Kodi Experiment (Kuyesera) ili ndi gawo muntchito ya Ruqya?

 Experiment  imachitika mu makhwala (akuchipatala kapena azisamba). Udokotala ngakhalenso using’anga zimachokera mma experiment pofuna kupeza mankhwala anthenda inayake. 

Pomwe Ruqya, Msilamu akuyenera kutenga zokhazo zomwe Shariah inaloleza, osawonjezera zochokera mu experiment yamtundu uliwonse.

Masiku ano anthu ambiri ochita Ruqya ya Shari’ah akusokoneza zinthu ziwirizi, akutenga njira ya udokotala, using’anga, matalasimu, kapena njira ya mankhwala azisamba nkulowetsa mu ruqya. Kumeneko ndikulephera dongosolo la ruqya. Ndipo zikawavuta amati “basi Ruqya tayesera yalephereka tione mbali ina”. Ruqya siyoyesera, koma kuchita. Zomwe mukuyenera kuyesera ndizaudokotala, using’anga kapena ufiti ndi matalasimu.

الرقية والرقاة – المدخلي ص13

Kodi ndizololedwa kum’pangira Ruqya Kaafir?

Palibe yemwe analesa kum’pangira Ruqya Kafir. Ndizololedwa kutero chifukwa Swahaabiyyu wolemekzeka, Abu Saeed Al Khudri anampangira Ruqya kaafir; pamene anali kupita kunkhondo ndi anzake, anadutsa pamudzi wina ndipo anawapempha eni mudziwo kuti apumuleko koma anawakana. Choncho iwo anakhala panja pamudzi uja ndikumadikira nthawi yonyamukira. Kenako anamva kuti mtsogoleri wamudzi uja analumidwa ndipo anthu ake anafika kwa ma swahaba aja nkuwapempha kuti akamuchitire ruqya. Ma swahaba anawauza anthuwo kuti awalonjeze zomwe angawapatse akawathandiza munthuyo nkuchira, poti iwo sanawathandize pachiysambi pamene anapempha malo. Abu Saeed anapita ndipo anamuwelengera Surah Al-Fatiha ndikuchira nthawi yomweyo, ndipo anawapatsa ziweto ngati malipiro. Atamudziwitsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam zomwe zinachitikazi, anavomereza.

Lero lino nzachisoni anthu ambiri akutsutsa zakumpangira kafir ruqya, kumachita chiyambi cha ruqya ya sharia chinachitikira pa kaafir! Tisapange halaal kukhala haraam chifukwa yemwe amaloleza ndi kulesa zinthu ndi Allah ndi Mtumiki wake basi!

Kodi ndizololedwa opanga Ruqya kutenga malipiro?

Palibe vuto kutenga malipiro pa Ruqya, chifukwa cha Hadith ya Abi Saeed ija, pomwe anatenga malipiro pambuyo pompangira munthu Ruqya ndikuchira. Koma lero lino chomwe amalakwitsa opanga Ruqya ambiri ndichoti akumalandira malipiro asanagwire ntchito! Kulolezedwa kwa kutenga malipiro a Ruqya kukuyenera kuchitika pambuyo poti munthu wachira. Ndipo ndikulakwitsa kulamula ndalama munthu akangokupemphani kuti mumuthandize! Musaike chipsinjo cha ndalama mumtima mwa odwala. 

Mmene tamvera mu Hadith ija, munthu uja akanakhala kuti sanachire, ma swahaba sakanatenga malipiro poti sanapindule naye. Komatu lero lino anthu aisandutsa ruqya kukhala business … munthu akumayamba kuganizira za ndalama kusiya machiritso a wodwala, kutanthauza kuti condition ndiyoti ngati alibe ndalama samuthandiza, pomwe zoona zake ndizoti munthu ngati sachira asapereke ndalama.

