Ine ndapanga machimo ambiri  ndipo ndikufuna kubwelera kwa Allah ndikupanga tawba, kulapa koona. Kodi ndingapange bwanji tawbah imeneyi 
Tawbah (Kulapa) ndi kokakamizidwa kwa Msilamu aliyense, ngakhaletu kwa makafiri. Munthu aliyense yem,we wafika msinkhu wolembedwa machimo, Msilamu ngakhale Mkafiri, akuyenera kumapanga tawbah kwa Allah Ta’la kuchokera ku shirk ndi kufr yakeyo ndipo alowe mChisilamu. Chifukwa Allah Ta’la akunena mu Qur’an Surah Al Dhaariyaat aayah 56 kuti:
وَمَا خَلَقْتُ الْجِنَّ وَالإِنسَ إِلَّا لِيَعْبُدُونِ 
“Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza.”
Kuchokera mu kuyankhula kumeneku, makafir onse a muanthu ndi majinn (Akhristu ndi Ayuda ndi ena onse azikhulupiliro zosiyanasiyana za chikafir) alowe Chisilamu Chi,pembedzo cha Allah Ta’la ndikumachita chifuniro chake potsatira malamulo a Chisilamu. Ndipotu apange tawbah kwa Allah kuchokera  mmachimo awo ndi ntchito zonse zoipa. Allah Ta’la akunena mu Surah Al Tahrim aayah 8 kuti:
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا تُوبُوا إِلَى اللَّهِ تَوْبَةً نَصُوحًا
“E, inu amene mwakhulupirira! Lapani kwa Mulungu; kulapa koona”
Akunenanso mu Surah Al Noor aayah 31 kuti:
وَتُوبُوا إِلَى اللَّهِ جَمِيعًا أَيُّهَ الْمُؤْمِنُونَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ
“Tembenukirani kwa Mulungu, nonse inu okhulupirira kuti mupambane.”
Akunenanso mu Surah Al Anfaal aayah 38 kuti:
قُلْ لِلَّذِينَ كَفَرُوا إِنْ يَنْتَهُوا يُغْفَرْ لَهُمْ مَا قَدْ سَلَفَ وَإِنْ يَعُودُوا فَقَدْ مَضَتْ سُنَّتُ الْأَوَّلِينَ
“Nena kwa osakhulupirira kuti: “Ngati asiya (zochita zawo zoipa), adzakhululukidwa zimene zidatsogola. Koma ngati abwereza (kuwazunza Asilamu, tiwalanga) ndithudi njira ya Mulungu yomwe idachitika kwa anthu akale inadutsa (powalanga akasiya kutsata malamulo a Mulungu).”
 
Choncho ndizofunikira kwa aliyense kupanga tawbah (kulapa nkubwelera kwa Allah) chifukwa Iye ndi Yekhayo yemwe amayankha kulapa kwa akapolo ake, monga momwe akunenera mu Surah Al Shura aayah 25:
وَهُوَ الَّذِي يَقْبَلُ التَّوْبَةَ عَنْ عِبَادِهِ وَيَعْفُوا عَنِ السَّيِّئَاتِ وَيَعْلَمُ مَا تَفْعَلُونَ
“Ndipo Iye (yekha) ndi amene amavomereza kulapa kuchokera kwa akapolo ake. Ndipo amakhululuka machimo (awo); komanso akudziwa zimene mukuchita.”
 
Olapa aliyense ali okakamizidwa kubwelera kwa Allah ndikudzidandaulira pa machimo ake omwe anapanga mbuyomo, komanso kutsimikiza kuti sadzabweleranso ku zimenezo. Akatero Allah adzamukhululukira in sha Allah.
 
Kuti Tawbah itheke, zikufunikira zinthu zitatu izi:
Kudzidandaulira (kupanga regret) ku machimo ake omwe wachita; monga zinaa (chiwerewere), kumwa mowa, kunyoza makolo kapena anthu ena, kupanga katapira, kudya chuma cha masiye,ndi machimo ena onse omwe anachita mbuyo mwake. 
Atsimikize kuti sadzabwerezanso kuchita zimenezo. Akuyenera kukhala ndi chitsimikizo (niyyah) kuti ntchito zake zonse zidzikhala zokomera Allah Ta’la, akamagwira ntchito iliyonse kapena kuchita chirichonse, adzionesetsa kuti chisangalatsa Allah Ta’la Mmodzi yekha, ndipo akhala ochita tawbah kwa Iye yekha.
 
Kuti munthu akwanitse kudzitalikitsa ku machimo omwe wapanga tawbah, akuyenera kusankha anthu ocheza nawo; asankhe anthu abwino ndikudzitalikitsa ndi anthu oipa amene angamubwezeretsenso ku machimo aja. Iyi ndi njira yopambana yompangitsa munthu kupindula ndi tawbah komanso kupangitsa kuti tawbah yake ikhale yopambana ndiyokhanzikika komanso yokwanira.
 
