Funso:
Kodi nchifukwa chani anthu amakonda kufunsa kuti “ndikufunafuna Sheikh omwe amachotsa ziwanda, amene ali ndi number yawo anditumizire?”
Yankho:
Amafuna kuti akawawelengere Qur’an, ma Dua ndi ma Dhikr chifukwa iwowo sadziwa, komanso safuna kudziwa.
Tidziwe kuti padziko lapansi palibe munthu yemwe angachotse chiwanda mthupi la munthu. Allah ndiyemwe amachotsa chiwanda kuzera mma dua, ma adhkaar komanso ma aayah omwe munthu amawerenga.
– Aliyense yemwe ali Msilamu ali okakamizidwa kudziwa ma dua, ma adhkaar komanso kuwerenga Qur’an.
– Msilamu aliyense ali okakamizidwa kukhulupilira mwa Allah, Angelo, Mabuku, Atumiki, Tsiku Lomaliza, ndikuti chikonzero cha zabwino ndi zoipa chimachokera kwa Allah (Qadar). Mwachidule, akhale ndi imaan. Imaan ndiyokakamizidwa mwa Msilamu aliyense.
– Msilamu aliyense akuletsedwa kuchita zoipa.
– Msilamu aliyense akukakamizidwa kukhala ndi Aqeeda yabwino osati ya bid’ah.
Zinthu zimenezi ndi zomwe zingapangitse kuti Msilamu aliyense adziteteze yekha kuziwanda ndipo akamatsatira malamulo a Chisilamu mmoyo mwake sadzakhunzidwa ndi chiwanda, azingomva mwa ena. Komanso akuyenera kusiya kutsatira zilizonse za dziko chifukwa ¾ ya za mdziko imachokera mu u Sultaan (utsogoleri) wa satana.
Iweyo ngati uli Msilamu okhulupilira zenizeni, ogwiritsa ntchito Chisilamu chako, sungafunefune komwe kuli Sheikh kuti akuwelengere Qur’an, chifukwa ukuidziwa kale. Sungafunefune Sheikh kuti akuwelengere ma dhikr, chifukwa ukuwadziwa kale. Sungafunefune Sheikh kuti akuwelengere ma Dua, chifukwa ukuwadziwa kale. Chimodzimodzinso, sungafunefune komwe kuli Sheikh kuti akuzingire nkhuku, poti dua yozingira nkhuku ukuidziwa, komanso zoyenera kuchita kuti uzinge ukuzidziwa.
Msilamu yemwe ali ndi mbiri zomwe ndazitchula zija, sangalowedwe chiwanda, chifukwa ali mumpanda wolimba womangidwa ndi Qur’an, Dhikr, Dua, Swalaat.
Ngati inu ndi akazi anu m’nyumbamo pamodzi ndi ana anu mukuphunzitsana zinthu zimenezi, simungaganizenso zoitana Sheikh chifukwa chilichonse chomwe mukufuna kuchokera kwa Sheikhko inu muli nacho m’nyumba. Palibe chachilendo chomwe Sheikhwo angachite chomwe inu mulibe.
Ngati zafika poti simungadziwelengere nokha, auzeni amuna anu, akazi anu, mwana wanu kapena achibale anu omwe ali Asilamu, kapena ma neighbor. A Sheikhwo afuneni kuti akuphunzitseni zoyenera kuti muzichita, zomwe simukuzidziwa.
Mukudziwa kale kuti ma Sheikh omwe amati “amachotsa ziwanda” ¾ ya iwo samachotsa ulere, koma business; kumeneko n’kudya chuma cha Asilamu munjira yolakwika. Kupangira business Ruqya ndi kosaloledwa.
Pofuna kuti makastomala achuluke apeze ndalama zambiri, mpamene amaonjezera zichitochito za haraam ndi shirk monga kugwiritsa ntchito ziwanda, kulemba Qur’an, matalasimu, ndi zina zotero. Komanso ambiri mwa iwo amaphwanya malamulo a Chisilamu; amamugwira odwala wamkazi pamutu, pamimba ndi malo ena ,,, kumugwira mkazi nthawi iliyonse ngakhale pa ruqya nkoletsedwa, mwamuna asagwire mkazi wamwini yemwe sim’bale wake. Kumuyang’ana popanda chotchinga nkoletsedwa ,,,, mapeto ake, ambiri akapanda kuchira amanena kuti “Ruqya sikuthandiza mwina tipite kwa asing’anga”. Ruqya ya Sharia singathandizidwe ndi msing’anga.
Ngati muli mkati mwakuphunzira Quran, ma dua, ma adhkaar, ndiye m’bale wanu wapezeka ndi chiwanda kapena kulozedwa, ndipo mulibe wachibale pafupi yemwe akudziwa; pezani aliyense yemwe akudziwa ndipo muonesetse kuti:
Ngati odwalayo ali mkazi, mupeze okuthandizani wamkazi. Koma ngati palibe, pezani mwamunayo ndipo musamusiye yekhayekha ndi wodwala mchipindamo.
– Msilamu aliyense aphunzire kudziteteza ku ziwanda ndi ufiti. Ruqya yomwe ili yabwino ndiyodzichitira wekha kapena mbale wako wapafupi kwambiri.
– Msilamu aliyense aphunzire ma Dua, ma adhkaar, kuwerenga Qur’an; kuti azidziteteza yekha ndipo ziwanda ndi ufiti sizingamukhunze
– Tikhonze Aqeeda
– Tiziswali kasanu patsiku komanso pa jamaah munthawi yake.
Pewani kupereka ndalama kwa ma businessman “ochotsa ziwanda” chifukwa inuyo panokha mukhonza kudziteteza kuti ziwandazo zisakukhunzeni, kapena kuti zikuchokeni ngati muli nazo.