Dowload PDF (direct link)

Listen/Download MP3

Munayamba mwaziwona nkhunda mazanamazana zitatera paphiri ndi mawonekedwe ake odziwika ndi aliyense, omwe amasonyeza mtendere, chikondi komanso mgwirizano?

Kumakkah, paphiri la Arafah mukhoza kukhala osangalatsidwa komanso odabwa powona chinamtindi cha anthu okapanga Hajj ochokera ku ngodya zonse za dziko lapansi omwe chiwelengero chawo chimapyola mamilioni awiri kapena kuposa pamenepa, onse atavala zovala zoyera zofanana za Ihram  zomwe zimawachita iwo kuti aziwoneka ngati nkhunda zomwe zasonkhana pamalo amodzi. Ngati mutawathira diso chapatali mukhoza kuganiza kuti ndi nkhunda zomwe zasonkhana pamalo amodzi. Ndipo ngati mutawayandikira kuti muwonetsetse mukhoza kuzindikira kuti iwo ndi anthu ochokera madera osiyanasiyana omwe afika mu mzinda wa Makkah womwe mkati mwake mukupezeka nyumba yolemekezeka ya Ka’bah ndi cholinga chofuna kukavomera kuyitana kwa Ibrahim alaih salaam, lamulo la Mbuye wawo pofuna kukwaniritsa ina mwa nsanamila zomwe zamanga chipembedzo cha chisilamu. Panthawiyi iwo amawoneka ngati nkhunda mazanamazana zomwe zatera patanthwe limodzi. Iwo amakhala atanyamula manja awo uku akumupempha ndi kumuyamika Mbuye wawo pamitendere yonse yomwe iye amawonetsera zolengedwa zake komanso uku akumupempha Iye kuti ayike mtendere, chikondi komanso mgwirizano pakati pawo.

Kumeneko, paphiri la Arafah pamakhala palibe opambana kuposa mzake munjira ina iliyonse. Izi zimakhala choncho posayang’ana kupambana kwa dziko lomwe iye akuchokera, zovala zomwe iye amavala angakhalenso pachilankhulo chomwe iye amalankhula. Siungathe kusiyanitsa pakati pa M’malawi ndi Msudani, Mtchayina ndi Mmwenye, mzungu ndi wakuda, olemera ndi osauka, ophunzira ndi osaphunzira, olamula ndi olamuliridwa; m’malo mwake onse amakhala akapolo onyozeka pamanso pa Allah Mbuye wa Zolengedwa zonse.

Ndizowonadi kuti siungasiyanitse pakati pa munthu ndi nzake. Onse amakhala pa moyo ofanana, Mayiko awo amasanduka dziko limodzi, chovala chawo chimakhala cha mtundu umodzi, Chilankhulo chawo chimakhala chimodzi. Kumeneko dziko lawo limakhala Chisilamu, Chovala chawo chimakhala Ihram, komanso chilankhulo chawo chimakhala Chiarab.

Onse amakhala akulankhula chilankhulo chimodzi povomera kuyitana kwa Mbuye wawo mokweza mawu uku akunena mawu awa:

Labbayka –Allahumma labbayka!

Ndavomera! Mbuye wanga ndavomera!

Wina aliyense amaganiza kuti ali pamaso pa Allah. Wina aliyense amaganiza kuti akamanena mawu amenewa akumulankhula Allah uku ali chiyimire pamalo pomwe panayima Mtumiki salla Allah alaih wasallam uku akupempha ngati m’mene Iye anapemphera komanso akupempha kwa Mbuye wawo ngati momwe iye adapemphera.

Anthu onse opanga Hajj panthawiyi, Wakuda ndi Oyera, Olemera ndi osauka amuna ndi akazi onse amakhala chimodzimodzi pamaso pa Allah.

