Mbiri ya Umar bun Al-Khattwaab mwachidule

Alongosolereni ana anu achichepere nkhani zimenezi

Umar bun Al Khattaab radhia Allah anhu anali mmodzi mwa ma Khalifa amphamvu komanso opambana, ochokera m’banja la Bani ‘Adiy, fuko la Quraysh ku Makkah. Anali Khalifa wachiwiri pambuyo pa Abu Bakr radhia Allah anhu, yemwe anali swahaba wamkulu wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Tikabwelera mbuyo mumbiri ya Chisilamu ndikuona anthu omwe anagwira ntchito yotamandika pofalitsa Chisilamu, tipeza kuti Umar radhia Allah anhu anali mwa anthu odalirika pa ntchitoyi.

Pali zambiri zomwe tingaphunzire kuchokera mu mbiri ya Umar radhia Allah anhu monga mphamvu zake, kulowa Chisilamu, utsogoleri wake ndi zina.

Umar radhia Allah anhu anabadwira ku Makkah m’banja la Banu ‘Adiy, fuko la Quraysh mchaka cha 583. Iye anali businessman komanso sanali Msilamu pachiyambi. Asanalowe Chislamu, Umar anali mdani wamkulu wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Panthawi imeneyo kunali anthu ochepa omwe anali kudziwa kuwerenga ndi kulemba, koma Umar radhia Allah anhu anali mmodzi mwa anthu ophunzira; iye ankadziwa bwino za moyo wa munthu, science of genetics, komanso history ya dziko la Arabia.

Umar radhia Allah anhu anali olimba mtima, odziwa kumenyana, zokambirana za mitsutso, kuyankhula pagulu komanso maluso ena ndi ena.

Komatu ngakhale Umar radhia Allah anhu anali ndi mbiri zonsezo, tsoka ndiloti munthawi imeneyi sanavomere ulaliki wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Iye anali mdani wotentheka kwa Mtumiki moti anali kutsutsa kalikonse mu uthenga wa Chisilamu, ndipo kawirikawiri anali kuopseza kuti amupha Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Tsiku lina anawuyatsa ulendo kuti akaphe Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Koma ali mu ulendowo, anazindikira kuti mlongo wake pamodzi ndi mwamuna wake analowa Chisilamu. Pamenepo anapita kunyumba kwawo ndikuwapeza akuphunzitsidwa Qur’an ndi Kabbaab radhia Allah anhu.

Anawafunsa chifukwa chimene analowera Chisilam ndipo anamumenya mlongo wake mpaka kutuluka magazi. Ataona izi, anamva chisoni ndipo anapempha kuti amuonetse ma page a mu Qur’an. Umar anasamba ndikuyamba kuwerenga Qur’an ija mu Surat Taha, mpaka anafika pa mawu oti:

إِنَّنِي أَنَا اللَّهُ لَا إِلَهَ إِلَّا أَنَا فَاعْبُدْنِي وَأَقِمِ الصَّلَاةَ لِذِكْرِي

“Ndithu, ine ndine Mulungu palibe wopembedzedwa mwachowonadi koma ine, choncho ndipembedze, pemphera swalaat moyenera pondikumbukira” 14

Anakhunzidwa kwambiri ndi verse imeneyi ndipo anavomereza kuti ndi mau a Allah.

Kuchokera pamenepo, Umar anapitiriza ulendo wake wopita kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, koma tsopano nthawiyi sikunali kukamupha monga mmene anaganizira koyamba.

Mtumiki atamuona Umar, anamufunsa chomwe wabwelera ndipo anayankha kuti wabwera kudzalowa Chisilamu.

Pachiyambi, Asilamu anali ndi manthu pa kupemphera swalaat zawo moonekera chifukwa cha kuwopa atsogoleri a Quraysh. Koma mmene Umar analowa Chisilamu, anayamba kupemphera mowonekera poti Umar anali wamphamvu kotero kuti aliyense anali kumuwopa.

Iye ndi amene anapereka maganizo kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti apemphere mkati mwa Ka’ba, ndipo Mtumiki kwanthawi yoyamba anatsogolera Asilamu pa Swalaat.

Chifukwa cha maganizo ake olimba mtima, anapatsidwa title yoti Al Faarooq, kutanthauza kuti munthu yemwe amalekanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Chimodzi mwa zikhalidwe za Umar ndi choti anali ofulumira kukwiya ndi anthu omwe anali kuchita zosemphana ndi Chisilmu ndipo anali kumupempha Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti amulole athane nawo, koma Mtumiki anali kumudekhetsa mtima nthawi zonse, pomuuza kuti Iye anatumizidwa kudzachitira chifundo anthu osati kudzawachitira nkhanza.

Pakuntha kwa nathawi, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamwalira ndipo Umar radhia Allah anhu anakwiya ndikuwauza anthu kuti yemwe angalengeze kuti Mtumiki wamwalira, athana naye. Koma Abu Bakr radhia Allah anhu ananena chilungamo ndipo Umar anadekha.

Pambuyo pake, Asilamu anasemphana maganizo pa munthu yemwe angatsogolere Asilamu pambuyo pa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Umar radhia Allah anhu anawakumbutsa anthu za umunthu wa Abu Bakr radhia Allah anhu komanso mmene ubale wake ndi Mtumiki unaliri. Anthu anamvesetsa mfundo zake zija ndipo anamusankha kukhala mlowammalo oyamba mChislamu.

Mosakhalitsa, Abu Bakr radhia Allah anhu anamwalira ndipo Umar radhia Allah anhu analowa mmalo mwake. Iye anatsogolera potsatira njira ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo Chisilamu chinafalikira ku madera osiyasnasiyana kunja kwa Arabia. Maufumu a ku Iran, Persina Empire, Turkish (Byzantine Empire) anagwa mu utsogoleri wa Umar ndi Asilikali ake. Pakutha zaka 10, Chisilamu chinakwanira mmaiko a Iran, Syria, Palestine, Egypt ndi Madera ena.

Umar sanangokhala commander wa nkhondo chabe, koma analinso odziwa mayendetsedwe a boma, moti amadziwika kuti ndi founder wa Islamic political system. Analimbikitsa kuti maiko a Chisilamu adziyendera malamulo a Chisilamu. Anayambitsa gulu la Polisi. Analinso kupereka gawo la chuma kwa osauka. Anamanga mizinda ya Chisimau ndi likulu la Asilikali, komanso anakweza ntchito za ulimi ndi zachuma. Anayambitsanso ndondomeko ya maphunziro.

Umar radhia Allah anhu ndi role model wa Asilamu; iye anali olimbikitsa chilungamo, chisoni, chikondi ndi makhalidwe onse abwino.