Ndizofunika Kwa Msilamu Aliyense Kudziwa Kusiyana Kwa Masjidul Aqsa Ndi Masjid Qubbat Assakharah.

Kuyambira kalekale kwambiri, Masjidul Aqsa ku Palestine yakhala ikukumana ndi zipsinjo zambiri kuchokera kwa adani a Chisilamu omwe safuna kuona Chisilamu chikufalikira padziko. Izi zakhala zikuchitika kudzera mundale za nkhwidzi zomwe Ayuda, ma Zion amachita pofuna kusokoneza anthu omwe sali ozindikira, kuti asadziwe mzikiti weni weni wa Masjdul Aqsa. Ndipo mmalo mwake awatangwanitse ndi Masjdul Qubbat Assakharah powaputsitsa kuti imeneyo ndi Masjidul Aqsa. Komatu lero, Alhamdulillah bodza likuyenera kuchoka ndipo choona chiwonekere poyera.

Kusiyana komwe kulipo pakati pa Mzikiti wolemekezeka wa Masjdul Aqsa ndi Masjdul Qubbat Assakharah ndikonena kuti Masjdul Aqsa uli ndi Dome ya black pamwamba pake, pomwe Masjdu Qubbatu Ssakhrah ili ndi Dome ya golide. Dome apa tikutanthauza chinthu cha round chija chomwe chimaikidwa a pamwamba pa mizikiti ina, monganso chomwe chimaoneka pa mzikiti wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ku Madina, cha mtundu wa green.

Tidziwe, komanso tikumbukire, kuti mzikiti wolemekezeka wa Masjidul Aqsa unali Qiblah yoyambilira; anthu anali kulunjika ku Masjidul Aqsa poswali, asanalamulidwe kuti azilunjika ku Masjidul Haraam ku Makkah.

Masjidul Aqsa ndiumodzi mwa mizikiti itatu yomwe tinalamulidwa kuchulukitsa ma ulendo athu opita kukayiwona (Masjidul Haraam, Masjidu Nnabawi ndi Masjidul Aqsa). Ndipo zikulongosoledwa mu Hadith ya Sahih yomwe ikupezeka mu Sahih Al-Nasaai #693, kuti amene anamanga Masjidul Aqsa ndi Sulayman alaih Ssalaam.

Zikulongosololedwanso kuti Mzikiti umenewu unalipo kuyambira kalekale Sulayman alaikh Ssalaam asanabadwe malingana ndi mmene Hadith ya Sahih ikulongosolera, ndipo kumanga komwe anamanga Sulayman kunali kungochita renovate, kudzutsa. Mwachidule Hadith yomwe ikupezeka mu Sahih Muslim #520 ndi Sahih Al-Bukhar #3366, ikunena kuti:

عن أبي ذر رضي الله عنه قال قلت يا رسول الله أي مسجد وضع في الأرض أولا ؟ قال المسجد الحرام، قال قلت ثم أي ؟ قال المسجد الأقصى، قلت كم كان بينهما ؟ قال أربعون سنة – ثم أينما أدركتك الصلاة بعد ،فصله فإن الفضل فيه.

Kuchokera kwa Abu Dhar radhia Allahu anhu, ananena kuti: ndinanena kwa Mtumiki (ﷺ) kuti: Oh! Mtumiki wa Allah, ndi Mzikiti wuti woyambilira kumangidwa pa dziko lapansi? Mtumiki (ﷺ) anayankha kuti: (Mzikiti woyamba pa dziko lapansi) ndi Masjdul Haraam, kenako ndinati: kenako ndi mzikiti uti? Anayankha Mtumiki (ﷺ) kuti: ndi Masjdul Aqsa, kenako ndinati panali kusiyana kwa zaka zingati pakati pa Mizikiti iwiriyo? Anati: panali kusiyana kwa zaka 40, choncho pena paliponse pomwe yakukwanira nthawi ya swalaat, uziswali ulemerero uli pamenepo.

MASJIDUL AQSA
Ya’qub alaih Ssalaam ndimunthu woyambilira kumanga Mzikiti wa Baytul Maqdas (Masjdul Aqsa).