Palibe chikayiko kuti chovala cha Ihram chomwe iwo amavala, ndi chovala cha chidziwitso cha mgwirizano. Iwo samavala chovala cha mtundu wina uliwonse kupatula Ihram, popanda chowonjezera chilichonse m’matupi mwawo ngati m’mene zimakhalira patsiku la kubadwa komanso patsiku lakufa.

Titangobadwa kumene, tidavekedwa chovala chimodzi, komanso tikadzamwalira tidzavekedwa chovala chimodzi. Tinabadwa amaliseche, ndipo chimodzimodzinso tidzamwalira tili amaliseche.

Choncho chovala cha Ihram ndi cha umaliseche wathu omwe umafunikira panthawi yomwe tili pamaso pa Allah. Uku ndiko kusiyana kwa kuwonekera kwa munthu pamanso pa Allah ndi pamanso pa mtsogoleri wa dziko.

Panthawi yomwe tikufuna kukawonana ndi mtsogoleri wa dziko, timawonetsetsa kuti tikhale a ukhondo komanso timayesetsa kuti tivale zovala zapamwamba. Koma panthawi yomwe tikuwonekera pamaso pa Allah, ife sikanthu, ndipo ichi ndichifukwa  chake zovala zapamwamba zili zosafunikira panthawi yokumana ndi Allah yemwe ndi Mbuye wa zolengedwa zonse.

Ichi ndi chifukwa chomwe Allah anamulamulira Mneneri wake Musa alaih salaam kuti avule nsapato zake panthawi yomwe iye anayandikira patanthwe loyera komwe iye amayembekezera kuti akumane ndi Mulengi komanso Mwini chilamulo. Nkhani imeneyi ikupezeka m’bukhu lolemekezeka la Qur’an motere:

“Ndipo kodi yakufika nkhani ya Musa (Yomwe ndi yododometsa)?. Adawuza banja lake yembekezani (pano); ndawona moto, mwina ndingakakutengereni chikuni chamoto (kuti muothe), kapena ndikapeza ondiongolera njira pamotopo. Koma pamene adaudzera motowo, Adayitanidwa (kuti) E! Iwe Musa!. Ndithu ine ndine Mbuye wako. Vula nsapato zako; ndithudi iwe uli pachigwa chopatulika, chotchedwa Tuwa. Ndipo ine ndakusankha kuti ukhale Mtumiki. Choncho mvera zonse zomwe zikubvumbulutsidwa kwa iwe. Ndithu Ine ndine Mulungu palibe wopembedzedwa mwachowonadi koma Ine, choncho ndipembeze, pemphera swala mondikumbukira. Ndithu nthawi ya tsiku lachiweruzo idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuyibisa dala kwa anthu kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita. (20:9-15)

Paphiri la Arafah, pamasonkhana anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso amitundu yosiyanasiyana, amawonekedwe osiyanasiyana komanso a zilankhulo zosiyanasiyana kuyambira masana mpakana madzulo. Iwo amakhala akulankhula ndi Allah popanda mkhala-pakati aliyense, pamtetete popanda choyala kapena denga kupatula mpweya omwe iwo amawupeza kuchokera kumbali zonse.

Panthawi yomwe iwo ali paphiri la Arafah, amapatsana moni wina ndi nzake komanso amadziwitsana wina ndi nzake, kupanga ubale wina ndi nzake komanso kuphunzira kuchokera kwa wina ndi nzake. Umenewu umakhala msonkhano waukulu komanso opambana womwe amasonkhana anthu amiyambo komanso maudindo osiyanasiyana komanso womwe pamakhala kugawana nzeru pakati pa wina ndi nzake omwe gwero lake limakhala kuvomera kwa anthu pa kuyitana kwa Allah yemwe ndi Mbuye wa zolengedwa zonse. Izi zimatsimikiza ndi kuchitira umboni mawu a Allah omwe tikuwapeza m’bukhu lake lolemekezeka motere:

