pamalo paja. Anali odabwa kuona mafupi ali ponseponse ndipo anaima nthawi yaitali kudabwa chomwe chinachitika. Kenako nthawi yomweyo kunamveka mau: “Kodi ukufuna ndikuonetse mmene ndingawabwezeretsere mafupawo kukhala amoyo?” mau aja anafunsa

“Inde” Mneneri anayankha. Anali kudabwa ndi mphamvu za Allah.

Choyamba mau aja analamula Mneneri kuti ayankhule mau awa: “Ee inu mafupa, Allah akukulamulani kuti musonkhane!”

Mneneri anayankhula momwe analamulidwira. Kenako mafupa anayamba kuwuluka uku ndi uko kusonkhana ndikulumikizana. Mau aja anamulamulanso Mneneri kuti ayankhule mau awa: “Ee inu mafupa, Allah akukulamulani kuti muvale minofu ndi zovala zomwe munaferamo.” Mneneri atanena izi, mafupa aja anavekedwa ndi mafupa komanso magazi, kenako anavekedwa zovala zawo.

Kenako mau anamulamula Mneneri kuti ayankhule mau awa: “Ee inu amene mwawukitsidwa, nonsenu imilirani muchilamulo cha Allah!”

Zinali zozizwitsa! Onse aja anabwelera kukhala amoyo! Hahaha.. Mneneri sanakhulupilire zomwe anaonazo; anaona anthu amoyo zikwizikwi omwe anali akufa pakanthawi ka posachedwa.