Nkhani ina yomwe Qur’an ndi Baibulo sizimagwirizana ndi ya mkazi yemwe akuikira umboni. Ndi zowona kuti Qur’an inalangiza okhulupilira omwe akugwirizana ngongole ya chuma kuti apeze mboni ziwiri zazimuna kapena mwamuna mmodzi ndi akazi awiri (2:282).

Ndi zowonanso kuti Qur’an imavomereza umboni wa mkazi kukhala wofanana ndi wa mwamuna. Ndipotu umboni wa mkaziyo ukhoza kulepheretsa wamwamuna kuti usagwire ntchito; Ngati mwamuna wamunamizira mkazi wake kuti ndi wosayera (wachita zadama), Qur’an ikumuuza kuti alumbirire mobwereza kasanu ngati umboni pa tchimo la mkazilo. Koma mukulumbira konseko, ngati mkazi wakana komanso walumbira mobwereza kasanu, sakuyenera kutengedwa kuti ndi wolakwa (24: 6-11).

Pomwe mbali ina (ku Chiyuda), akazi sankaloledwa kuikira umboni mzaka zoyambirirazo. 12Ma Rabbi (akuluakulu a Chiyuda) ankawelengera kuti akazi satha kuchitira umboni pakati pa matembelero asanu ndi anai a akazi onse,  chifukwa chakuti akazi onse ndi ochimwa (onani gawo la “Cholowa cha Hawaa”).

Akazi achi Israeli lero lino saloledwa kupereka umboni mmakhoti mwawo. 13 Ma Rabbi amapereka umboni woletsa mayi kuikira umboni, kuchokera pa Genesis 18:9-16, pamene pananenedwa kuti Sara, mkazi wa Abrahamu adanama. Iwo amagwiritsa ntchito nkhaniyi ngati umboni wakuti akazi sangakwanitse kuikira umboni. Dziwani kuti nkhaniyi, yomwe inakambidwa mu Genesis 18:9-16, yafotokozedwa kangapo mu Qur’an popanda kumunamizira Sara kulikonse (11:69-74, 51:24-30).

Mu Chikhristu cha Kumadzulo, akazi akhala akuletsedwa kuikira umboni  mpaka kufikira mzaka zaposachedwapa. 14

Malinga ndi Baibulo, ngati mwamuna wamunamizira mkazi wake kuti sali woyera, umboni wa mkaziyo sungagwiritsidwe ntchito. Mkazi yemwe waganiziridwa kulakwa, ayenera kufunsidwa pogwiritsa ntchito myambo yovuta ndi yowawa kwambiri, yomwe ingatsimikize poyera kuti si wolakwa kapena ndi wolakwa (Numeri 5:11-31). Ngati wapezeka wolakwa pambuyo pa mwambowo, adzapatsidwa chilango cha kuphedwa. Koma ngati wapezeka kuti si wolakwa, mwamuna wake (yemwe adamunamizira tchimolo) sadzapatsidwa chilango chirichonse pakumunamizira mkazi wosalakwa.

Kuphatikizanso apo, ngati mwamuna wakwatira ndikupezeka kuti mkaziyo sinamwali (si virgin), umboni wake uliwonse sudzawerengedwa (chifukwa chakuti anagonapo ndi mwamuna asanakwatiwe). Ndipo ngati akuona kuti akumunamizira, makolo ake amayenera kubweretsa umboni pamaso pa akuluakulu, wakuti mwana wawo anali namwali, koma ngati alephera kutero, mwanayo anali kugendedwa pamaso pa bambo ake mpaka kufa. Ndipo ngati makolowo abweretsa umboni wakuti mwana wawo anali namwali, mwamuna uja (poti anamunamizira mkazi) anali kulipiritsidwa ndalama yokwana masekeli zana a siliva (100 Shekels) ndipo anali kulamulidwa kuti asadzamusiye banja. Malemba akunena kuti:

“Mwamuna akatenga mkazi ndi kugona naye koma sakum’kondanso, ndipo akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi, mwakuti wamuipitsira mbiri yake ponena kuti, ‘Ine ndinatenga mkazi uyu ndi kugona naye, koma sindinapeze umboni uliwonse woti anali namwali.’ Pamenepo bambo ndi mayi a mtsikanayo azibweretsa umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali kwa akulu a mzinda kuchipata cha mzindawo. Bambo a mtsikanayo aziuza akuluwo kuti, ‘Ine ndinapereka mwana wa mkazi kwa mwamuna uyu kuti akhale mkazi wake ndipo akumuda. Pano akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi kuti: “Ndaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti mwana wanuyu anali namwali.” Koma nawu umboni wa unamwali wa mwana wanga.’ Pamenepo azifunyulula chofunda pamaso pa akulu a mzinda. Ndiyeno akulu a mzindawo azigwira mwamunayo ndi kum’langa. Akatero azimulipiritsa masekeli 100 asiliva, ndipo azipereka ndalamazo kwa bambo a mtsikanayo chifukwa waipitsa mbiri ya namwali wa mu Isiraeli. Mtsikanayo apitirize kukhala mkazi wake ndipo sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake. “Koma zimenezi zikatsimikizika kuti ndi zoona, palibedi umboni wa unamwali wa mtsikanayo, azim’bweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna a mumzindawo azim’ponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli, mwa kuchita uhule m’nyumba ya bambo ake. Motero muzichotsa woipayo pakati panu. (Deuteronomo 22: 13-21)

Chiwerewere