Mbiri ya ‘Uthmaan bun ‘Affaan mwachidule

Alongosolereni ana anu achichepere nkhani zimenezi

Uthman bun Affaan radhia Allah anhu anabadwa patadutsa zaka 7 chibadwire Mtumiki salla Allah alaih wasalaam. Iye anali ochokera mu nthambi ya fuko la Quraysh yotchedwa Umayyah, fuko lopambana kwambiri mma Quraysh. Awa anali anthu amphamvu komanso olemera, ndipo Uthman anali mwana okondedwa kwambiri chifukwa cha makhalidwe ake abwino komanso manyazi.

Munthawi ya umbuli, anthu odziwa kulemba ndikuwerenga anali osowa pakati pa ma Arabs, koma Uthman anali kudziwa monga mmene analiri Umar radhia Allah anhu.

Uthman anali wa business ya zovala wopambana ndipo aaali ndi mbiri yabwino mmoyo mwake kuyambira nthawi yomwe sanali Msilamu.

Uthman anali mzake wa Abu Bakr, yemwe anamulondolera ku Chisilamu pamene anali ndi zaka 34 zakubadwa.

Pambuyo pakulowa Chisilamu, Uthman ankakonda kukhala pafupi ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti aphunzire zambiri za Chipembedzo cha Chisilamu. Analoweza ma Hadith okwana 146 kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo anali mmodzi mwa ma Swahaba omwe anali kulemba Qur’an.

Patatha zaka zingapo, Uthman anakwatira mwana wachiwiri wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, Ruqayyah.

Koma ngakhale anali olemera komanso olemekezeka , abale ake anali kumuzunza chifukwa cha kulowa Chisilamu, choncho anasamukira ku Abbysinia, ndipo atabwelera kumeneko anatsamukira ku Madina pamodzi ndi Asilamu ena.

Ku Madina kunali kosowa madzi, ndipo kusamalira chuma kunali kovuta kupatula kwa anthu ochepa. Koma poti Uthman anali odziwa za malonda komanso kukambirana ndi anthu, anaganiza zopeza madzi kuti athandize Asilamu. Choncho anakambirana mtengo ndi mwini chitsime kuti adzitunga madzi tsiku limodzi, tsiku linalo adzitunga mwini wake, ndipo Uthman anali kupereka madzi kwa Asilamu mwa ulere. Kenako mwini chitsime anaganiza zogulitsa mbali ina ya chitsime kwa Uthman.  Pamenepo Asilamu anali kutunga madzi mwa ulere.

Business ya Uthman inayambanso kuyenda bwino ku Madina moti anapindula monga mmene anali kupindulira ku Makkah. Nthawi zonse Uthman anali kupereka chuma chake kwa Asilamu komanso anali kuthandizira Asilikali a Chisilamu; nchifukwa chake anali odziwika ndi kupereka.

Isanachitike nkhondo ya Badr, mkazi wake anadwala ndipo Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamulola kuti asamenye nawo nkhondo. Koma mwatsoka Ruqayyah anamwalira. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamva naye chisoni ndipo anampatsa mwana ina, Kulthum. Uthman radhia Allah anhu anatchedwa kuti Dhu Nnurain (mwini kuwala kuwiri) chifukwa cha ulemelero wokwatira ana awiri a Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Uthman anamenya nawo nkhondo ya Uhud ndi Khan’daq. Ndipo pambuyo pa nkhondo  ya Khan’daq Mtumiki salla Allah alaih wasallama anaganiza zokachita Hajj ku Makkah, koma anamutumiza kaye Uthman ndipo mwatsoka ma Quraysh anamugwira nkumusunga. Pambuyo pake anakambirana ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam mpaka anaika mapangano omwe anatchedwa Sulhul Hudaibiyah.

Chithunzithunzi chomwe tikuchipeza mwa Uthman ndi choti anali wachilungamo, wopereka, wachikondi  ndi chisoni.  Iye anali kupemphera usiku kawirikawiri, kusala masana, kupanga Hajj chaka chirichonse komanso kusamalira osauka.