“E inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mamuna m’modzi (Adam) ndi mkazi m’modzi (Hawa) ndipo tidakupangani kukhal a mitundi ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti mdziwane basi. Ndithu olemekezeka kwambiri mwa inu kwa Mulungu, ndi yemwe ali owopa. Ndithu Mulungu Ngodziwa ndipo Ngodziwa kwambiri nkhani zonse” (49:13)

Panthawi yomwe iwo asonkhana pa phiri la Arafah, mkwiyo umasandulika chikondi, kusiyana kumasandulika mgwirizano, amene amkapanga zoipa amasintha ndikuyamba kupanga zabwino, omwe amkakhulupilira zamabodza amasintha ndikuyamba kusankha zowona zokhazokha, anthu oyipa amasintha kukhala abwino komanso tsankho limasandulika chilungamo.

Kuphatikiza pa zonsezi, machimo onse am’mbuyo omwe munthu anatsogoza amakhala atakhululukidwa ndipo amakhala ndi tsogolo labwino chifukwa choti amakhala opanda tchimo lina lililonse. Malingana ndi Hadith’ yomwe inalandiridwa ndi Jabir’ alaih salaam, Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti:

“Likafika tsiku la Arafah, Allah amawatsitsa angelo ake pamtambo otsiriza ndipo amawayamikira onse opanga Hajj pamanso pa Angelo motere: ‘Tawonani akapolo anga amene adza kwa ine monyozeka, komanso otuwa omwe akulira kuchokera m’matanthwe onse. Ndikufuna kuti muchitire umboni kuti ndawakhululukira’. Kenako angelo amanena kuti: ‘O Mbuye wathu! Wakuti ndi wauti amakayikiridwa chimodzimodzinso azimayi akuti ndi akuti’. Iye amati Allah yemwe ndi wapamwamba komanso otamandika wayankha kuti: ‘Ndawakhululukira iwo’. Mtumiki wa Allah anati: ‘Palibe tsiku lomwe anthu amatulutsidwa kumoto ngati la Arafah”.

Muyenera kukumbukira kuti Hajar yemwe ndi mayi ake a Ismail ndi yemwe anayimilira azimayi onse pa m’bado uliwonse. Mwana wake anagwidwa ndi ludzu. Ndipo atawona kuti panalibe madzi, anaganiza zokafunafuna madziwo. Iye anati: “Mwina ndingakawapeze pa phiri la Safaa kapena paphiri la Marwah kapena patanthwe lapakati pa mapiri awiriwa. Iye anachita izi poyenda pamapiri awiriwa mobwerezabwereza koma sanawapeze madzi. Iye anayesetsa mwa iye yekha munjira ina iliyonse. Pachifukwachi iye analidi mayi odziwa udindo wake, kapena mukulankhula kwina tinganene kuti anali opambana kuposera mayi.

Chikondi cha mayi chomwe iye anali nacho ndi chomwe chinamupatsa iye mphamvu zoti ayende pamapiri awiriwa mobwerezabwereza ndicholinga chofunafuna madzi othetsera ludzu la mwana wake ndipo iye nali ndi chikhulupiliro chonse kuti zingavute maka kwina kwake kuyenera kupezeka madzi. Mneneri Ibrahim yemwe ndi Mamuna wake anawasiya iwo muchisamaliro cha Allah. Ndipo Ibrahim anali ndi chikhulupiliro chonse kuti Allah awasamalira ndi kuwayang’anira iwo ndipo sizingatheke kuti awanyalanyaze ndi kuwasiya akuvutika.

Hajar atabwelera pomwe panali mwana wake pambuyo pakutopa ndi kuvutika kamba kofunafuna madzi, anali odabwa kwambiri powona kasupe wamadzi yemwe anabuka pansi pa mapazi a mwana wake ndipo iye anati monthunthwa: “Ndithudi madzi akutuluka pansi pa mapazi a mwana wanga. O Allah! M’dalitseni Ismail, Inu ndipo gwero la chipambano ndi chisangalalo. Mulungu akudalitse iwe Ibrahim, ndithudi unali kunena zowona”.

