خـــاتَمُ الخِـــطْبَةِ

ENGAGEMENT (WEDDING) RING
(Sheikh Naasiru Ddeen Al-Albaani)

Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse, Mtendere ndi Madalitso zipite kwa uyo yemwe Allah anamutumiza kuti adzakwaniritse makhalidwe abwino.

Pali zichitochito zina timazichita chifukwa cha kuzolowera, koma tikanakhala tikudzuwa kuti zambiri mwa izo zimachokera muzithaphwi zonyansa, bwenzi tikumazipewa.

Uthengawu ukuchokera mu buku la

آدَابُ الزِّفَافِ فِي السُّنَّةِ المُطَهَّرَةِ – لِلشَّيخِ نَاصِرُ  الأَلْبَانِيُّ (p.212,

buku lomwe Sheikh Muhammad Al-Albaani analongosola momveka bwino zikhalidwe komanso zizolowezi za pa nikaah zomwe ndizoipitsitsa komanso mathero ake ndioopsa kwa Msilamu yemwe amazichita. Ichi ndichilungamo chowawa, koma kwa okhulupilira omwe amachitsata chikhulupiliro chawocho mwachoonadi, asangalala kumva chifukwa ndinjira yosinthira kuti akapeze chipulumutso ku ng’anjo ya moto.

خــَــاتَمُ الخِـــطْبَةِ أو النكاح
ENGAGEMENT (WEDDING) RING

(Mphete yosonyeza kuti ndiwokwatira) zinachokera ku Shirk ya “Utatu wa Mulungu”.

Timatha kuona Asilamu ambiri pambuyo pochita “chinkhoswe”, kapena nikaah, mkwati ndi mkwatibwi amavekana ring yomwe amaitcha kuti “Engagement Ring,” kapena “Wedding Ring”. Izi tikawafunsa kuti anazitenga kuti, palibe yemwe amapereka yankho lolonda kupatula kukometsera zochokera mmitu mwawo kuti kuvala ring’ko kukhale kolondola komanso kwabwino. Koma lero lino dziwani kuti palibenso chilungamo china choposa kunena kuti zimenezi zikuchokera muchizolowezi za ma Kafir, chifukwa chiyambi chake chinachokera mu chipembedzo cha Akhristu kalelo.

Vuto lomwe liri mwa Asilamu ambiri lero lino ndiloti timangoti zikatisangalatsa zomwe taona ena akuchita, timazitengera ku zochita zathu za M’chipembedzo.

Tisamaiwale kuti nikaah ndi Ibaadah, ndipo ibaada iliyonse ikachitika imayenera kutsatizidwa ndi zabwino zokhazokha. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

وَأَتْبِعْ السَّيِّئَةَ الحَسَنَةَ تَمْحُهَــا

Ndipo tsatizani chabwino pambuyo pa choipa kuti chifute choipacho

Koma lero lino tikutsatiza choipa kuti chifute kapena kuchotsa madalitsa a chabwino chomwe tinatsogoza.

أصل خـاتم الخطبة أو الزواج
CHIYAMBI CHA WEDDING RING

Nkhosa za mpingo wa Chikristu kalelo zimati zikakwatira, mkazi anali kuveka mphete pachala chachikulu cha mwamuna, ndipo mwamunayo anali kuyankhula mawu awa: “M’dzina la Atate”.

Kenako amaisuntha mphete ija nkumuveka chala cha mkombaphala, ndipo amayankhulanso mawu awa: “Ndi la Mwana”. Kenako amaveka pachala chapakati ndipo mwamuna amayankhula mawu awa: “Ndi la Mzimu Woyera”.

Akamaliza amayankhula kuti “Aameen” kenako mkazi amaveka mphete ija pachala chachinayi ndipo sichimachotsedwanso. Kumeneku kunali kumanga banja, ndipo sangachotse pokhapokha banja lithe.