Ndipo pamene Ibrahim ndi mwana wake Isma’il alaihima Ssalaam anachita renovate Masjidul Haram, panadutsa zaka 40 kenako Ya’aqoob alaih Ssalaam nkumanga Baytul Maqdas (Masjidul Aqsa). Kenako anaabwera Sulayman alaih Ssalaam nadzachitanso renovate. Sulaimana analamula Majin (Ziwanda) kuti zimangenso Mzikiti Wolemekezeka wa Masjidul Aqsa ndipo Majin anamanga potsatira chilamulo cha Sulaiman alaih Ssalaam.

Mzikiti umenewu ulipobe mpaka lero lino, chifukwa unamangidwa pansi pa nthaka. Munthawi ya u Khalifa wa Umar radhia Allah anhu pamene anapulumutsa dziko la Palestine kuti likhale paufulu, anawupanganso renovate Mzikitiwu ndipo anawumanga pamwamba pa mzikiti wakalewu. Pachipatapa chachikulu (main entrance) cha Mzikiti umene Umar radhia Allah anhu anamangawu, palinso khomo lolowera ku Mzikiti wakale, kupita pansi ndipo pali chikwangwani cholozera pansi pakhomo lolowera mumzikiti wakalewu chomwe chinalembedwa kuti:

مسجد الأقصى القديم

“Mzikiti wakale wa Aqsa”
Mtumiki (ﷺ) anayendetsedwa ulendo wa usiku kuchoka ku Masjdul Haraam kupita ku Masjdul Aqsa (Baytul Maqdas) mu ulendo wa Israa wal Mi’raaj womwe tikuwudziwa ambiri uja mumbiri ya Chisilamu, ndipo ulendowu unapitilira mpaka kumwamba kwa Allah Ta’ala kukatenga Swalaat. Mtumiki (ﷺ) anatsogolera mapemphero Atumiki onse alaihim Ssalaam mu Mzikiti wodalitsikawu. Nchifukwa chaketu amatchedwanso kuti Imaamul Mursaleen.
Allah (ﷻ) akunena kuti:

سُبْحَانَ الَّذِي أَسْرَى بِعَبْدِهِ لَيْلًا مِنَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ إِلَى الْمَسْجِدِ الْأَقْصَى الَّذِي بَارَكْنَا حَوْلَهُ لِنُرِيَهُ مِنْ آيَاتِنَا إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ

“Ulemerero ndiwa (Allah) (ﷻ) Yemwe adayendetsa kapolo Wake usiku (umodzi) kuchokera mu Mzikiti wopatulika (wa Makkah) kupita ku Mzikiti wakutali Masjdul Aqsa (wa Baitul- Muqaddas), womwe tidaudalitsa ndi kuzidalitsa zam’mphepete mwake; (tidampititsa kumeneko) kuti timsonyeze zina mwa zisonyezo zathu; ndithu, Iye (Allah) ndi wakumva, ndi wopenya (chilichonse)”. Surah Al Israai Aayah 1

MASJIDUL QUBBAT ASSAKHARAH
Mzikiti wa Qubbat Assakharah unamangidwa mchaka cha 72 Hijiriya ndi Abul Waleed Abdul Malik bin Marwan, yemwe anali anali mtsogoleri wa Asilamu wa number 5 mu ukhalifa wa nyengo ya Umawiya.

Abul Waleed Abdul Malik bin Marwan anabadwira mumzinda wa Madinah Nnabawie mudziko la Saudi Arabia, mchaka cha 26 Hijriah, chomwe chili chaka cha 646 CE, ndipo anatenga utsogoleri wa Aslam mu ukhalifa wa Umawiyya (Umayyed mu chaka cha 65 Hijriah chomwe chili chaka cha 684 CE. Anakhala mtsogoleri wa Asilamu kwa zaka zokwana 21, ndipo anamwalilira mu mzinda wa Damascus mudziko la Syria, mchaka cha 86 Hijriah, chomwe chili chaka cha 705 CE, zomwe zikutanthauza kuti anamwalira ali ndi zaka 60 zakubadwa.