Wina aliyense amene amakapanga Hajj kapena Umrah , amuna kaya akazi, anyamata kapena asungwana amakhala akumukumbukira mayi olemekezeka yemwe sanataye chikhulupiliro kuti zingavute maka, madzi ayenera kupezeka kwinakwake ngangale anayenda pakati pa mapiri a Safaa ndi Marwah kasanu ndi kawiri (7).

Kuyenda kwa ndawala komwe Hajar anakuchita ndi chitsanzo chabwino kwa ife cha mavuto omwe amapezeka pamoyo. Ngati m’mene anavutikira Hajar, ndimomwenso ayenera kuchitira aliyense tsiku lina lirilonse, ndithudi umu ndi m’mene moyo umakhalira. Panthawi yomwe ife tili pamavuto, tiyenera kuyesetsa kupeza njira yothetsera vutolo, ndipo ngati titalephera ngati momwe analephelera Hajar, tiyenera kudziwa kuti Allah amakhala tcheru nthawi zonse pofuna kumva kugogoda ndi kulira kwa akapolo ake. Ndipo chisoni ndi chifundo chake chimakhala chikutidikilira ife nthawi zonse. Tamvani m’mene Allah akulankhulira m’bukhu lake lolemekezeka la Qur’an:

“Ndipo ngati Mulungu atakukhudza ndi masautso, Palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni”. (10:107)

Kuwupsyopsyona Mwala Wakuda

Ina mwa miyambo yomwe imachitika panthawi ya Hajj ndiko kuwupsyopsyona mwala wakuda panthawi yozungulira nyumba yolemekezeka ya Ka’bah. Ndikofunikira kwambiri kuti tikambepo zokhudzana ndi mwambo opsyopsyona mwala wakuda pofuna kuwongolera kusamvetsa kwa anthu ena pamwambo umenewu makamaka alembi akumayiko aku wulaya omwe ndi adani a chipembedzo cha chisilamu.

Alembi amenewa amanena kuti ulemu omwe umaperekedwa ku nyumba ya Ka’bah komanso mwala wakuda ndi miyambo ya Ma Arab omwe anali kumuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina komanso omwe amkapembedza mafano. Mbiri pa iyo yokha ikutsutsa mowonekera mfundo imeneyi ndipo ikutifotokozera kuti Ma Arab anthawi imeneyo sanali kuyipembedza Ka’bah kapena mwala wakuda omwe anthu opanga Hajj amayenera kuwupsyopsyona ngati atapeza danga panthawi yomwe akuzungulira nyumba ya Ka’bah. Komanso tiyenera kudziwa kuti nyumba ya Ka’bah siyinali mgulu la mafano omwe Ma arab amenewa anali kuwapembedza. Mwala wakuda umenewu uli ngati chikumbutso kapena chizindikiro cha mwala wamaziko omwe iye anayika panthawi yomwe iye anali kumanga nyumba ya Ka’bah. Anthu opanga Hajj samagwadira nyumba ya Ka’bah kapena mwala wakuda koma amamugwadira Allah, Mbuye wa Ka’bah ndi mwala wakuda.

Komanso ina mwa miyambo yomwe imachitika panthawi ya Hajj ndiko kugenda miyala ing’onoing’ono pa zipilala za chikumbutso za Aqaba. Kugenda komwe kumachitikaku kumakhala kukumbukira kugendedwa kwa Satana komwe kunali kuchitika ndi Ibrahim panthawi yomwe anakafuna kumunyenga kuti alephere mayeso a Mbuye wake panthawi yomwe iye analamulidwa kuti amupereke nsembe mwana wake Ismail. Komanso kumayimira kulonjeza ndi kutsimikiza kwa munthu opanga Hajjiyo kuti sadzatsatira mapazi komanso njira zosokonekera za satana, kapena kupanga ubale ndi anthu ochita zoipa kapenanso kumvera zinthu zomwe zingamuwongolere ku njira ya satana.