Imvani zomwe anayankha Angela Talbot, yemwe anali Chief Editor wa Section ya Mafunso mu nyuzipepala ya “The Woman” no.19, page 8, yomwe inatsindikizidwa ku London m’chaka cha 1960:

Funso: “N’chifukwa chani mkazi amavala ring pachala chachitatu chakumanzere?”

Yankho: “Zimanenedwa kuti m’chala chimenechi muli nsempha womwe wayenda mpaka mumtima. Komanso pachiyambi, kalekale mkazi amaika ring pachala cha mwamuna chachikulu chakumanzere ndikunena kuti: “M’dzina la Atate”, kenako pachala chamkombaphala ndikunena kuti: “Ndi la Mwana”, kenako pachala chapakati nkunena kuti: “Ndi la Mzimu Woyera”, ndipo akanena kuti Aameen, amaika pachala chachitatu pamene imakhanzikika osachotsedwa”.

Chongomva yankholi, Msilamu akhonza kudziwiratu kuti izi umu mulibemo chake. Zikuonekera poyera kuti omwe amachita zimenezi amatengera chikhulupiliro chachikunjachi, pochita zomwe anali kuchita komanso amachita akhristu. Inde, wamakani pamenepa akhonza kuyankha kuti “ife sitimayankhula m’dzina la atate ndi lamwana… koma timangovekana basi”. Nanga aliponso ena omwe munawatengera za ring’zi posakhala ma kafiriwa? Ngati mukusiya osayankhula mawuwo, ndiye kuti simukugwirizana nazo, bwanji osasiya zonse? Kodi inu mungadyere nsima yanu msuzi wa nyama ya nkhumba wokha nkumati simumadya nkhumba? Sizingatheke Msilamu kukhulupilira mbali ina ya chikaafir ndikukanira mbali ina, iyeyo nkukhala Msilamu wokhulupilira weniweni!

Sister, brother, mukuloledwa kuvala ring, koma ngati ring’yo chala chanucho chinalowamo kudzera munjira ya engagement, ichotseni ndipo mupange tawba chifukwa ndinu Msilamu koma mukupanga za chikhristu. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

مَنْ تَشَبَّهَ بِقَوْمٍ فَهُوَ مِنْهُمْ

Yemwe wadzifanizira ndi gulu lina, ndithu ameneyo ali m’gulu limenelo
Ndikudziwa kuti ena amaiyankha Hadithiyi kuti

“إِنَّمَـا الأَعْمَالُ بِالنِّيَّاتِ”

Ndithu ntchito zimakhala malinga ndi zitsimikizo;
ndipo ife sitikupanga ndi chitsimikizo chotengera kwa akhristu. Ayi ndithu, kumeneko nkuimva Hadtih mothamanga.

Ngakhale kuti niyya yanu siimeneyo, koma mukupanga za chikafir. Kodi inuyo mungapite pa bar nkukhala ndikuitanitsa fantha nkumamwera pomwepo? Poti chongofika pa counter ya bar’yo, mumakhala kuti muli mu system ya odzamwa mowa. Kudzifanizira sikukutanthauza kuti pokhapokha unene kuti ndikupanga izi poti akhristu amapanga.

Kuopsa kwa engagement ring nkokuti zikuchokera mu chikhulupiliro cha shirk, chom’panga Allah kuti ali mutatu (Atate – Mwana – Mzimu Woyera), zomwe Msilamu sakhulupilira.
Inuyo mukuona bwanji kuswali pomwe ring yotsimikiza utatu wa Mulungu ili pachala chanu? Tawheed ndi Shirk sizingasonkhane malo amodzi. Chotsani chimodzicho chitsale chimodzi … chotsani kudzifananiza ndi shirk ndipo mutsale ndi Tawheed.

Zili kwa inu kusintha kapena kutsala mu Mkwiyo wa Allah.

اللَّهُمَّ إِنِّي بَلَّغْتُ فَاشْهَدْ

Ee Allah, ine ndafalitsa uthenga wanu, choncho ikirani umboni