Mwa zinthu zomwe zikusiyanitsa kwambiri pakati pa Qur’an ndi Baibulo ndi malamulo a mkazi pa chosiyidwa cha omwalira. Malinga ndi Baibulo, zafotokozedwa mosapsatira ndi Rabbi Epstein kuti: “Chikhalidwe chosasunthika komanso chamuyaya kuyambira pachiyambi cha Baibulo, sichinapereke kwa mkazi ndi ana achikazi ufulu wa ulowammalo pa katundu wosiyidwa m’banja. Akazi amaonedwa kuti ndi chimodzi mwa katundu wamnyumba, choncho ali otalikitsidwa kwambiri ndi kutenga katundu wosiyidwa. Ngakhale kuti mmalamulo a Mose ana aakazi adaloledwa ulowammalo ngati ana amuna kulibe, koma mkazi wamwamuna sanali kuloledwa.” 44 Kodi nchifukwa chiyani akazi ankatengedwa kuti ndi gawo la chuma? Rabbi Epstein anayankha motere: “Chifukwa choti iwowo ndi a abambo awo – asanakwatiwe, ndipo ndi a amuna awo – akakwatiwa.”

Malamulo a m’Baibulo pa  kulowammalo kwa mkazi alembedwa mu Numeri 27:1-11. Mkazi samapatsidwa gawo mu chuma cha mwamuna wake, ngakhale kuti iye ndi oyambilira oyenera kulandira asanalandire ana ake. Mwana wamkazi akhoza kutenga cholowa ngati palibe wamwamuna. Mayi si wolandira pamene bambo alipo. Amayi wosiyidwa ndi amuna awo komanso ana aakazi anali kuchitiridwa chifundo ngati ana aamuna atsala. Ichi ndi chifukwa chake akazi amasiye pamodzi ndi ana awo aakazi amakhala osauka kwambiri mu mtundu wa Chiyuda. Chikhristu chakhala Zimenezi chikutsatira kwanthawi yaitali; malamulo a zipembedzo ndi zikhalidwe cha matchalitchi a Chikhristu analetsa ana aakazi kuti asamayanjane ndi abale awo mu cholowa chawo. Kuphatikiza apo, akazi anali kulandidwa ufulu wa cholowa chirichonse, ndipo malamulo oipawa akhala akugwiritsidwa ntchito mpaka zaka zakumapeto kuno.

Nthawi ya ma Arabu achikunja (Shariah ya Chisilamu isanabwere), chimodzimodzinso ufulu wa cholowa unkaikidwa kwa abale achimuna okhaokha, koma Qur’an inathetsa miyambo yonseyi yomwe ndiyopanda chilungamo ndipo inapatsa amayi onse achibale ufulu pa cholowa chawo:

Qur’an 4:7: “Amuna mchuma chimene makolo ndi achibale asiya ali ndi gawo. Nawonso akazi ali ndigawo mchuma chimene asiya makolo ndi achibale (chapafupi), ngakhale chitakhala chochepa kapena chochuluka ndigawo logawidwa (ndi Mulungu).

Amayi a Chisilamu, akazi, ana achikazi ndi alongo adalandira ufulu wolandira gawo la zosiyidwa zaka1300 maiko aku Ulaya (Europe) asanazindikire kuti ufulu umenewu unalipo. Kugawidwa kwa cholowa ndi phunziro lalikulu lomwe liri ndi mfundo zambiri. Tawerengani Qur’an: (4:7, 4:11, 4:12, 4: 176).

Lamulo lake ndiloti gawo la mkazi ndi theka la gawo la mwamuna, kupatula pamene mayi alandira gawo lofanana ndi la bambo. Komatu mmaganiziridwe ena, lamulo limeneli ngati lingatengedwe palokha kuchoka mmalamulo ena okhudza abambo ndi amayi, mutha kuona ngati kuti palibe chilungamo. Pofuna kumvetsetsa zomwe zimachitika potsatira lamuloli, munthu ayenera kuganizira kuti udindo wa amuna pa ndalama Mchisilamu umaposa wa akazi (onani gawo la “Katundu cha Mkazi”).

Mkwati ayenera kupereka mphatso yaukwati kwa mkwatibwi. Mphatso imeneyi imakhala yake mkaziyo ndipo simabwezedwa ngakhale pambuyo pa kusudzulidwa. Mkwatibwi sanalamulidwe kupereka mphatso iriyonse kwa mwamuna wake. Ndi udindo wa mwamuna kusamalira mkazi ndi ana ake, ndipo mkazi sanalamulidwe kuti amuthandize mwamuna wake pa udindo wakewo, kotero kuti chuma chake komanso zopeza za paumoyo wake zimakhala zake iyeyo kupatula ngati wafuna kugawana kapena kuthandiza mwamuna wake kusamalira banja mongodzipereka.

Wina aliyense akuyenera kudziwa kuti Chisilamu chimalimbikitsa moyo wa m’banja; chimalimbikitsa achinyamata kuti akwatirane, chimadana ndi kusudzulana, ndipo kukhala osakwatira sichimakutenga kuti ndi ubwino. Kotero mu chikhalidwe cha Chisilamu, moyo wa pabanja ndi moyo wachilengedwe, komanso ndi chikhalidwe chake, pomwe kukhala wosakwatira ndi zosemphana ndi chikhalidwe cha Chisilamu. Nchifukwa chake pafupifupi akazi ndi amuna onse achikulire amakhala okwatira. Malingana ndi izi, munthu amvetsetsa kuti amuna a Chisilamu onse amakhala ndi mavuto aakulu pankhani zachuma kuposa akazi, nchifukwa chake kulowammalo pa chuma chosiyidwa kumakhala kosafanana pakati pawo, kuti pasakhale kulimbana.

Pambuyo pa kuyerekeza pakati pa maufulu a zachuma a mayi ndi maudindo ake, mmodzi mwa amayi a ku Britain adatsimikiza kuti Chisilamu sichinangosamalira amayi ake mwaulemu mokha, koma chinawasamaliranso mowolowa manja.

Mavuto a Akazi Amasiye