Ngati ali ndi anzake omwe amagwirizana nawo pa tchimo linalake, asiyane nawo, komanso ngati ali ndi zina zake zimene zimampangitsa kukhala connected ku machimowo, adule connection imeneyo kuti pasakhale kuthekera kulikonse komuyandikitsa kumachimo aliwonsewo…monga kupanga delete ma video oipa omwe amaonera, kupanga delete nyimbo zonse mu phone mwake ndikulowetsamo Qur’an ndi ma ulaliki, ngati ali oimba, aotche zida zonse zomwe amagwiritsa ntchito powakokera anthu omvera ku machimo omvera nyimbozo komanso podzikokera iye mwini ku machimo a kufalitsa zoipa padziko ndi zina zotero. Kupanga zimenezo kupangitsa kuti tawbah ikhale yopambana ndipo sadzabwelera ku machimowo.
Allah amafuta zochimwa za munthu kuzera mu Tawba التوبة يمحو الله بها الذنوب, machimo onse omwe munthu unachita mbuyomu Allah amawafafaniza kuzera mu tawbah imeneyo.
 
Ngati wachita machimo ochuluka, usataye mtima kapena kudandaula pa machimo ako kuti basi sudzakhululukidwa, chifukwa Allah Ta’la akunena mu Qur’an Surah Al Zumar aayah 53 kuti:
قُلْ يَا عِبَادِيَ الَّذِينَ أَسْرَفُوا عَلَى أَنفُسِهِمْ لَا تَقْنَطُوا مِن رَّحْمَةِ اللَّهِ إِنَّ اللَّهَ يَغْفِرُ الذُّنُوبَ جَمِيعاً إِنَّهُ هُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ
“Nena (kwa iwo mau anga akuti): “E, inu akapolo anga amene mwadzichitira chinyengo, musataye mtima ndi chifundo cha Mulungu. Ndithu, Mulungu amakhululuka machimo onse. Ndithu, Iye ngokhululuka kwambiri”
 
Aayah imeneyi ndi uthenga womwe ukupita kwa onse ochita tawbah, akutiletsa kutaya mtima monga mmene akunenera kuti لا تقنطوا musataye mtima pa Mulungu; okhulupilira samayenera kutaya mtima kapena kudandaula chifukwa cha machimo awo, koma akangozindikira kuti achimwa, amathamangira kupanga tawba ndipo amakhala ndi maganizo abwino okhaokha pa Allah Ta’la. Mtumiki salla Allah alaih wasallam akunena kuti:
التائب من الذنب كمن لا ذنب له
“Opanga tawbah ali ngati yemwe ali opanda tchimo”
Ukalapa ku tchimo ndikudzidandaulira komanso kudzitalikitsa ku zoyambitsa machimo ndikutsimikiza kuti sudzabweleranso ku ntchito zomwe zakuchititsa machimowo, ndithu Allah Ta’la amakufafanizira machimo ako onse, ngati wachita zonsezi chifukwa cha Allah Ta’la.
Tsopano ngati wachita mosakhala mwa Allah Ta’la, koma wasiya ntchito za machimo zija komanso watsimikiza kuti sudzayambiranso, koma zonsezo d\sunachitire Allah Ta’la, koma wachita chifukwa cha kuopa kuti zinaku vulazapo kapena powopera kuti zidzapereka mavuto kwa abale ako ukamadzichita, pamenepo usadziwelengere kuti wachita tawbah. Imeneyo si tawbatun nasooha imene Allah wainena kuti tichite tawbatan nasooha, tawbah yeniyeni. Ndipo machimo ako amakhala kuti adakalipobe mpaka kalekale pokhpokha udzapange tawbah. Tawbah imayenera kukhala yochitira Allah osati kudziopera iwe mwini kuti zomwe ukuchitazo zikupatsa mavuto.
Ukapanga tawbah sumayenera kubwerezanso tchimolo chifukwa unalumbira kuti sudzabwerezanso, ndipo unadzitalikitsa ku zifukwa zomwe zingakupangitse kugwera mu tchimolo. Koma ngati ungachitenso tchimolo, dziwa kuti wabweretsa tchimo latsopano lomwe ukuyenera kupanga tawbah ina.
 
