Hajj ndi Chiyani?

Dowload PDF (direct link)

Listen/Download MP3

Poyambilira ndikumuyamika Allah Subhaanah wa Ta’ala Mbuye wa zolengedwa zonse. Yemwe anayipanga Hajj kukhala imodzi mwa nsichi zomwe zamanga chipembedzo cha chisilamu yomwe mkati mwake Asilamu amaphunzira mgwirizano, chikondi komanso kukhalira limodzi wina ndi nzake. Madalitso ndi mtendere zipite kwa Mtumiki wathu Muhammad yemwe anatiwongolera ife ku njira yowongoka. Komanso madalitso ndi mtendere zipite kwa aku banja lake, ophunzira ake ndi onse omwe anamuthandiza iye kufalitsa chipembedzo cha chisilamu kufikira tsiku la chiweruzo.

Ndizachidziwikire kuti nsichi za chikukhulupiliro cha chipembedzo cha chisilamu zilipo zisanu zomwe ndi kukhulupilira mwa Allah, Angelo ake, mabuku ake, atumiki ake, komanso tsiku la chiweruzo. Kumugwadira Allah kumachitika kudzera mu zichitochito zosiyanasiyana monga kuyimika mapemphero, kupeleka chopeleka, kusala chakudya, komanso kukapanga mapemphero a Hajji ku Makkah. Chikhulupiliro ndiye tsinde la mchitidwe wina uliwonse womwe umasonyeza kumugwadira Allah komanso tsinde la zichitochito zonse mchipembedzo cha chisilamu.

Kutanthauza Kwa Hajj

Kupita ku Hajji ngati imodzi mwa nsanamila za chipembedzo cha chisilamu, ndi nchitidwe wakapembedzedwe wakale kwambiri omwe unkachitika pofuna kumugwadira ndi kumupembedza Mulungu. Hajj ndi liwu la chinenero cha chiluya lomwe limatanthauza kuchoka pamalo  ndikupita kumalo ena ndi cholinga chofuna kukachita chinthu china chake. Pamalamulo a chipembedzo cha chisilamu, Hajj imatanthauza kupita ku nyumba yolemekezeka ya Ka’bah ku Makkah ndi cholinga chofuna kukachita ndi kukakwaniritsa mapemphero a Hajj.

Chifukwa choti Hajj iri ndi miyambo yambiri yomwe imawoneka ngati ndiyovutirapo kwa anthu ambiri, ndinaganiza kuti chinali chinthu chofunikira kwambiri kuwafotokozera anthu zamiyamboyi ndicholinga choti azikhala odziwa. Ndizowonadi kuti Hajj iri ndi miyambo yambiri, Koma ine pankhaniyi ndafotokoza mwachidule ndi cholinga choti wina aliyense athe kumvetsetsa mosavuta. Choncho ngati zitapezeka kuti zinthu zina sidzinafotokozedwe, ndikupempha kuti tiyenera kubwelera ku mabukhu akuluakulu omwe anafotokoza mwatsatanetsatane zankhaniyi.

Nyumba ya Ka’bah

Tisanafotokoze za malamulo a Hajj, ndikofunikira kwambiri kwa Asilamu kudziwa angakhale mwachidule zokhudzana ndi mbiri ya nyumba ya Ka’bah yomwe malingana ndi m’mene ikutifotokozelera Qur’an yolemekezeka ndi malo omwe Asilamu amayang’anitsa nkhope zawo akamachita mapemphero awo yomwe pachinenero cha chiarab imatchedwa kuti Qibla komanso ndi malo omwe Asilamu amakachitirako miyambo yawo ya mapemphero a Hajj. Qur’an yolemekezeka ikutifotokozera mwatsatanetsatane motere:

“Choncho tikutembenuzira ku chibula chimene ukuchifuna: Tero titembenuzira nkhope yako yako kumbali yamsikiti woyera (Al-kaaba).  (2:144)’

Mukulankhula kwinanso Allah akulankhula motere M’bukhu Lake:

“Ndithudi nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu kuti azipempheramo ndi yomwe ili m’maka, yodalitsidwa ndiponso ndi chiongolo kwa anthu onse. M’menemo muli zizindikiro zowonekera zozindikiritsa kupatulika kwake ndi ukale wake, ndi pamalo pomwe Ibrahim adali kuyimilira, ndipo omwe akulowamo amakhala mchitetezo.  Ndithudi Mulungu walamula anthu kuti akachite Hajj mnyumbayo, amene angathe kukonza ulendo wonka kumeneko” (3:96-97) .

Mbiri ya nyumba yolemekezeka ya Ka’bah yomwe anthu amayikonzera ulendo ndi cholinga chofuna kukakwaniritsa mapemphero komanso miyambo ya Hajj, ikubwelera ku nthawi ya Mneneri Ibarahim mtendere ndi madalitso zikhale pa Iye ndi mwana wake Ismail. Mzinda wa makka omwe mkati mwake mukupezeka nyumba yolemekezeka ya Ka’bah ndi umodzi mwa mizinda yakalekale yodziwika kwambiri padziko lapansi, kuyambira kale mpakana lero. Mahadith’ a Mtumiki madalitso ndi mtendere zikhale pa iye amanena mwatchutchutchu kuti tsinde komanso gwero la nyumba imeneyi ndi Mneneri Ibarahim komanso mwana wake Ismail mtendere ukhale pa iwo.