Mchaka cha 72 Hijriah chomwe ndi chaka cha 691 CE ndi pomwe anamanga Mzikiti wa Qubbat Assakharah. Kale Mzikiti wa Masjdul Aqsa unkatchedwa “Al Haramul Qudsiyy Shareef” kutanthauza kuti Malo oyera olemekezeka amu Jerusalem, ndipo malo onse mpakana pomwe panamangidwa Mzikiti wa Qubbat Assakharah womwe anamanga Abul Waleed Abdul Malik bin Marwan amatchedwabe kuti ndi malo opatulika (oyera), pomwe lero malo omwe pali Mzikitiwu amatchedwa Al Masjidul Kabeer.
Izi zikupezeka muchitabu chotchedwa:

الموسوعة الفلسطينية Al-Mawsooatul Filstwiniyya – volume 4 page 203 –

Kuchokera mu chitabu chomwechi zikunenedwa kuti: Mzikiti wa Qubbat Assakharah unamangidwa pakati pa malo omwe pali Mzikiti wa Masjdul Aqsa chigawo cha Kummwera cha kummawa (South East) kwa Mzinda wa Jerusalem; ndimalo akulu komanso aatali omwe akuchokera kudera la ku mpoto kukafika ku Mwera, omwe kukula kwake ndi pafupifupi ma mita 480 kuchokera kumpoto kukafika kummwera, ndipo kuchokera kumvuma (East) kukafika kudzambwe (West) pali mtunda wokwana pafupifupi ma mita 300. Malo amenewa amatenga chigawo chokwana pafupifupi 1/5 ya Mzinda wa Jerusalem. Zikuchokera mu volume 3 page 23 ya chitabu chomwe chija.

Ichi ndichitabu chawino kwambiri makamaka kwa omwe akufuna kudziwa mbiri ya Palestine. Osati kumangoti zilizonse google, googlwe anapanga adani a Chisilamu omwewa omwe safuna kuti inu mudziwe zoona zenizeni za Masjidul Aqsa.

MZIKITI WOYERA WA AQSA
Kodi Mzikiti womwe Mtumiki ananena kuti ukaswali umapeza malipiro ochuluka si mzikiti womwe timawudziwa ndi chi qubba cha golide pamwamba uja?
Ayi ndithu. Mzikiti wa Qubba yagolide yonyezimira womwe mumawuona uja, dzina lake ndi Masjid Qubbat Assakharah, womwe chithunzi chake nchofalikira kwambiri pa media, komanso ngakhale pa internet mpakana Asilamu ambiri akachiwona chithunzi chimenechi, amaganiza kuti ndi Masjdul Aqsa pomwe si choncho. Imene ija ndi Qubbatu Ssakhrah osati Masjidul Aqsa.

Ichi ndi chifukwa chake ma ulamaa athu olemekezeka lero lino amati akafika mu Mzinda wa Jerusalem samalunjika kukaswali swalaat zawo pomwe pali chi qubbah chimenechi, pamzikiti wa Qubbat, ngakhale Umar bin Khattab radhia Allah anhu komanso ma Sahaba ngakhale ma Khulafa-ul Rashideen ena onse, sankaswali pomwe pali mzikiti wa Qubbatu Assakharah. Ndipo palibe amene ankalemekeza pa mwala pomwe panamangidwa Mzikiti umenewu wa Qubbat Assakharah, koma ndi mwambo wa Ayuda olemekeza mwalawo.

Muchingerezimalowa amatchedwa kuti Dome of the Rock (Qubbatu Ssakhrah).

DZIWANI KUTI NDALE ZA MA ISRAEL NDIZOFUNA KUSOKONEZA ANTHU PAKUZINDIKIRA ZENIZENI ZA PAKATI PA MZIKITI WA MASJIDUL AQSA NDI MZIKITI WA QUBBAT ASSAKHARAH
Nyumba zowulutsira mawu (media) za Israel zimachita dala pochiwonetsa chithunzi cha Qubbat Assakharah nthawi zonse pakakhala zochitikika zosiyanasiyana ponena kuti Mzikiti womwe akuwonetsawo ndi Mzikiti wolemekezeka wa Masjidul Aqsa. Izi cholinga chawo ndikusokoneza anthu kuti ayiwale mzikiti weniweni, kotero kuti akawona Mzikiti wa Qubbat Assakharah aziti umenewo ndi Mzikiti wa Masjidul Aqsa.