Tiyenera kudziwa kuti miyambo yonse yomwe imachitika panthawi ya Hajj zimathandiza kulimbikitsa chikondi komanso mgwirizano pakati pa anthu kwina kulikonse komwe angakhale. Panthawi yomwe iwo akupanga hajj, onse amakhala ofanana ndipo pamakhala palibe opambana kuposa nzake. Sipamakhala kusiya kwina kulikonse pakati pa osauka ndi olemera, oyera ndi wakuda, ophunzira ndi osaphunzira, mtsogoleri ndi otsogoleredwa. Kusiyana kwawo konse kumatha panthawi ndipo onse amakhala ofanana ndi onyozeka pamanso pa Mbuye wawo.

Mathero

Pomaliza kufotokoza zokhudzana ndi Hajj, ndikufuna kuwakumbutsa onse amene amakapanga Hajj kuti m’mene akudziwira kuti mankhwala ozunguza bongo komanso mchititidwe uliwonse onyansa uli oletsedwa m’malamulo a chipembedzo cha Chisilamu; yeneranso kudziwa kuti kuphwanya malamulo onse omwe anakhazikitsidwa ndi dziko la Saudi Arabia kapena bungwe lina lilionse ndikoletsedwa mchipembedio cha chisilamu.

Chifukwa choti Hajj ndiko kunyamuka kupita kwa Allah ndi Mtumiki wake, ndipo anthu onse okapanga Hajj ayenera kuwonetsetsa kuti chimenechi ndi chomwe chiyenera kukhala chitsimikizo chawo. Iwo ayenera kudziyeretsa ku machimo onse komanso ku zilakolako za dziko lapansi ndicholinga choti pamapeto pa Hajj yawo ayenera kubwelera kwawo ali opanda tchimo lina lililonse ngati ana omwe angobadwa kumene.

Malingana ndi Hadith’ yomwe inalandiridwa ndi Umar Ibn el-Khattab, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

“China chilichonse chiyenera kuchitika malingana ndi chitsimikizo chake ndipo wina aliyense adzakhala ndi chomwe watsimikiza. Yemwe angasamuke kupita kwa Allah ndi Mtumiki wake, amasamukadi kupita kwa Allah ndi Mtumiki wake. Ndipo amene angasamuke pofuna kupeza zamdziko kapena chifukwa cha mkazi amene akufna kumukwatira, Nsamuko wake umakhala pazomwe wasamukira”.

Chisilamu sichimaletsa kupanga zinthu zolorezedwa panthawi ya ulendo wa Hajj,  ngati zinthuzo zitachitika mosapyola malire pamalamulo a chipembedzo cha Chisilamu. Chimidzomodzinso ngati zinthuzo sizikutsutsana ndi malamu a dziko kapena bungwe lomwe liri ndi udindo oyang’anira zinthuzo.

Pomaliza penipeni ndikumupempha Allah kuti atipatse ife zonse zotiyenereza kuti tidzakwaniritse ina mwa nsichi zomwe zamanga chipembedzo cha chisilamu yomwe ndi Hajj. Komanso kuti awalipire ndikuwadalitsa onse omwe anakwaniritsa kale nsichi imeneyi. Komanso ndikumupempha Iye kuti akatiyike ife mgulu la akapolo ake omwe akalandire chisoni ndi mtendere wake tsiku la chiweruzo. Komanso ndikumupempha Iye kuti apereke zabwino zake zonse kwa Mtumiki wake Muhammad salla Allah alaih wasallam yemwe anatiphunzitsa ife chipembedzo chathu komanso yemwe anatiwongolera ife njira yowongoka. Komanso kuti awadalitse akubanja lake, Omutsatira ake ndi onse omwe anamuthandiza iye pofalitsa chipembedzo cha chisilamu kufikira tsiku la chiweruzo.  Ameen!!!

Bwelerani Mutu Woyamba