Kupanga Tawbha ku Machimo Ochuluka
Panali munthu kuchokera mu anthu omwe analipo kale yemwe anapha anthu okwana 99, ndipo anafunsa zamunthu ozindikira kudera lomwe anali kukhalalo. Anthu anamulondoleraa kwa m’busa wina, ndipo atapita anamuuza m’busa kuti “ine ndapha anthu okwana 99 kodi zingatheke kulapa ndikukhululukidwa?” M’busa anayankha nati “ayi, palibe kulapa kwa iwe”. Munthu uja anakwiya namuphanso m’busa uja ndipo anakwanitsa anthu 100.
Anafunsaso za munthu ozindikira malamulo a Mulungu, ndipo anamuuza kuti “ine ndapha anthu 100 kodi ndingalape nkulandiridwa Tawbah yanga?” ‘Aalim ameneyo anamuuza kuti “inde palibe choletsa kuti Tawbah yako ilandiridwa” Ndipo anamuuza kuti apite dera lakuti lakuti, kumeneko akapeza anthu omwe amagwadira ndikupembeza Allah ndipo akapembedze nawo limodzi Allah. Ananyamuka, atafika pakati pa ulendo wake inampeza imfa ndipo anamwalira munsewu asanakafike kokalapa kuja.
Angelo a Chifundo ndi Angelo a Chilango anayamba kukangana; aliyense anafuna kutenga munthu, ndipo Angelo a Chifundo anati: “anabwera kwa Allah kuzalapa ndipo Allah walandira kulapa kwake” Angelo a Chilango anati “palibe ndi ntchito yabwino yomwe wagwira ndipo sangakhululukidwe chifukwa koma amafuna akalapeko sanakafike” Pamenepo Allah anatumiza Mngelo wina yemwe anabwera mmaonekedwe a munthu; anabwera kudzaweruza pakati pawo. Iye anati “yezani kutuchuluka kwa mtunda womwe wayenda kuchokera kudera lomwe wachitira uchimo ndi dera lomwe akupita kukalapa komwe; kuli mtunda wautaliko ndiye kuti munthu apite kumeneko, ngati mtunda womwe watsala uli wochepa kuti akafike dera lomwe akupita kukalapa, ndiye kuti omwe atenge munthuyu ndi Angelo a Chifundo, ndipo ngati mtunda wayenda ndi wochepa kuchokera kudera lake la uchimo, ndiye kuti atengedwa ndi Angelo a Chilango.
Atayeza mtunda anapeza kuti anatsala pang’ono kuti akafike ku dera lomwe amafuna kuti akalape, ndipo Angelo a Chifundo anapambana natenga munthu uja.
Iyi ndi Hadith #22 mu buku la Riyadh Swaliheen pa khomo la Tawbah.
Mu hadith imeneyi tikuphunziramo zinthu zambiri zochepa chabe zomwe tikuphunzimo ndi izi:
1) Machimo angachuluke bwanji, Allah amakhululuka ngati wapanga tawba chifukwa ngati ukupanga tawbah ndiye kuti maganizo ako asiyana ndi zintchito zoipa zija tsopano uli chifupi ndi khomo la zintchito zabwino.
2) Osawopa kulapa kwa Allah kamba kakuwona kuchuluka kwa machimo kapena kuliwona tchimo kukula. Dziwa kuti Allah ndi Wachifundo ndipo amakhululuka.
3) Tidziweso kuti makomo a Tawba akadali otsegula mpakana kufikira tsiku lomwe dzuwa lidzatulukire kumadzulo.
4) Ntchito yathu yomwe tikugwira yabwino siyokwanira kukatilowetsa ku jannah. Munthu yemwe akutchulidwa mu Hadith imeneyi sanagwireko ntchito yabwino yoyenera kukalowa ku Jannah, koma kamba ka Chifundo cha Allah, analowetsedwa ku Jannah. Inunso ndi ine tikalowa ku jannah mu Chifundo cha Allah osati kamba ka ntchito zathu zabwino zomwe tikugwira. Komatu sizikutanthauza kuti tisamagwire ntchito zabwino. Ntchito zabwinozo ndi zomwe zimatichititsa kuti titalikirane ndi zoipa ndikuti Chifundo cha Allah chitipeze.
5) Tikuphunziranso kuchokera mu Hadith imeneyi kuyeretsa ma niyyah athu pa ntchito yathu yomwe tikugwira. Ikaonongeka niyyah ntchitonso imaonongeka, monga swalaat ukangoswali ndi cholinga choti akudziwe kuti umatha kuswali, basi waononga ngakhale uswali palibe chopeza kwa Allah. Kupereka swadaqah ndicholinga choti akudziweni kuti ndinu a chuma kapena owolowa manja, aponso mwalandiliratu zanu kuchokera kwa anthu. Kulalikira ndi cholinga choti mudziwike kwa anthu kuti nanu munashoma deen, munamwa chitabu, aponso mwadzionongera.
6) Hadith imeneyi ikutiphunzitsanso kuti tileke kuwaweruza anthu kamba ka ntchito zawo, chifukwa choti wina akupanga uchimo mkumuwona ngati basi nde waku moto, mumvekere muzafa ngati m’busa imfa yowawa, simukudziwa adzatha kulapa ndikukalowa ku Jannah kamba kachifundo cha Allah inu mukuziwona ngati ndinu olondolanu nkukakhala nkhuni zakumoto.
Izi ndizochepa chabe zomwe ine ndikuphuzira mu Hadith imeneyi. Nanga inu mwaphunziramo chani mu Hadith imeneyi? Aliyense anene monga mmene wamvera ndipo adziuze yekha, adzigwiritse ntchito mwa iye yekha
Tipemphe Allah .. tilape nthawi zonse in shaa Allah kulapa kwathu kudzalandiridwa