Taraweh ndi swalaat yausiku yomwe timaswali mmwezi wa Ramadhan, pokwaniritsa Sunnah ya Mtumiki salla Allah laaih wasallam yomwe sanali kuisiya. Ndipo swalaat imeneyi imatheka kuswalidwa pa jamaah kapena pawekha kunyumba, monganso mmene Mtumiki anali kuchitira.

Kuchokera mu Hadith ya Aisha radhia Allah anha, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalitsa anthu munsikiti usiku woyamba, kenako anaswalitsa usiku wotsatira ndipo anthu anachuluka, kenako anasonkhana usiku wachitatu kapena wachinayi ndipo Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanatuluke kudzawaswalitsa usiku umenewu. Mmene kunacha, ananena kuti: “ndaona zomwe mwachita, palibe chomwe chinandilepheretsa kutuluka kudzakuswalitsani kupatula kuti ndaopera kuti (swalaat imeneyi) ingakhale yokakamizidwa (faradh) kwainu” mmenemo munali mu Ramadhan.

Apa zikutipatsa chitsimikizo choti palibe vuto kuswalira munsikiti ngakhale kunyumba, ngati tili ndi chifukwa chomveka chotilepheretsa kupoita kunsikiti.

CHIWERENGO CHA MA RAKAAT A TARAWEH
Pamutu umenewu ndafuna kutambasula makamaka pamene kusemphana kwa ma imam kumachokera, kuti azipezeka ena kauswlaitsa ma rakaat 13, ena 23. Izi zili choncho malinganso ndi kusiyana kwa ma ulamaa akuluakulu omwenso aliyense mwaiwo anali ndi maumboni pa mawu awo, kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Ibn Qudaamah ananena mu buku lake la Al Mughni kuti:
Zomwe zinasankhidwa ndi Abu Abdullah ndi zoti Tarweh ndi marakaat 20, komanso zomwezi anayankhula Atthawri, Abu Hanifa ndi Shafi, pomwe Malik anati Taraweh ili ndi ma rakaat 36
Imaam Al Nawawi ananena mu buku lake la Al Majmu’ kuti:
‘Iyaadh anatenga report kuchokera kwa ma Ulamaa ochuluka kuti ndimarakaat 20, ndipo Al ‘Ainiy anati ma rakaat 11. Izi ndi ndizomwe anadzisankhira Malik ndi Abu Bakr Ibn Al ‘Arabi
Al Tirmidhi anati:

Zomwe zinakambidwa kwambiri ndizoti Taraweh ndimarakaat 41, rakaat imodzi ya witr.

Chiwerengero cha ma rakaat a swalat ya Tarweh ndi 11, malinga ndi Hadith ya Aisha radhia Allah anha pamene anafunsidwa zamomwe swalaat ya Mtumiki inali kukhalira. Iye anati:

ما كان يزيد في رمضان ولا في غيره على احد

ى عشر ركعة

Sanali kuwonjezera mu Ramadhan ngakhale myezi ina yonse kupitilira ma rakaat 11.

Ngati munthu akuswali ma rakaat 13, palibe vuto, malinga ndi kuyankhula kwa Ibn Abbas radhia Allah anhuma:

كانت صلاة النبي صلى الله عليه وسلم ثلاث ,عشر ركعة

Swalat ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam ankaswali ma rakaat 13

Aapa akutanthauza swalaat yausiku. Sahih Al Bukhari
Ma rakaat 11 ndiomwe ali otsimikizika kuti anali kuswali Mtumiki, kuchokera kwa Umar radhia Allah anhu, monga mmene zikukambidwira mu Al Muwatta’ ya Imaam Malik.

Koma tsopano ngakhale zili choncho, ngati ena angaonjezere pamwamba pa ma rakaat 11 omwe anali kuswali Mtumiki, palibe chovuta. Izi zikutsimikizika kuchokera mmawu a Mtumiki salla Allah alaih wasallam:

صلاة الليل مثنى مثنى

Swalat yausiku ndimarakaat awiriawiri.

Ndipo sanaike malire poyankhula kuwauza anthu. Komabe, ngati tingafune kusankha paziwirizi, tisankhe ndizomwe anali kuchita Iye mwini – ma rakaat 11 kapena 13 – poti ndizomwe tili nazo umboni poyera kuti anali kuchita.
Tilibe umboni uliwonse woona, wonena kuti Mtumiki kapena ma Khulafaa Raashidoon (Abu Bakr, Umar, Uthman ndi Ali) radhia Allah anhum, anaswalipo ma rakaat 23. Koma zomwe zikuchokera kwa Khalifa Umar ndizoti anali kuswali ma rakaat 11, pamene anamulamula Ubayy bun Ka’b ndi Tamima Addaari kuti aswalitse anthu marakat 11. Izi ndizomwe Umar radhia Allah anhu anazitenga kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Ndipo sindikudziwa ngati pali Swahaba wina yemwe anawonjezera pa ma rakaat 23.

Ndikufuna ndinenetse apa kuti kusemphana kwa anthu kumene kumachokera pa kusiyana maganizo pa chiwerengero cha ma rakaat a Tarweh, sikofunika kuti kukhale chifukwa cha kugawana pakati pa Asilamu a dera limodzi, moti mpaka ena kumanga msikiti wawo. Tidziwe kuti Mtumiki anali kuswali ma rakaat 11, ndipo ndiyemwe analamula kuti swalat yausiku iziswalidwa ma rakaat awiriawiri sanaike malire.

Choncho ma Sahaba ale anatengera pamenepo, namaonjezera kuchoka pa ma rakaat 11 kapena 13, mpaka 23. yamba kupemphera ma rakaat owonjezera kuchokera pa 13
Pali kusiyana kwanji pakati pa Taraweh, Qiyaamullayl ndi Tahajjud?

Swalaat ya usiku imatchedwa Tahajjud (kudzuka mtulo usiku ndikupemphera), monga mmene Allah akunenera:

ومن الليل فتهجد به نافلة لك

“Ndipo pakati pa usiku, dzuka m’tulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma.)” Al Muzzammil #79
Komanso Swalaat ya usiku imatchedwa Qiyaamullayl (kuimilira usiku ndikupemphera) monga mmene akunenera Allah Ta’la:

يا أيها المزمل قم الليل إلا قليلا

“Ee iwe amene wadzifunda! Imilira usiku (upemphere), kupatula nthawi yochepa” Al Muzzammil #2 Akunenanso kuti

كَانُوا قَلِيلًا مِنَ اللَّيْلِ مَا يَهْجَعُونَ

“Nthawi yausiku amagona pang’ono, (Amadzuka nachita mapemphero Mochulukitsa),” Al Dhaariyyaat #17

Tsopano Taraweh, ndidzina la swalaat lomwe ma Ulamaa anaitchula swalaat yausiku (Qiyaamullayl) yomwe imachitika kuyambira usiku woyamba mmwezi wa Ramadhan. Swalatiyi itha kutchedwanso Tahajjud, kapena Qiyaamullayl palibe vuto.
Shaykh Ibn Baz Majmoo’ vol.11/318