Walimah ndi phwando kapena chisangalalo chomwe chimabwera kumapeto komangitsa banja (Nikaah).

Ndizololedwa kuchita walimah nthawi yomweyo kapena kuchedwetsa malingana ndi kuthekera kwa munthu, ndipo iyenera kuchitika munjira yomwe ili yololedwa ndi malamulo a Chisilamu; zilizonse zomwe zili zoletsedwa mChisilamu monga nyimbo, kusakanikirana kwa akazi ndi amuna, kuimba ndikuvina kwa azimayi pamaso pa amuna, zonsezo ndizoletsedwa pa chisangalalo cha nikaah (walimah).

Ngati Nikaah yayenda bwino ndipo walimah yachitika mwa haraam, zimakhala nsambi za padera zomwe ndi tchimo koma nsambi zake sizimaononga nikaah. Koma ngakhale kuti tchimo la pawalimah silikuononga nikaah, sitikulimbikitsa kuchita zoipazo, chifukwa Chisilamu chikuletsa kwatunthu kupanga zirizonse za haram nthawi ina iriyoye. Ndiye sikuti titengere mwayi kuti poti walimah ya haraam simaononga nikaah.

Pomaliza tikumbutsane kuti nikaah ndi mapemphero (Ibaadah) omwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anachita kuwatchula kuti ndi njira (Sunnah) yake, choncho zikufunika kutsatira chiphunzitso cha Mtumiki ndikupewa zopeka zomwe zilibe umboni uliwonse komanso zomwe zikutsutsana ndi chiphunzitso cha Chisilamu pa mwambo wa nikaah. Mtumiki salla Allah alaih wasallam analimbikitsa kuchita walimah, choncho titsatire ndondomeko yake kuti tisaipitse chiphunzitso choyera cha Mtumiki.