Anthu anaika freedom of choice pa kukwatira ndikukhala pa banja lovomerezeka, chifukwa chopangidwa influence ndi ma ideologies a ku west omwe adadza kudzalimbana ndi malamulo a Deen ya Chislamu, omwe amatsutsa kalikonse ponena kuti Chisilamu chimapondereza ufulu wa munthu.

Zimenezi zimapangitsa Asilamu omwe ali ofooka mu imaan ndi maphunziro akaganizira za kavuto kakang’ono mmabanja a anzawo, amangobwera ndi maganizo oti basi adzingokhala sadzakwatira mpaka kale. Ndiye kuli mabungwe ena omwe amalimbikitsa khalidwe limeneli powapatsa omwe sanakwatire njira zochitira zinaa, zomwe zimamutalikitsira munthu khumbo la kukhala pabanja poti amati zomwe angamadzipeze m’banjamo akudzipeza munjira ina, “ndipo banja ndi mavuto okhaokha bola ndizingoyendera yomweyi”.

Tidziwe kuti kukwatira ndi imodzi mwa ibaada mChisilamu. Kukwatira ndi lamulo la Chisilamu ndipo phindu lake likubwelera ku society komanso mbali yaikulu kwa okwatira, komanso pomakhala ibaada, Allah Ta’ala amasangalala nawo anthuwo.

Kodi ibaada ya kukwatira ikuchokera pati?

Kukwatira ndi Sunnah mmasunnah osayenera kuwasiya.Tikamati sunnah, imeneyo ndi njira ya Mtumiki yochitira zinthu yomwe timayenera kutsatira. Tsopano pali Sunnah zomwe Mtumiki anali kuchita nthawi zina, ndipo nthawi zina sankachita; zimenezo zimatchedwa ghair muakkada (zosasindikizidwa) zoti ukhonza kuchita kapena osachita ngati pali chokuletsa kutero, posakhala kunyozera chabe. Pali Sunnah zomwe Mtumiki sankazisiya mmoyo mwake, komanso anazilamula kuti tidzichita; zimenezo ndi muakkada (zosindikizidwa) zomwe sitikuyenera kudzisiya popanda chifukwa cheninechi chovomerezeka. Imodzi mwa sunnah mauakkada zimenezi ndiko kukwatira. Iyitu ndi sunnah ya Aneneri onse.

Tsiku lina pamene anthu atatu anadza kwa Mtumiki kudzafunsa za ibaada, anali kutchula mmodzimmodzi ibaada yomwe amalimbikira, ndipo mmodzi wa iwo anati: Ine ndimaswali usiku wonse sindimagona. Wina anati: ine ndimasala chaka chonse ndipo sindimasula. Wina anati: ine ndiye ndimapewa azimai moti sindidzakwatira mpaka kale.Pamenepo Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “inu amene mwanena zakutizakuti, ndithu ine Wallahi ndimawopa Allah kuposa inu, koma ndimasala ndipo ndimamasula, ndimaswali usiku ndipo ndimagona, komanso ndimakwatira azimai. Choncho yemwe angasankhe njira zina posakhala za inezi, sali mwa ine.”

Apa Mtumiki amatanthauza kuti kusiya kukwatira chifukwa chodziyandikitsa kwa Allah, ndizolakwika ndipo sichiphunzitso chake. Ndiye omwe amati ine sindidzakwatira koma ndizingozisunga, akuzinamiza; chifukwa 1. Akusemphana ndi sunnah ya Allah yomwe iye anapezeka kudzekera, 2. Chimenecho sichiphunzitso cha Mtumiki. Ndiye munthu akuti akudziyandikitsa kwa Allah pochita zomwe zili zosayenera ndi Allah, amulandira ndani? akudzitalikitsa ndithu.

mau oti “…sali mwa ine” sakumutulutsa munthu Chisilamu

Ma hadith olamula kukwatira alipo ambiri, koma tingoona kaye mbali zina, chifukwa ambiri akangomva kuti Mtumiki analamula zakuti, amayankhula kuti aaa imeneyo ndi sunnah, sunnah ngakhale osachita. Kuyankhula komanso kuganiza uku ndikolakwika komanso kunyoza malamulo a Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndikuwachepetsa. Omwe amadziwa kufunikira kwa Sunnah koma samakwanitsa kupanga, amadandaula kwambiri mmoyo mwawo, pomwe mbuli imasangalala ikamva ena akunena kuti “olo osachita supeza nsambi”.

Kodi kusiya ibaada yomwe analamula Mtumiki ndi tchimo?
Ndi tchimo kusiya ibaada yomwe analamula Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Chisilamu malamulo ake akuchokera mu Qur’an ndi Sunnah. Allah Ta’ala watilamula kambirimbiri kutsatira Mtumiki salla Allah alaih wasallam, monga:

وَمَا آتَاكُمُ الرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَاكُمْ عَنْهُ فَانتَهُوا وَاتَّقُوا اللَّهَ إِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ

“Ndipo chimene wakupatsani Mtumiki, chilandireni; ndipo chimene wakuletsani chisiyeni. Muopeni Mulungu (potsatira malamulo ake). Ndithu, Mulungu ngwaukali polanga”. Qur’an 59:7

Ili ndi lamulo la Allah, akutilamula kutsatira zomwe watilamula Mtumiki ndikusiya zomwe watiletsa. Ndipo tiwope chilango cha Allah potsatira lamulo lake loti tidzitenga zomwe Mtumiki watilamula. Kukwaira ndi Ibaada yolamulidwa.

Munthu asazisankhire kuti ine sindikwatira … kungofuna chabe. Ngakhale patapezeka zifukwa, athane ndi zifukwazo then akwatire. Osazisankhira zochita zina pambuyo poti walamulidwa zoti uchite:

وَمَا كَانَ لِمُؤْمِنٍ وَلَا مُؤْمِنَةٍ إِذَا قَضَى اللَّهُ وَرَسُولُهُ أَمْراً أَن يَكُونَ لَهُمُ الْخِيَرَةُ مِنْ أَمْرِهِمْ وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالاً مُّبِيناً

“Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Mulungu ndi Mtumiki wake akalamula chinthu, iwo kukhala ndi chifuniro pazinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Mulungu ndi Mtumiki wake, ndithu, wasokera; kusokera koonekera” Qur’an 33:36

Kuzisankhira zochita nkusiya zomwe tinalamulidwa ndiko kunyoza Allah ndi Mtumiki wake omwe anatilamula zoyenera kuchita. Asiyeni awo omwe amayendera maufulu awo odzikhonzerawo, azizisankhira zomwe akufuna poti mwina malamulo mchipembecho chawo amawalola kudzisankhira zochita. Koma inu musatengere, poti muli ndi Life Constitution yanu – ndi Qur’an yomwe inalongosoledwa nd Sunnah.

Werengani gawo lachitatu >>