Kodi cholinga chawo ndi chani kwenikweni? Cholinga chawo nchoti generation yomwe ikudza isadzauzindikire Mzikiti wa Aqsa weniweni, koma mmalo mwake awuzindikire Mzikiti wa Qubbat Assakharah ndikuwuchita kukhala woyera mmalo mwa Masjidul Aqsa. Pambuyo poti generation yaphimbidwa mmaso ndipo sikuwona kulemekezeka kulikonse kwa Masjidul Aqsa, kenako adzaigumula ndikumangapo Synagogue of Solomon (Sulaiman). Eyetu, pambuyo podzafafaniza malo omwe anamangapo Sulaiman alaih Ssalaam, akufuna adzamangepo zawo nkumpachika Iye. Zonsezitu zikuchokera muzikhulupiliro zawo zomwe amakhulupirira kuti kumapeto kwa dziko payenera kudzamangidwa “Church of Solomon” tchalitchi cha Solomon, ndiye akuona kuti nthawi yake yakwana n’chifukwa chake akufuna kuchotsa chithunzithunzi cha Mzikiti weniweni wa Aqsa, kuti anthu asawudziwe, kotero kuti akamadzamanga Synagogue yawoyo pa malo pomwe pali Mzikiti wa Masjidul Aqsa, anthu asadzawone ngati ndi mtopola. Zofunika Asilamu tichenjere.

Koma zachisoni Asilamu ambiri tili pa umbuli pankhani imeneyi ndipo timathandizira kukwaniritsa zofuna za ma Zionists pofalitsa chithunzi chimenechi cha Qubbat Assakharah kuti ndiwo Mzikiti wa Masjdul Aqsa. Lero lino tapitani mnyumba ya Msilamu, mukachipeza chithunzi chimenechi chili pa khoma, mbali ina kuli Masjidul Haraam, pakatippa pali aayah ija ya mu Surat Al Israa yonena kuti Mtumiki anayendetsedwa kuchoka ku Makkah kupita ku Jerusalem, ndipo mzikiti wa Qubbatu Ssakhara (Dome of the Rock), koma sichoncho. Ndipo kuipitsitsa kwakukulu nkoti chithunzichi mukachipeza munzikiti, pafupi ndi Qibla, achipachika pamenepo Asilamu azichiwona akamaswali. Chotsani ndithu propaganda ya Ayuda imeneyo.

NewsPaper ya Orman net inachita post pa internet chithunzi cha Masjdul Qubbat Assakharah, ndipo ankafunsa anthu kuti atchule dzina la Mzikiti womwe uli pa chithunzicho. Anthu ambiri ankayankha kuti ndi Masjdul Aqsa! Zomvetsa chisoni kwambiri.

Nchifukwa chani izizi zikutikhudza Asilamu tonse?
Ndili ndi zifukwa zingapo:

Tsiku lina Secretary General wa chipani cha
حزب جبهة العمل الإسلامي “Islamic Operation Front Party”-
Anayankhula mawu ogwira mtima pa Newspaper ya Orman Net, ananena kuti: Ndiudindo wa maiko onse a Chisilamu padziko lonse lapansi, kulimbana ndi kuthana ndi ndale zonyasa za ma Zionistizi, osati kusiyira dziko limodzi lokha. Asilamu akuyenera azindikire kuti cholinga cha ma Zionists ndikugwetsa Mzikiti wa Masjdul Aqsa komanso kuchotsa kapena kuti kufufuta chithunzithunzi cha Masjdul Aqsa mmitu ya ummah wonse, pofunika kuchenjera. Chisilamu chilibe boundary, kugawidwa kwa maiko kusatiputsitse nkumangolekelera Asilamu anzathu akuvutika chifukwa choti ife ndi Amalawi iwo ndi ma Palistine.

