Msilamu asamalimbane ndi kutsatira maina, magulu kapena zirizonse zomwe zikuonetsa kugawika kwa Ummah. Koma ndizofunika kwa iye kuzidziwa munjira ya kuphunzira, akadziphunzira afalitse choona chenicheni chomwe Asilamu atsatire. Imeneyo ndiye Da’wah ya Sheikh Muhammad bun Abul Wahhaab yomwe amadana nayo anthu ambiri.
Zomwe zili zofunikira kwa Msilamu ndikutsatira Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Sahaba ake, Manhaj ya ma Salaf Saalih amene anagwiritsa chiwongoko cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam, omwe ndi ma Sahaba ndi ma Taabieen onse. Amenewo amatchedwa Ahlu Sunnah wal Jamaah. Yense yemwe amatsata zomwe anabweretsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam adziwe kuti ali munjira imeneyo.
Mtumiki salla Allahj alaih wasallam anabweretsa Tawheed ndipo cholinga chake kunali kudzaononga Shirk ndikudzaitanira Ummah wonse ku Ibaada yomchitira Allah yekha. Choncho aliyense okhulupilira akuyenera kumaitanira ku Tawheed ndikuononga chirichonse chomwe chimayambitsa shirk komanso kuchitalikira.
Tsopnao liwu loti Wahabiya, ndililongosola mnjira ziwiri:
a. Likuchokera mmaina a Allah abwino (Al Wahhaab), ndipo munthu amapatsidwa dzina loti Abdul Wahhaab monga maina ena onse Abdul Rahmaan, Abdul Malik etc. Ndithu ine ndinali wokhumudwa brother ena atandifunsa maina oti asankhepo dzina la mwana wawo, nditawapatsa ndandanda womwe munali “Abdul Wahaab”, anati “brother dzina ili ndimadana nalo, sindikufuna mwana wanga adzatengere za ma Wahhabi”. Sindinayankhule zambiri, ndinangoti sorry, yang’anani maina enawo.
Ndinaona kuti ndibwino ndilongosole mwachidule poti zafika penapake.
Mukunena kwina, kutchula kuti Wahaabiya zikutanthauza kuti chirichonse cholumikizana ndi Al Wahhaab (Allah).
b. Dzina limeneli masiku ano limatchulidwa kwa anthu omwe amatsatira Da’wa ya Sheikh Imaamul Mujaddid Muhammad bun Abdul Wahaab bun Sulaiman Al Tamimi Al Hanbali – Allah amuchitire Chisoni. Chocho monga tikudziwira, omwe amatsatira Da’wah ya Sheikh ameneyu amatchedwa ma Wahaabiy.
Tatiyerni tione mtundu wa Da’wah imene anali kuitanira Sheikh Abdul Wahab yomwe imachititsa kuti anthu adzitchula dzina limeneli moipidwa.
Sheikh Abdul Wahhaab anali mmodzi mwa ma Sheikh a madh’hab a Imaam Ahmad bun Hanbali. Anapeza anthu a ku Najd (komwe anabadwira), akupanga ibaada yosemphana ndi yomwe anaisiya Mtumiki ndi ma Sahaba ake, monga kupembedza maliro, mitengo, myala, kufuna madalitso kuchokera kwa anthu ndi ma shirk amitundu yonse. Sheikhwa anayamba kufalitsa Da’wah ya Tawheed; anali kuchenjeza za shirk ya mtundu uliwonse. Aqeeda imene anali kuyendera ndi Aqeeda yomwe anasiya Mtumiki ndi ma Sahaba ake, Aqeeda ya Salaf Saalih yomwe ndi ya Ahlu Sunnah wal Jamaah. Izi tizidziwa bwinobwino tikamawerenga mabuku ndi ma fatwa a Sheikhwa komanso mabuku a otsatira ake, ana ake ndi zizukulu zake komanso ma Sheikh ena ambiri. Mabuku amenewa ali ponseponse. Koma poti Sheikhwa mmene anali kuletsa za Shirk ndikulimbikitsa Tawheed, anthu omwe ankaletsedwawo anali kuona kuti akuletsedwa ibaada ndipo anali kudana naye, komanso anali kudana ndi aliyense woletsa bid’ah ndi shirk. Anthu amenewo sikuti anatha nthawi imeneyo ayi, koma analipobe ndipo mmalo molola Sa’wa