Komatu ngakhale anali olemera choncho, moyo wake unali simple moti anali kugona pabwalo lamzikiti wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Uthman radhia Allah anhu anaidziwa Qur’an mumtima ndipo anali kudziwa tanthauzo la verse iliyonse. Munthawi ya utsogoleri wake, mbiri zabwino za utsogoleri wa Abu Bakr ndi Umar monga kuchita chilungamo kwa aliyense, kulimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu komanso kufalikira kwa Chisilamu, zinapitilira.

Ulamuliro wa Uthman unafalikira mpaka ku Morocco mbali ya kumadzulo, ndipo ku Afghanistan mbali yaku mmawa, komanso kumpoto, unafalikira ku Armenia ndi Azerbaijan.

Mu utsogoleri wa Uthman, anakhanzikitsa gulu la asilikali a nkhondo ya mmadzi, ndondomeko ya boma inawunikidwa ndipo ntchito zambiri zinakwaniritsidwa.

Uthman radhia Allah anhu anatumiza ma swahaba omuyimilira mmadera osiyanasiyana omwe Chisilamu chinafalikira, kuti adzitha kudziwa mmene miyoyo ya anthu ikuyendera.

Ina mwa ntchito zapamwamba zomwe Uthman anagwira potukula Chisilamu ndi kusonkhanitsa Qur’an yolemekezeka. Mabuku ambiri a Qur’an anapangidwa ndikugawidwa mmadera onse a Chisilamu dziko lonse.

Utsogoleri wa Uthman unatha zaka 10. Zaka 6 zoyambilira zinali za bata ndi mtendere, pomwe zaka 6 zomaliza zinali zovuta  pamene anthu anayamba kupandukira. Ayuda pamodzi ndi anthu ena anayamba kumemeza anthu kuti awukire mtsogoleriyu. Anali kuwulutsa mavuto a anthu poyera ndikubweretsa mkwiyo mmitima mwawo.

Mwinatu nkumadabwa kuti zinatheka bwanji mtsogoleri yemwe anali ndi asilikali ochuluka komanso amphamvu, sanakwanitse kuthana ndi anthu opandukirawa. Komatu Uthman akanafuna, akanatha kuwaononga onse nthawi imodzi, koma sanafune kuti akhale oyamba kukhetsa mwazi wa Asilamu. Ngakhale kuti iwo anali opanduka kwambiri, Uthman anasankha kuwapilira powanyengelera ndi chifundo komanso kukoma mtima kwake. Iye anali kukumbukira nthawi zonse mawu a Mtumiki oletsa kukhetsa mwazi wa Msilamu.

Anthu ogalukira anamulamula kuti atule pansi utsogoleri, komanso ena mwa ma swahaba anamupempha kutero. Anatsala pang’ono kuvomera koma anabwelera mbuyo malinga ndi lonjezo lomwe anapereka kwa  Mtumiki loti Allah akadzamupatsa  udindo pakati pa Asilamu, anthu akadzafuna kuti asiye, asadzawalole.

Tsiku lina, anthu ogalukira anazungulira nyumba ya Uthman kuti amuphe. Iye anayankhula kwa munthu wina wabwino kuti Mtumiki anapanga pangano ndi iye ndipo apilira pokwaniritsa.

Patadutsa kanthawi, anthu aja anakwanitsa kutswa nyumba ya Uthman ndikumupha. Pamene anali kuyesera kumupha, Uthman adali kuwerenga Qur’an verse 137:

فَسَيَكْفِيكَهُمُ اللّهُ وَهُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ

“Choncho Mulungu akuteteza kuzoipa zawo, ndipo Iye ndi wwakumva, wodziwa”.

Uthman anamwalira masana a Lachinai pa 17 Dhul Hijjah 35H. Anali ndi zaka 84 zakubadwa koma  anamwalira ali wamphamvu komanso  wodzichepetsa chifukwa cha kukonda Allah ndi Mtumiki wake, ngakhale kuti anadutsa mu zovuta zambiri.