Muft wa dziko la Palestine mu Mzinda wa Jerusalem munyumba yotulutsira ma Fatwa yotchedwa
الديار الفلسطينية Al- Diyaarul Filistieniyya –
analamula nyumba zowulutsira mawu komanso kanema ndi media zonse za mayiko a Chiluya komanso media za Chisilamu zonse padziko lapansi kuti ayambe kufalitsa chithunzi chathunthu cha Masjdul Aqsa. Ndipo anachenjeza kuwopsa kwa kupitirizabe kufalitsa chithunzi cha Qubbat Assakharah nkumanama kuti ndichithunzi cha Mzikiti Wolemekezeka wa Aqsa popanda kufalitsa chinthunzi chamtunthu cheni cheni cha Masjidul Aqsa, chifukwa kumeneko ndikusokoneza mitu makamaka ya achinyamata ambiri a ummah wa Chisilamu.

Newspaper ya New York Times yaku America inatulutsa map a mzinda wa Jerusalem. Koma pa mapupo anachotsapo Mzikiti wa Aqsa, ndipo pamalo pomwe pali Mzikitipo anayikapo Synagogue of Solomon (yomwe akuganiza zodzaimanga akadzakwanitsa kugumula Masjidul Aqsa yathuyi), ndipo anayikapo uthenga womwe Msilamu aliyense akuyensera kuchenjera nawo. Uthengawu unali motere:

لا وجودَ لإسرائيل بدونا لقدس، ولا وجودَ للقدس بدون الهيكل

Israel singapezeke popanda Jerusalem, ndipo Jerusalem singapezeke popanda Synagogue of Solomon.

Uku nkuwaphimba anthu mmaso, makamaka awo omwe samafuna kuwerenga Mbiri kuchokera mmabuku a Chisilamu, koma pa internet mma website a azungu basi. Koma munthu wanzeru apa, monga mmene ndanenera kuti Synagogue of Solomon kulibe pakalipano, ndipo uthengawo ukunenetsa kuti “Jerusalem (Qudsi) singapezeke popanda Synagogue ya Solomon”, Msilamu wanzeru adziwa kuti anthuwa akusewera phada ndi Asilamu.

Chifukwa Quds yomwe akuinena mu utnhengamo ndi Qubbatu Ssakhra ija yomwe anatiphimba mmaso kuti tiziona ngati ndi Masjidul Aqsa, choncho ife tidziona ngati akusapota Masjidul Aqa. Tikamaombera mmanja zimenezi, basi zidzapezeka kuti atiikirapo chi synagogue ife tomwe nkuyamba kuchilambira ndi chikhulupiliro choti Sulaiman ndiyemwe anamanga. Synagogue of Solomon kulibe!

Tamvani izi:
Newspaper ya New York Times inatsindika kuti ndithudi nthawi yoyamba kumanga church cha Solomon yayandikira, ndipo kuti zitheke zomanga Synagogue of Solomon Mzikiti wa Aqsa uyenera kugumulidwa.

Ma plan ogumula Mzikiti wa Aqsa anayikidwa kuchokera kalekale ndipo ena mwa ma plan awo ndiko kugwiritsa ntchito media pochotsa chithunzi chenicheni cha Masjdul Aqsa ndikumafalitsa chinthunzi cha Qubbat Assakharah, mkumati umenewo ndiye Mzikiti wa Aqsa, lomwe ndibodza. Koma zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri timakhulupilira bodza limeneli.
Izi zikutsindika zomwe Sheikhul Islam ibn Taymiyah rahimahu Allah ananena mu chitabu chawo chotchedwa الكبرى الرسائل مجموعة, volume 2 page 61. Ananena kuti:

فالمسجد الأقصى اسم لجميع المسجد الذي بناه سليمان عليه السلام، وقد صار بعض الناس يسمي الأقصى، المصلَّى الذي بناه عمر بن الخطاب في مقدم

