Uzair anali munthu woyera komanso wanzeru. Anakhala pambuyo pa Mneneri Sulaiman alaih salaam komanso asanabwere Mneneri Zakaria alaih salaam.

Tsiku lina monga mwachizolowezi chake, Mneneri anakayendera munda wake pa bulu. Chakumasana, anafika pa kamzinda kena kamene kanawonongedwa kalekale, ndipo panalibe yemwe anali moyo mmenemo. Anapeza nyumba zokugwaigwa, makoma afumbi ndi mafupa a anthu ambiri.

Mneneriyu anayenda mamawa wonse ndipo dzuwa linali kutentha kwambiri pamene anaganiza zopuma mumzinda umenewu. Anatsika pa bulu wake ndikukhala pansi pamtengo.

Anali ndi njala kotero anatenga nkhuyu ndi mphesa zomwe anali nazo mudengu ndipo anayamba kudya.

Anakhala pamenepo nthawi yaitali, kenako atadzuka kuti ayang’ane mbali zina, anaona kuti makoma omwe anali chimire anali akale kwambiri komanso okutha.
Anaganiza kuti akhonza kugwa nthawi iriyonse. Kenako anaona mafupa a wanthu ali ponseponse.

“Allah angadzawabwezeretse chotani anthu amenewa kukhala amoyo?” anayankhula izi mwachidwi.

Pamene Allah subhaanahu wa Ta’ala anamva zomwe anayankhulazi,  anakwiya ndipo anafuna kumuonetsa Mneneri uja kutha kwake. Anamutumizira Mngelo wa Imfa ndipo anatenga moyo wake monga mmene analamulidwira ndi Allah. Mneneri uja anafa kwanthawi yaitali. Zinanenedwa kuti anafa kwa zaka 100. Bulu wake uja anafanso mosakhalitsa ndipo zinthu zambiri zinasintha muzaka 100 zimenezo.

Tsiku lina Allah anaganiza zomudzutsa Mneneri uja kuchokera ku imfa. Anatumizanso Mngelo wa Imfa ndikumudzutsa. Pamene Mneneri anatsekula maso ake, sadadziwe zomwe zinachitika.

“Wakhala mutulo nthawi yaitali bwanji?” Mngelo anafunsa.

Kunali chakumadzulo ndipo Mneneri anali kukonda kugona masana…”Ndikuyenera kuti ndagona tsiku lonse, kapena gawo
latsiku…” anatero poti anali osokonezeka.

“Unali chigonere kwa zaka 100!” Mngelo anamuuza.

Mneneri anali odabwa kumva zimenezo. Anadziwa kuti zinali mphamvu za Allah zomwe zinam’bwezeretsa kukhala wamoyo.

Kenako Mngelo anawukitsanso bulu wa Mneneri uja.

Mneneri ananyamuka kubwelera kwawo.

Atafika pamalo omwe anabadwira, anali odabwanso kuona kuti mzinda wonse unasintha; unali ndi masitolo atsopano komanso misewu yatsopano, moti sanamuzindikire aliyense.

Pamene anafika panyumba yake, sanathe kumuzindikiranso aliyense.

“Ndine Uzair” anawauza anthu aja mowerezabwereza, koma anagwedeza mitu yawo ndikumuuza kuti sakumudziwa.

Kenako anapita kwa mai wina olumala yenwe anakhala panja panyumba, ndipo anapeza kuti anali osapenya.

“Iyi si nyumba ya Uzair?” anamufunsa 

“Inde ndi yomweyo” anayankha. “Koma anthu anaiwala za iye
kalekale, anachoka zaka 100 zapitazo”.

Mneneri anazindikira kuti mai okalambayu anali mzakazi yake nthawi imeneyo.

“Ndine Uzair!” anamuuza. “Allah anatenga moyo wanga, ndipo pambuyo pa zaka 100, wandibwezera!”

Mzakazi yokalamba ija inatha kuzindikira mau, koma sinali yotsimikiza. Choncho anamuuza Mneneri uja: “Allah anali kuyankha mapemphero a Uzair, ndiye ngati iweyo uli Uzair, pempha kwa Allah kuti ndikhale openya, komanso upemphe kuti ndiyende.”

Mneneri anavomera ndipo anagwada ndikupempha Allah. Kenako anaimilira ndikuika zala zake mmaso mwa mai uja ndikuwasisita pang’onopang’ono, ndipo anachotsa ndikunena kuti: “dzuka mu mphamvu ya Allah!”.

Zinali zozizwitsa! Anayamba kuwona chirichonse tsopano! Kenako anadzuka yekha ndikuyenda. Mai anali osangalala kwambiri ndipo anamuuza Mneneri uja mokondwa: “inde, zomwe ukuyankhulazo ndizoona. Ndikuikira umboni kuti ndiwe Uzair!”

Kenako anamupempha Mneneri kuti amutsate. Anapita naye ku msonkhano wa ma Israel. Mwana wa Mneneri yemwe anali ndi zaka 118 panthawiyo ndi amene anali kutsogolera mtsonkhanowo. Ana ndi zidzukulu zake, onse anali nawo pamsonkhanowo. Mzakazi yachikulire ija anawaitana iwo: “Tamuoneni uyu!

Mungamudziwe kuti ndi ndani?” Koma palibe yemwe anamuzindikira ndipo anagwedeza mitu yawo.

 “Ndi bambo ako, Uzair! abwelera!”

“Ukunama!” mwana wake uja anatero. “Angabwelere bwanji pakutha pa zaka 100?”

“Tandione ine!” anatero mzimai “ndine mzakazi yako yokalamba ija. Ndinali openya mbuyomu? Munandiona liti ndikuyenda? Bambo ako andipemphelera, ndine tsopano; ndikuyenda komanso kupenya!”

Mwana wa Mneneri anaimilira ndikupita kwa iwo. “Bambo anga anali ndi chizindikiro pakati pa mapewa awo.” Anamuuza Mneneri uja.
“Tikukhulupilira ngati ungationetse chizindikiro chimenecho”

Uzair anawaonetsa chizindikiro, ndipo mwana wake anazindikira kuti analidi bambo ake.

Anthu onse anamukumbatira Mneneri ndipo anali osangala kuona kuti wabwelera.

Munthawi yomwe Mneneri anali mu imfa ija, Mfumu yoipa yak u Babylon, Nebuchadnezzar, inaononga mabuku onse a Torah ncholinga choononga Chipembedzo. Choncho palibenso yemwe anali kukumbukira Torah panthawiyi. Buku lomwe linatsala ndi lomwe linakwiliridwa malo ena ake omwe anali kudziwako Mneneri uja basi.

“Allah ndi Wamkulu ndithu”. Zidzukulu zake zinatero. “Ndinu nokha yemwe angatiuze komwe kuli buku lomaliza la Torah”

Uzair anawatenga anthu aja nkupita nawo pamalo pomwe ankadziwa kuti Buku la Torah linakwiliridwa, ndipo analitulutsa.

Anthu ataona buku lija anali osangalala kwambiri; poti ankaganiza kuti basi linasoweratu.

Zilembo za m’buku lija zinali zitawola ndipo buku linanyenyeka.

Uzair alaih salaam anakhala pamthunzi wa mtengo mozunguliridwa ndi ana ake kuti akopere buku lija. Anakopera mosamala mau onse a mu Torah ndikukhonza buku latsopano.

Uzair anakahala ndi ana a Israel kwa zaka 40.