ya Tawheed anayamba kuitanira mbali yawo ya shirk ndi bid’ah, nkumayendelera mibadwo yawo mpaka lero lino. Nchifukwa chake tikuona anthu ambiri odana ndi Da’wah ya Sheikh Abdul Wahaab, abweretsa liwu loti Wahaabiya kukhala ngati ndigulu limodzi mmagulu osochera a m’Chisilamu. Tidziwe kuti magulu aja omwe Mtumiki anawatchula, ndimagulu osemphana ndi gulu la Mtumiki la Tawheed komanso lotsatira Qur’an ndi Sunnah … ndiye Wahabiya silimodzi mwa magulu amenewo, komanso Wahabiya si Madh’hab, si twareeqa monga mmene aliri ma twareeqa ena aja “twareeqatu Aqadiyaani, twareeqatu Ahmadiya, twareeqatu Qaadiriyaa etc”. Kulibe Twareeqatul Wahabiya – Kulibe! Koma ndi Ahlu Sunnah wal Jamaah, komanso ndi anthu omwe amatsatira Manhaj a Salaf Saalih. Abdul Wahhaab ndi Imaam chabe, monga ma imaam ena onse. Kusiyana kwake ndikoti iye anali Mujaddid (yemwe anagwira ntchito yaikulu popanga tajdeed (kupanga revive kapena restore Da’wah ya Tawheed). Ndiye ena okumva molakwika, opelewedwa mmaphunziro komanso safuna kupanga kafukufuku wazinthu zomwe amva, amangotenga zilizonse zomwe media ikuwauza, mpaka kusanduka nazo ma Sheikh ndikumafalitsa.
Tikamawerenga mabuku omwe analembedwa ndi eni ake Sheikh, ana awo, komanso ma Sheikh omwe amatsatira Da’wah ya Tawheed, sitipeza zomwe tikumamvazi, koma tipeza Tawheed yokhayokha. Mmene ndanenera muja kuti mabuku a Da’wah ya Sheikhwa ali ponseponse olembedwa ndi ma Sheikh ambirimbiri, mupeza kuti maiko omwe amadana ndi Da’wah imeneyi amadananso ndi mabukuwo. Ma Sheikh ochokera mu zizukulu za anthu omwe anali kudana ndi Da’wah ya Sheikhwa, amadana ndi mabuku onse a Tawheed imeneyi. Mumva akunena kuti mabuku a ma Wahabi musamawerenge … mabuku a Salafi musamawerenge … mabuku a Ahlu Sunnah wal jamaah musamawerenge. Chifukwea akudziwa kuti mukawerenga mabuku amenewo, mudziwa choonadi ndipo musiya bid’ah ndi shirk. Inu choyenera kuchita mufufuze kuti kodi Salaf Salih ndi ndani, nanga Ahlu Sunnah wal Jamaah ndi ndani, nanga Wahabi ndi ndani.
Da’wah ya Sheikh Abdul Wahhaab inali yochokera mu Qur’an ndi Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam
Wahhaabiya si Twareeqa – Wahaabiya si Madh’hab – Koma inali ntchito yoitanira ku Tawheed, kuwukitsa tawheed yomwe inakwilirika anthu nkuyiiwala.
Chocho ndi zofunika kwa m’bale iwe amene ukuphunzira Tawheed, utalikire anthu awo omwe akumakuchenjeza za Wahabiyya, chifukwa akukuchenjeza kuti usatsatire Haqq yochokera ku Ummah wa Salafi (Ummah womwe unapita pa chiwongoko cha Qur’an ndi Sunnah). Ndipo akumakubweretsera liwu loti Wahabiya ncholinga chokuopseza basi, chifukwa liwu limeneli limatchulidwa kwa anthu omwe agwiritsa Aqeeda yolondola ya Tawheed yeniyeni. Choncho atalikire anthu omwe akukumwetsa za kuipa ‘kochita kulenga’ kwa Adbul Wahaab ndi onse omwe ali mu Da’wah yake. Kuchenjeza kuti musatsatire Da’wah ya Tawheed ndi kwa kale kuyambira nthawi ya Umbuli pamene anthu anali asanavomereze uthenga wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Tawheed sungaidziwe popanda kuphunzira. Choncho m’bale wanga phunzira, ndipo uphunzire zochokera kwa anthu omwe anapita kale (Mtumiki, ma Sahaba, ma Taabieen, ma Taabie-taabieen). Awa ndiomwe anachoka ndi Tawheed komanso Aqeeda yopanga zigamba.