.والصلاة في هذا المصلى الذي بناه عمر للمسلمين أفضل من الصلاة في سائر المسجد ، فإن عمر بن الخطاب لما فتح بيت المقدس وكان على الصخرة زبالة عظيمة لأن النصارى كانوا يقصدون إهانتها مقابلة لليهود الذين يصلون إليها ، فأمر عمر بإزالة النجاسة عنها ، وقال لكعب: أين ترى أن نبني مصلى للمسلمين ؟ فقال : خلف الصخرة ، فقال : يا ابن اليهودية ! خالطتك اليهودية ، بل أبنيه أمامها فإنّ لنا صدور المساجد

Tikanena kuti Masjdul Aqsa, timatanthauza Mzikiti wonse womwe anamanga Sulayman alaih Ssalaam, ndipo unayamba kudziwika pakati pa anthu ndi dzina loti Aqsa – Mzikiti womwe anamanga Umar bin Khattab radhia Allah anhu kutsogolo kwake. Kuchitira mapemphero mu Mzikiti umenewu ndikopambana kwambiri kuposa mu Mzikiti wina uliwonse (kuposanso ngakhale Masjid Qubbat Assakharah), chifukwa Umar bin Khattab radhia Allah anhu munthawi yomwe anachita liberate Palestine, anapeza kuti pamwala (pomwe panamangidwa mzikiti wa Qubbat Assakharah) Akhristu ankatayilapo zinyalala. Akhristu ankachita izi pochita chipongwe Ayuda omwe anali kulemekeza mwalawo powulambira (komaso kwina kunali kubisa malo omwe ali mzikiti weniweni wa Aqsa).

Choncho Umar bin Khattab radhia Allah anhu analamula zochotsa nyasizo pamalopo, kenako anamufunsa Ka’ab bin Ahbaar (yemwe anali Swahaabah wa Chiyuda komanso anali pachimbedzo cha Chiyuda poyambilira asanalowe Chisilamu ndipo anali wophunzira bwino Torah (Bible), moti Mtumiki (ﷺ) ankawatuma ma Swahaabah monga Abu Hurayrah kukaphunzira Torah kwa Ka’ab). Umar anamufunsa Ka’ab kuti ukuwona bwanji ndimalo ati omwe tiyenera kumanga Mzikiti wa Asilamu? Ka’ab anayankha kuti: timange kuseli kwa mwala (apa amatanthauza pomwe panamangidwa Mzikiti wa Qubbat Assakharah). Pamenepo, Umar bin Khattab radhia Allah anhu anamudzudzula kuti oh iwe mwana wa Chiyuda!! Chinakusokoneza mutu Chiyuda? kenako ananena kuti koma uyenera umangidwe kutsogolo kwa mwalawu chifukwa pali tsinde la Mizikiti (apa amatanthauza kuti amange pomwe anamanga Mzikiti Sulayman).

CHENJEZO LANGA LOMALIZA
Zomvetsa chisoni kwambiri ndizonena kuti ife Asilamu ambiri lero lino, tikawona chithunzi cha Qubbat Assakharah timakhutitsidwa kuti tawona Mzikiti wolemekezeka wa Aqsa, pomwe si choncho. Mwina pena timaputsitsika ndi mamangidwe okongola a Mzikitiwu, koma izi sizikupatulabe kuti ndizinthu zolakwika kwambiri kwa ife ngati Asilamu kulephera kuzindikira kusiyana kwa Masjdul Aqsa ndi Qubbat Assakharah…

Pofunika kusamala, chifukwa ichi chikhoza kukhala chiwembu ndi kaduka wa Ayuda chifukwa chakulemekeza kwawo mwala powulambira, kapena akupangira dala pofuna kukwaniritsa zolinga zawo zomanga Synagogue of Solomon ndikugwetsa Masjidul Aqsa, kuti Asilamu aziganiza kuti Qubbat Assakharah ndiye Masjidul Aqsa, kotero kuti ukagumulidwa Asilamu azidzati ayi Mzikiti wathu wolemekezeka wa Aqsa ulipobe sunagumulidwe. Iwo pamenepo adzakhala atakwaniritsa zolinga zawo
نسأل الله تعالى أن يعيد للمسلمين عزَّهم ومجدَهم ، وأن يطهر المسجد الأقصى من إخوان القردة والخنازير ، والله غالب على أمره ولكن أكثر الناس لا يعلمون…