Ndipo ambiri akumamumwerengera munthu kamodzi kokha, basi nkutenga ndalama … pakadutsa timasiku vuto lija nkuyambiranso, amalipiritsanso ndalama ina. Vuto ndiloti owerenga Ruqya sanakwaniritse Ruqya, chifukwa Ruqya siimafunika kungowerenga kamodzi nkumapita. Ruqya sitimadziwa kuti munthu achira liti, mumayenera kungomuwerengera mpaka muone kusintha

Nchifukwa chake timalimbikitsa zoti aliyense adziwe kudzipangira ruqya komanso kuwapangira ena, kuti zovuta ngati izi zizichepa.

 Kuwerengera Ruqya Mmadzi – Zoona zake zenizeni

Ndizoona kuti ma ulamaa ambiri, ngakhale ma sheikh ambiri lero lino, amaphunzitsa mbali ina ya mapangidwe a ruqya kuti kumawerengera mmadzi ndikumpatsa wodwala kuti amwe kapena kusamba. Ndipo chifukwa chakuona kuti izi zimathekadi, komanso ma ulamaa otchuka anazilowetsa mu system ya ruqya, ambiri timaphunzitsa ndithu kuti ndizotheka kugwiritsa ntchito. Komatu izi zikuchokera mu experiment, chifukwa choti zilibe umboni weniweni wa saheeh woti Mtumiki salla Allah alaih wasallam anachitapo kapena kulamula. Koma ndizochokera mwa ma sheikh omwe anatiphunzitsa mapangidwe a ruqya komanso analemba mabuku awo a ruqya shar’iyah. Ndipo ndizambiri zomwe timazitenga kuti ndinjira yovomerezeka ya ruqya,,, koma funso nkumati kodi zimenezi zili ndi umboni?

Pafunso loti “Kodi kuwerengera Qur’an mmadzi ndi hukm yanji?” Sheikh Rabieu bun Haadi Al Madkhali anayankha mu buku lawo la الرقية والرقاة – المدخلي ص23-24 kuti:

“Sizofunikira kutero, ngakhale kuti ma ulamaa ena analoleza, koma palibe umboni wololeza kutero. Mtumiki salla Allah alaih wasallam ngakhale ma Swahaba sanachite zimenezo. Ndipo awo omwe akuloleza kulemba Ruqya, kusamba ndi kumwa komanso zina zotero, alibe umboni. Tinaphunzitsidwa kuti sitikuyenera kutenga chigamulo mu deen popanda umboni. Mawu a munthu aliyense amatha kutengedwa ndi kukanidwa, kupatula Mtumiki wa Allah salla Allah alaih wasallam

 Chomwe chimapangitsa kuti ma Sheikh ambiri azidzikakamiza kupanga Ruqya mwaumbuli

Ambiri omwe amapanga ruqya nkumasakaniza za harama komanso za shirk ndi bid’ah mkati mwake, ukawalangiza kuti asiye mchitidwe umenewo, amayankha kuti: “Ndibwino kugwiritsa ntchito matalasimu chifukwa mmenemo timagwiritsanso ntchito Qur’an, kusiyana ndikuwalola Asilamu kuti azipita kwa asing’anga kapena ma pulofeti ndi ma pasitala!”

Inu ndamene akuwononga, alalikireni kuipa kwa kupita kwa abimbi, asing’anga ndi a prophet. Ngati sakumverani, asiyeni azipita bola inu mwakwaniritsa udindo wanu, koma ngati mufuna kuwathandiza ndi ruqya, phunzirani ndondomeko yake ndipo musaiyambe ntchitoyo musanakwaniritse. Musadzikakamize kugwira ntchito yomwe simukuidziwa, mapeto ake muwononga aqeeda yanu ndi aqeeda ya anthu komanso miyoyo yawo ndi moyo wanu womwe. Musapange ruqya chifukwa chowaletsa anthu kupita kwa asing’anga!Koma aphuzntiseni kuipa kwa kupita kwa asing’anga ndipo ngati muli ndikuthekera, apangireni ruqya ncholinga chowathandiza.

الرقية والرقاة – المدخلي ص27