Funso

Pali mtsikana yemwe sakudwala kumwezi koma kumayambiliroko ankadwala. Panopa almost two years ikutha osadwala. Sanagonepo ndi munthu chibadwire. Ndiye ali ndi vuto lakumva kuwawa mmimba ndi msana, koma kuchipatala anauzidwa kuti  ngati akufuna kuti mmimba ndi nsana zisamawawe akhoza kukumana ndi mwamuna. Koma iye sakufuna kutero. Tayesa kumpasa mankhwala a Black Seed zimayesa kuleka kuwawa kwa mmimba koma  after a day zikumayambira. Ndiye I need your help kuti what’s is the way forward?

Wa ‘alaikum salaam warahmatullah wabarakaatuh.

Kutamandidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zooengedwa zonse, Mtendere ndi madalitso zipite kwa Mtumiki wake.

 
“…kuchipatala anamuuza kuti…akhonza kukumana ndi mwamuna koma iye sakufuna…”

Chisilamu sichifuna zimenezo ndipo ndi zomwe zikumchititsa sisteryo kuti asalole. Ma sha Allah. Ndipo asachite zimenezo.

Makhwala azimenezo amapezeka both kuchipatala ndi kuchikuda.Ma doctor omwe amangofikira kunena kuti akagone ndi mwamunawo, amatero chifukwa choti mtundu wa matendawo si specialization yawo.
Pali mavuto ena monga amenewo, akakhala mwa mzimai wapabanja, kugonana ndi mwamuna wake ndi zololedwa komanso sizimavuta kuchira. Ndipo vutolo likhonza kudza kuchokera ponena kuti amakumana ndi mwamuna wake m’banja. Tiyeerekeze kuti sanakhalire pamodzi ndi mwamuna wake kwa kanthawi …  nchifukwa chake treatment yake ikuyenera kukhala kugona ndi mwamuna wakeyo, ndipo pali njira zina zosakhala kugonanako zomwe angagwiritse ntchito mtsikana osakwatiwa. Koma asatenge njira ya wapabanja pomwe iyeyo sanayambe wagonapo ndi mwamuna.

A doctor sakuyenera kumusankhira mtsikana treatment imeneyo kukhala yoyambilira komanso yokhayo yomwe angatenge… awone mbali zina, palibe chifukwa chomulowetsera mu zinaa.

Allah anatsitsa nthenda iriyonse ndi mankhwala ake, sanangotsitsa nthenda yopanda mankhwala. Komanso sanaike mankhwala a nthenda inayake mu zinthu za haram.Allah analetsa kuyiwandikira zinaa chifukwa ndi njira yoipisitsa komanso ndi tchimo lalikilu … Kodi nanga kuchichita kungaopse bwanji?

Mtsikanayo apite kuchipatala ndipo akakumane ndi gynecologist (doctor wa matenda a azimai komanso zokhunza kubereka). Ngati kuchipatala kungavute, makhwala achikuda a halala amapezeka. 

Allah ndi amene anatsitsa matenda… Yemweyonso anatsitsa makhwala ake a halal. Sangaletse kuchiwandikira chiwerewere komanso kuchichita, nkudzabweretsa matenda oti makhwala ake akhale chiwerewerecho.

Sisteryo asayerekeze kuchita zimenezo chifukwa pali ziopsezo izi:- akhonza kutenga mimba- akhonza kutenga matenda- akhala kuti watsegula njira yochitira chiwerewere- mwazonsezo, machimo ochita chiwerewere agwera pa iye.
Akumane ndi gynecologist kapena makhwala a chikuda (omwe ndi a halal {zisamba/mitsitsi}).

Njira ziwirizi zikalephereka, ndiye kuti ziwanda … apeze Sheikh yemwe amadziwa Qur’an ndi ma aayaa oyenera pa ruqya malinga ndi vuto lakelo,  amupangire ruqya ndipo awone ngati zingapezeke zizindikiro zoti ndi matenda odza kamba ka ziwanda kapena ufiti.

Adzilimbikira ibaada (swalat+Qur’an kumvera ndi kuwerenga+ma adhkaar) adzitalikire za haraam zonse monga nyimbo komanso kukhala ndi antju okonda za haraam.

In shaa Allah, athandiza.