بسم الله الرحمن الرحيم
Kugawa Chuma Chosiyidwa Malinga ndi Qur’an Yolemekezeka
Munthu akamwalira nkusiya chuma, Asilamu akuyemera kugawa chumacho moyenera ndi abale ake omwe wasiya omwalirayo.
Nzomvetsa chisoni masiku ano munthu ali ndi makolo ake, azibale ake, komanso anakwatira mpaka kukhala ndi ana…akangomwalira chuma anthu amachita chokanganirana; wina akufuna munda, wina grocery, wina machine osokera, wina njinga, wina akufuna angotengeraru mkazi….
Zomvetsa chisoni kuti Asilamu tikusungira constitution yathu yochokera kuseli kwa mitamble (Qur’an Yolemekezeka),  koma sitikuigwiritsa ntchito chonsecho timadzichemelera  kuti ndife Asilamu otsatira Qur’an ndi Sunnah.
Magawidwe a Chuma Chosiyidwa Malinga ndi Qur’an (Surah Al Nisaa 11-12) ali motere:
Mulungu akukulamulani za ana anu achimuna apate gawo lolingana ndi gawo la akazi awiri.
Ngati akaziwo ali (opitirira) awiri, ndiye kuti adzalandira zigawo ziwiri mwazigawo zitatu (⅔) za (chumacho) chimene wasiya (womwalira).
Ngati mwana wamkazi ndi mmodzi, apatsidwe chigawo chimodzi mwa zigawo ziwiri (½), naonso makolo ake awiri aliyense waiwo alandile chigawo chimodzi mwazigawo zisanu ndi chimodzi (1/6) chachuma chosiidwacho.
Ngati (womwalirayo) wasiya mwana (kapena mdzukulu). Koma ngati sadasiye mwana, ndipo makolo ake awiri ndiwo awasiira, ndiye kuti mayi wake alandire chigawo chimodzi mwazigawo zitatu (1/3) chachumacho, (ndipo bambo alandire (⅔).
Ngati wakufayo wasiya abale, ndiye kuti mayi wake apeza chigawo chimodzi mwazigawo zisanu ndi chimodzi (1/6) chachumacho. (Kugawa chumaku kuchitike) atachotsapo chimene iye adalamulira kuti adzachipereke kwakutikwakuti, kapena kulipira ngongole (zake).
Atate anu ndi ana anu, simudziwa inu kuti ndani mwaiwo amene ali ndi chithandizo chapafupi kwainu.
Amenewa ndi malamulo omwe akhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndithudi, Mulungu ngodziwa kwambiri, ngwanzeru zakuya.
Inunso mupata chigawo chimodzi mwazigawo ziwiri (½) chachuma chimene akazi anu asiya ngati alibe mwana (kapena mdzukulu) ngati asiya mwana ndiye kuti inu mupata chigawo chimodzi m’zigawo zinayi (¼) chachuma chosiidwacho mutachotsapo zomwe adalamula kuti zipite kwakutikwakuti kapena ngongole zake, naonso akazi anu apata chigawo chimodzi m’zingawo zinayi (¼) pachuma chomwe mwasiya, ngati mulibe mwana (ndi mdzukulu).
Koma ngati mwasiya mwana (ndi mdzukulu), (akaziwo) apata chigawo chimodzi m’zigawo zisanu ndi zitatu (1/8) pachuma chomwe mwasiya mutachotsapo chomwe mudanena kuti chipite kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole (zanu),
Ngati mwamuna kapena mkazi olowedwa m’malo pachuma pomwe alibe mwana (ndi mdzukulu) ngakhale makolo awiri, koma ali naye m’bale wake (wakuchikazi) kapena mlongo wake (wakuchikazinso), aliyense waiwo apata chigawo chimodzi m’zigawo zisanu ndi chimodzi (1/5). Ndipo ngati ali ochulukirapo, ndiye kuti agawirana chigawo chimodzi m’zigawo zitatu (1/3) cha chumacho pambuyo pochotsapo chomwe chidanenedwa kuti chipita kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole, popanda kupereka mavuto.
Awa ndi malamulo ofunika omwe achokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ngodziwa kwambiri (pokhazikitsa malamulo); woleza (pa akapolo ake).
Limenelitu ndi phunziro (subject) limene limataidwa ndi Msilamu osaliphunzira, koma ndizokakamizidwa kuto aliyense aphunzire magawidwe a chuma oterewa