Funso:

“Kodi nchifukwa chani mu ulaliki wa ma Khawaarij munasankha  kupereka chitsanzo nkhani ya Usama? mesa anali Msilamu? simukuona kuti anthu adziwona ngati mukumufukula zinsinsi zake kapenanso kumuweruza komans kuipitsa mbiiri yake? Komanso ambiri amakhulupirira kut iye uja amapanga jihad yolongosoka, komano kuyankhula nkhani yakeku zikhala ngati mukumuwukira, komans kudana ndi jihadiyo. Bwanji simunasankhe kunena njira za sharia popanga jihad ndi zina kuti anthu aidziwe bwino papanda kumutchula munthu ndi gulu la jihad? Anthuwo bwenzi akudzipasa okha yankho potengera mmene magulu ankhondowo amapangira.

Ndikanakonda ma audio a ulaliki wokhawo asafalikire.

Ngat ndalakwitsa pliz forgive me.”

Kutamandidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa zonse, mtendere ndi madalitso zipite kwa Mtumiki wake Muhammad salla Allah wasallam.
Simunalakwitse kalikonse popereka maganizo anu. Ineyo ndakumvani, ndipo ndizomwe zimafunikira zimenezo; yemwe waona vuto pa ulaliki adzimudziwitsa olalikirayo, kuchokera munjira imeneyo aliyense mwa olalikira amatha kudziwa zolakwika zake ndikukhonza komanso kupindula,,, kapena ngati zisali zolakwika ndiye kuti yemwe anaona ngati kuti zinali zolakwikayo apindulapo.. ndipempha Allah anditsogolere pakulongosola mfundo iliyonse yomwe mwatulutsa in shaa Allah.
Ndingokumbutsa kuti cholinga cha ma audio a Khawaarij aja ndi kufotokoza Aqeeda za magulu osochera mChisilamu. Ndipo gulu loyamba ndi limenelo, Khawaarij; momwe kumapeto kwake kwadza chitsanzo cha Osama bin Laden ndi magulu a Jihaad omwe akuwadziwa anthu munthawi zathu zino.
Chitsanzocho chabwera chifukwa choti Al Qaeda komanso magulu ena ndi omwe akuyendera Aqeeda ya Khawaarij pochita jihaad komanso da’wah zawo. Choncho panalibe chitsanzo chomwe ndikanapereka kuposa zomwe anthu akudziwa. Komanso dziwani kuti ndizovuta kuti munthu aidziwe aqeeda ya ma Khawaarij popanda kupereka chitsanzo, chifukwa imapusitsa kwambiri; zochitika zawo zoonekera zimaonetsa kuti ndi zabwino kwambiri pamaso pa Allah (monga mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananenera) koma aqeeda ndiyomwe imakhala yosokonekera, choncho ndimayenera kupereka chitsanzo kuchokera mwa omwe tili nawo pakali pano ndipo ndi odziwika.
Osama bin Laden anali Msilamu ndithu okhulupilira mu umodzi wa Allah (Tawhid),  Mbiri zake (Swifaatih) komanso Maina ake abwino (Asmaaul Husnaa), komanso anali Ahlu Sunnah wal Jamaah – Salafi (malinga ndi biography yake) ndipo anthu omwe amamutsatira ndi chimodzimodzi.
Koma Mchisilamu munthu akamabweretsa zinthu zosemphana ndi Aqeeda ya Mtumiki, amayenera kulangizidwa … akapanda kumvera malangizowo, ma Sheikh amayenera kuwalangiza anthu kuti asatsatire zomwe akuchita zolakwikazo.
Choncho Osama sindikumujaja, koma ndikufalitsa zomwe ma Ulamaa komanso ma Mufti omwe ankakimana naye face to face anafalitsa kalekale, kuti tipewe kukhala ndi ma ideologies a khawaarij omwe anafalitsa Osama. Koma judgment ya ntchito zake ili mmanja mwa Allah … kwa ife ndikupewa zoipa zomwe zikupezeka mu da’wah yake ndikuwadziwitsa ena. Munthu amayenera kubisidwa zolakwika zake ngati analangizidwa ndikumvera ndipo anasintha
ومن ستر مسلما ستره الله في الدنيا والآخرة
“ndipo yemwe wamubisira Msilamu, Allah amubisa padziko ndi Tsiku Lomaliza”
Koma ngati anapanga zolakwika nkulangizidwa koma sanabwelere mbuyo, yemwe wazindikira zolakwikazo apulumutse Asilamu ena kuti asagweremo.