Malingana ndi  Hadith’ ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, zikufotokozeredwa kuti Mneneri Ibrahim anamuyika mwana wake wamamuna Ismail pamodzi ndi mayi wake Hajar, pachigwa chomwe lerolino pakupezekapo mzinda wolemekezeka wa Makkah. Panthawyi nkuti dera limeneli linali kwalokha komanso lopanda zinthu zoliyenereza kuti anthu akhoza kulitenga ngati malo okhala. Iye anawasiyila iwo zina mwazipatso za tende ndi madzi pang’ono, kenako anamupempha Allah kuti akhale mtetezi komanso muyang’aniri wa iwo ndikutinso awapatse iwo zowanenereza pa moyo mdera lopanda chonde ngati limeneli.

Zimanenedwa kuti chifukwa chomwe chinamupangitsa iye kuti amutenge mwana wake Ismail pamodzi ndi mkazi wake Hajar ndi kukamuyika kudera limeneri, kunali kufuna kupewa mikangano yapabanja. Izi zinali choncho chifukwa choti mkazi wake wamkulu Sarah, anayamba kuwonetsa zizindikiro za nsanje pambuyo pa kubadwa kwa Ismail yemwe anali mwana wake oyamba kuchokera kwamkazi wake wachiwiri Hajar. Izi zinali chonchi chifukwa choti Sarah anakhala nthawi yayitali asanakhale ndi mwana, koma pamapeto pake muchifundo komanso chisomo cha Mulungu, iye anamubalira Ibrahim mwana wake wachiwiri yemwe ndi Ishaqa.

Ismail pamodzi ndi mayi wake anakhala modalira zipatso zatende komanso madzi omwe Ibrahim alaih salaam anawasiyira kwa masiku angapo, koma pamene madzi anawathera, Hajar anayamba kufunafuna madzi m’malo ozungulira derali. Iye anali kuchita izi pokwera komanso kutsika mapiri awiri odziwika bwino omwe ndi Safaa komanso Marwah. Iye atalephera kuwapeza madzi anabwelera komwe kunali mwana wake Ismail. Atabwelera, iye anali odabwa kwambiri powona kuti pansi pa mapazi a Ismail panayamba kutuluka kasupe wamadzi. Madzi amenewa amatuluka kuchokera ku kasupe amaneyu yemwe pamapeto pake anasandulika chitsime chosaphwa chomwe chimadziwika ndi dzina loti Zamzam.

Kenaka gulu la mtundu wa anthu otchedwa Jurhum lochokera cha kum’mwera lomwe linali paulendo opita ku Syria, linawapeza anthu awiriwa komanso madzi omwe anali nawo. Ndipo gulu limeneri litawona madzi omwe anapezeka pamalo pomwe panali Ismail ndi mayi ake Hajar, anaganiza zoti azikhalira limodzi ndi iwo. Malingana ndi m’mene Hadith’ ikufotokozera, izi zinali zotsatira za mapemphero omwe Ibrahim alaih salaam anawapemphera iwo kwa Mulungu.

Kenaka Ismail anakula mumtundu wa anthu a Jurhum ndipo anaphunzira chilankhulo chawo cha Chiarab komanso zikhalidwe ndi miyambo yawo, pamapeto pake iye anakwatira mwa iwo.

Nthawi zambiri, Ibarahim anali kupita kukamuyendera Ismail pamodzi ndi mayi ake Hajar. Mu ulendo wake wina okawayendera iwo, Ibrahim analota maloto omwe mkati mwake anali kulamulidwa kuti ayenera kumupeleka nsembe mwana wake Ismail. Pomwe maloto amenewa anali kupitilira, Ibrahim anatsimikiza kuti malotowa linali lamulo lowona lochokera kwa Allah. Kenaka iye anamutenga mwana wake Ismail yemwe panthawiyi anali mwana wamng’ono kupita naye kumalo apaokha. Iye anamufotokozera mwanawake kuti Iye anali kulamulidwa ndi Allah kuti amupeleke iye nsembe pofuna kumva maganizo ake. Ismail pokhala mwana waulemu komanso omvera, sanawiringule m’malo mwake anadzipereka pofuna kukwaniritsa lamulo la Allah pa iye. Ngakhale kuti Ibrahim anali ndi chikondi chonse pa mwana wake Ismail, anatsimikiza zomuzinga mwana wake ndicholinga chofuna kumupeleka nsembe. Kenaka kunabwera lamulo lochokera kwa Allah lomulamula iye kuti apeleke nsembe nkhosa kukhala ngati chiwombolo cha mwana wake. Qur’an yafotokoza za nkhani imeneyi mu Sura 37 kuyambira pa ndime 99 kukafika 113 motere:

“Ndipo Ibrahim adati: Ndithu ine ndikupita kwa mbuye wanga, Iye andiwongolera. O Ambuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale m’modzi wa olungama. Ndipo tidamuwuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa (Ismail). Ndipo (Adabadwa ndi kuyamba kukaula) pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake (pochitachita zamdziko Ibrahim adayesedwa mayeso kudzera m’maloto omwe iye adalota). Adati mwana wanga! Ine kutulo ndikuwona maloto owona ochokera kwa Mulungu omwe akundilamula kuti ndikuzinge monga nsembe yopeleka kwa Mulungu. Nanga ukuti bwanji? (Mwana wabwino adanena) Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamuridwa. Ngati Mulungu afuna, mundipeza ndiri m’modzi mwa opilira”.  Pamene adagonjera onse awiri chofuna cha Mulungu, ndipo Ibrahim adamgoneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha). Ndipo Tidamuyitana: E: Iwe Ibrahim! Ndithu wavomereza maloto (choncho usamuphe mwana wakoyo). Umo ndi momwe timawalipilira ochita zabwino. Ndithu amenewa ndi mayeso oonekera. Ndipo Tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apeleke nsembe). Ndipo Tidansiyira nkhani yabwino kwa anthu ena (omwe adadza pambuyo pake). Mtendere ukhale pa Ibrahim. M’menemo ndi momwe timawalipilira ochita zabwino. Ndithu Iye adali m’modzi mwa akapolo athu okhulupilira. Ndiponso tidamuwuza nkhani yabwin yoti akhala ndi mwana otchedwa Isihaqa; Mneneri wa mgulu la olungama. Ndipo tidamdalitsa iye ndi mwana wake Isihaqa. (37:99-113).

Nsembe imeneyi ndi chitsanzo chabwino cha chikhulupiliro chokhwima kwa anthu. Izi zikuwonetsa kuti Allah samamupondereza wina aliyense mwa anthu, koma kuti nthawi zina amawapatsa iwo mayesero ndi cholinga chofuna kuwayesa pa chikhulupiliro chawo. Ndipo amene amakhala ndi chikhulupiliro chenicheni mwa Mulungu, amakhala ndi chida cholandilira chifundo, chisoni, mtendere, chisangalalo komanso chiwongoko cha Allah.

Maulendo obwerezabwereza omwe Hajar, mayi wa Ismail anayenda pakati pa mapiri a Saffa ndi Marwah pomwe iye ankafunafuna madzi a mwana wake, komanso nsembe ya Ismail yomwe inawomboledwa ndi nkhosa, zinasanduka imodzi mwa miyambo ya mapemphero a Hajj yomwe anthu ochita Hajj amapanga.

Ibrahim anali osangalala kwambiri powona kuti mwana wake Ismail anakhazikika ku Makkah. Tsiku lina iye anamuwuza mwana wake kuti iye walamulidwa kuti amange nyumba komwe anthu okhulupilira adzikapangira mapemphero awo pofuna kudziyandikitsa ndi chisangalalo cha Allah. Ismail anawathandiza bambo ake kumanga nyumba ya ngodya zinayi, yomwe imadziwika lero lino ndi dzina loti Ka’bah. Qur’an yolemekezeka ikufotokoza zankhaniyi motere:

“Ndipo kumbukiranso pomwe Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Mulungu): O Mbuye wathu! Tilandireni ntchito yathuyi. Ndithudi inu ndinu wakumva Wodziwa”. (2:127)

Kenaka Ibrahim alaih salaam anamupempha Allah kuti awupange mzinda wa Makkah kukhala otetezedwa komaso opambana, ndikutinso anthu ochokera madera onse adziko lapansi adzakhale akupita ku Makkah kukachita mapemphero awo odziyeretsa wokha kwa Allah pa nyumba ya Ka’bah. Qur’an yolemekezeka ikufotokoza motere:

“Ndipo kumbukani pamene Ibrahim adanena: “Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu wa Makkah kukhala wa mtendere, ndipo ndipatuleni ine ndi ana anga kumchitidwe opembedza mafano. Mbuye wanga! Ndithu mafano awa asokeretsa anthu ambiri, choncho amene wanditsata, ndithudi iyeyo ali mwa ine (mudzamulipira chabwino monga mwandilonjeza), Ndipo amene wandinyoza (Mutha kumukhululukira), Ndithu inu ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni. Mbuye wanga!  ndithu Ine ndaikhazika ina mwa nyumba yanga (mwana wanga Ismail) pachigwa ichi cha Makkah chopanda zomera panyumba yanu yopatulika (Al-Ka’bah), Mbuye wathu aloleni kuti akhale opemphera swala, choncho ichiteni mitima ya anthu kukhala yopendekera kwa iwo (akonde kudzakhala malo amenewo), ndipo apatseni zipatso kuti athokoze. (14:35-37). 

Hajj Ndi Mchitidwe Wakalekale