Munkhani zimenezi ndakamba mbiri yake yomwe ili related to Aqeeda ya Chisilamu yomwe amagwiritsa ntchito. Mbiri yake ya personal tilibe nayo ntchito chifukwa singatithandize mu Chisilamu … choncho Jihad komanso Aqeeda si mbiri zamunthu koma Chisilamu.
Sindikuonapo kuti ndamuukira munthu, kuukira munthu wamba kulibe kanthu Mchisilamu koposa kuwukira malamulo a Chisilamu ndi atsogoleri ake (zomwe amachita magulu amenewa).
Komanso sindikudana ndi Jihaad. Msilamu aliyense yemwe amaidziwa Jihaad yomwe analamula Allah ndikuphunzitsa Mtumiki, akaona kuti ena ake akuipanga molakwika, akuyenera kulongosola zolakwikazo posonyeza kuikonda Jihaad ya Mtumiki komanso kudana ndi jihaad yolakwika.
Ndinalongosola mbali ina pang’ono, ya machitidwe a jihaad mu audio ina, chifukwa mma audio awa cholinga chake sikulongosola za jihaad, koma Aqeeda
Ndizovuta kuti anthu adzipatse okha yankho lolondola potengera mmene magulu awa amachitira jihaad … mapeto ake yankho lake limakhala loti “Chisilamu chimalimbikitsa terrorism, Qur’an yadzadza ndi kukhetsa mwazi wa osalakwa” etc monga mmene timamvera mma media.
Komanso maiko ambiri ngakhale ku Malawi, anthu amaopa kutsogoleredwa ndi President wa Chisilamu poganiza kuti adzalowetsa Magulu a nkhondo amenewa (Al Qaeda, ISIS, Boko Haraam,  Al Shabaab) mdziko. Imeneyotu ndiye judgment yomwe anthu amatenga kuchokera ku magulu amenewa … tsopano mukuona, Chisilamu chonse chikuipa chifukwa cha munthu mmodzi, ndiye ife tikulongosola za mmene jihaad ya munthuyo iliri kuti tipulumutse mbiri ya Chisilamu, anthu aidziwe Jihaad yeniyeni komanso Aqeeda yake ya jihaadiyo.
Pofunika tilimbikire kuphunzira Aqeeda kuti mdima wa umbuli wa zonsezi utichoke.
Mfundo yanu yomalizayo ndiyovuta kuti ingachitike, poti nkhanizi zinafala kalekale mmabuku omwe ma ulamaa amene anali kulangiza Osama analemba, ndipo ine ndimangotanthauzira Mchichewa, monga mmene mukumvera ndikamayankhula, palibe mau ochokera mwa ine koma ndikumatchula ma ulamaa ndi mabuku awo. Ndiye kumbali ya kufala, zinafala kalekale ndithu kuyambira nthawi yomwe Osama anali moyo ndipo sikhala miseche. Anthu akuwerengabe ndipo ofalitsa akufalitsa, kunangosala kudziika mchichewa. Zikuoneka ngati zoipa poti kuyamba kumene kwa ife kudzimva pambuyo poti tinkangomvera mma nyuzi ndi,mma TV anthu akungoti Chisilamu ndi uchigawenga,,,osadziwa zikuchokera pati.
Ngakhale mu Qur’an Allah Ta’ala anafotokoza nkhani za anthu omwe anali kuchita zolakwika ncholinga choti ife tiphunzire tisadzichite.
Komanso nkhani za ma Khawaarij, zonena kuti kudzafika anthu oterewa, anena kale Mtumiki kuwauza anthu (mu hadith yomwe ndaifotokoza kumayambiliro kwa ma audio). Ndiyetu paja iye anati
بلغوا عني ولو آية
“falitsani zochokera kwa ine ngakhale liwu limodzi”
Koma sitikutulutsa munthu Chisilamu komanso sitikumujaja. Chiweruzo chili mmanja mwa Allah, kwa ife nkuwunikirana Haqq.
Inenso ndingakondwe nditakhonzedwa ma mistake omwe akupezeka mma audio onse 25 aja, osati pankhani ya Osama yokha, imene yafika ku ma audio atatu akumapeto.
Vuto ndiloti ambiri omwe akudzudzula akukhala kuti angomvera ma audio amenewo okha poti ndi omwe akufalitsidwa mwakathithi ncholinga chofuna kupanga criticize basi, popanda kudziwa kuti kodi series yonse ikuchokera kuti, nanga cholinga chake ndi chani
Ndithokoze mmodzi mwa anthu 100 aliyense yemwe akumati akapeza vuto akumandifunsa directly ineyo mwini ma audio. Kuchokera mwa iwo ndikuwonjezera ‘ilm.
Ndathokoza pa mafunso anu komanso pempho lanu.
Allah akudalitseni.
Wassalaam Alaikum